Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndingatani Wina Atandifunsira Kuti Tikagonane?

Ndingatani Wina Atandifunsira Kuti Tikagonane?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Ndingatani Wina Atandifunsira Kuti Tikagonane?

“Ana amafunsirana kuti angoona ngati angafike podzagonana ndi munthuyo ndiponso kuti ndi anthu angati amene angagonane nawo.”—Anatero Penny. *

“Anyamata sachita manyazi kukambirana nkhaniyi. Amadzitama kwa anzawo kuti ngakhale ali ndi chibwenzi, amathabe kugonana ndi atsikana ena ambirimbiri.”—Anatero Edward.

“Anthu amene ankandifunsira anali ankhakamira kwabasi. Sankamva ngakhale utawakana motani!”—Anatero Ida.

KU MADERA ena khalidweli amalitcha kuti kuthandizana. Pomwe m’madera ena limadziwika ndi maina enanso. Mwachitsanzo ku Japan, mtsikana wina dzina lake Akiko anati, khalidweli amalitcha kuti kunyamulana. Iye anatinso: “Pali mawu ena omwe amatanthauza kuti ‘mnzako wongogonana naye.’ Ndiye kuti munthuyo ndi mnzako woti muzingogonana basi.”

Inde, pali mayina osiyanasiyana, koma tanthauzo lake ndi limodzi basi, kugonana popanda chikondi kapena chibwenzi chilichonse. Achinyamata ena amachita kudzionetsera chifukwa chokhala ndi anzawo omwe amawatcha kuti “anzawo aphindu,” kutanthauza kuti angathe kugonana nawo popanda kuvutika n’kuchita nawo chibwenzi. Mtsikana wina anati: “Kukhala ndi mnzako wotere kumatanthauza kuti mukangogonana ndiye kuti basi mwathana. Iwe umalowera kwina mnzakoyo kwina.”

Poti ndinu Mkhristu, muyenera ‘kuthawa dama.’ * (1 Akorinto 6:18) Podziwa zimenezi, muyenera kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingakulowetseni m’mavuto. Komabe nthawi zina zinthuzi zimachita kukutsatirani zokha. Cindy anati: “Kusukulu, anyamata ambiri andifunsirapo kuti tikangogonana basi.” Zimenezi zingachitikenso ku ntchito. Margaret anati: “Abwana anga anandifunsira kuti tikagonane. Anandikakamira kwambiri moti ntchitoyo ndinangoisiya!”

Komano musadabwe ngati nthawi zina mtima wanu umachita dyokodyoko ndi zinthu zimenezi. Baibulo limati: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Izi n’zimene zinam’chitikira mtsikana wina dzina lake Lourdes. Iye anati: “Osanama ayi, mnyamata amene anandifunsirayo ankandidolola kwabasi. Zimenezi zinam’chitikiraponso Jane. Iye anafotokoza kuti: “Mnyamatayo anandiimitsa mutu kwambiri. Moti kum’kana kunali chinthu chovuta kwambiri chimene ndachitapo pa moyo wanga wonse.” Nayenso Edward, yemwe tam’tchulapo kale m’nkhani ino, akuvomereza kuti kudzisunga kumavuta. Iye anati: “Atsikana ambiri akhala akundinyengerera kuti ndikagonane nawo koma ndimakana ndipo ili ndilo vuto langa lalikulu kwambiri monga Mkhristu. N’zovuta kwambiri kunena kuti toto, ndakana!”

Ngati munakumanapo ndi zimene anakumana nazo Lourdes, Jane, ndiponso Edward ndipo munachita zinthu zoyenerera pamaso pa Yehova Mulungu, dziwani kuti tikukuyamikirani kuti munachita bwino kwambiri. Nkhani ya mtumwi Paulo ingakulimbitseni mtima chifukwa nayenso ankavutika kwambiri polimbana ndi maganizo olakwika.—Aroma 7:21-24.

Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene muyenera kuziganizira wina akakufunsirani kuti mukagonane?

Kodi Cholakwa N’chiyani Kugonana Musanakwatirane?

Baibulo limaletsa kugonana musanakwatirane. Chigololo ndi tchimo lalikulu zedi moti anthu ochita tchimo limeneli “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Chimene chingakuthandizeni mukamayesedwa kuchita zachiwerewere ndicho kuona tchimoli mmene Yehova amalionera. Kwanu kudzikhala kudzisunga basi.

“Sindikayikira ngakhale pang’ono kuti njira yabwino kwambiri ndiyo kumvera Yehova basi.”—Anatero Karen, wa ku Canada

“Munthu amataya zinthu zambiri zofunika akanyalanyaza malamulo a Yehova a makhalidwe abwino chifukwa chongofuna kusangalala kwa kanthawi kochepa chabe.”—Anatero Vivian, wa ku Mexico.

“Musaiwale kuti muli ndi makolo, ndiponso anzanu, komanso abale ndi alongo ambiri mumpingo wanu. Anthu onsewa mungathe kuwakhumudwitsa ngati mutalola kuchita zimenezi.”—Anatero Peter, wa ku Britain.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti cholandirika kwa Ambuye n’chiti.” (Aefeso 5:10) Mukamaona chigololo mmene Yehova amachionera, mungathe ‘kudana nazo zoipazi’ ngakhale zitakukopani chifukwa cha kupanda ungwiro kwanu.—Salmo 97:10.

Werengani malemba awa: Genesis 39:7-9. Taonani mmene Yosefe analimbira mtima n’kukana kuchita chigololo atayesedwa. Onaninso chimene chinam’thandiza kuti atero.

Nyadirani Zimene Mumakhulupirira

Sizachilendo kuona achinyamata akunena monyadira mfundo zimene amaona kuti n’zogwira kwa iwowo. Ngati ndinu Mkhristu, muli ndi mwayi wokometsa dzina la Mulungu posonyeza makhalidwe abwino. Musamachite manyazi kuti simungasinthe mfundo zanu zokana kugonana ndi munthu yemwe simunakwatirane naye.

“Anthu azidziwiratu kuti mumayendera mfundo za makhalidwe abwino.”—Anatero Allen, wa ku Germany.

“Musamachite manyazi ndi zimene mumakhulupirira.”—Anatero Esther, wa ku Nigeria.

“Anyamata sangaone kuti mukukanadi zenizeni ngati mutawauza kuti, ‘Makolo anga amandiletsa kuchita zibwenzi.’ Koma muziwauza kuti inuyo panokha simukuwafuna.”—Anatero Janet, wa ku South Africa.

“Anyamata a kusukulu kwathu ankandidziwa, ndipo ankadziwiratu kuti kulimbana n’kundifunsira ineyo n’kungodzivutitsa.”—Anatero Vicky, wa ku United States.

Kukana kuchita zinthu zosemphana ndi zimene mumakhulupirira n’chizindikiro chakuti mwayamba kuganiza monga Mkhristu wokhwima maganizo.—1 Akorinto 14:20.

Werengani lemba ili: Miyambo 27:11. Ganizirani mmene zochita zanu zingathandizire pa nkhani yaikulu kwambiri m’chilengedwe chonse, nkhani ya kuyeretsa dzina la Yehova.

Kanani Mwamphamvu

Kukana n’kofunika. Koma ena angaganize kuti mukungofuna kuvuta basi, koma pansi pamtima mukuwafuna ndithu.

“N’zotheka kuti mukakana, munthu amene akukufunsiraniyo angaonjeze moto pofuna kuonetsa kuti iyeyo ndi mwamunamuna.”—Anatero Lauren, wa ku Canada.

“Zochita zanu zonse ziyenera kuonetsa kuti simukufuna; kaya n’kavalidwe kanu, kalankhulidwe kanu ngakhalenso khalidwe lanu.”—Anatero Joy, wa ku Nigeria.

“Kanani kwamtuwagalu.”—Anatero Daniel, wa ku Australia.

“Osalola kuti anthu azikutolani. Mnyamata wina atayamba kundigwiragwira paphewa ndinamuuza kuti ‘Ndisiye ngati ukufuna zaulemu!’ ndipo ndinachokapo ndikuoneka woipidwa kwambiri.”—Anatero Ellen, wa ku Britain.

“Muzinena mosapsatira mawu kuti mwakana ndipo angoiwalako basi chifukwa choti zivute zitani simudzalola ayi. Imeneyitu si nthawi yolankhula mwamanyazi ayi!”—Anatero Jean, wa ku Scotland.

“Mnyamata wina ankangondivutitsa pondifunsa mafunso opusa ndiponso kundisereula. Koma kenaka ndinalimba mtima n’kumuuza mwamphamvu kuti asadzayerekezenso kuchita zimenezi. Apa m’pamene analekera kundivutitsa.—Anatero Juanita, wa ku Mexico.

“Muzimuuza mnyamatayo mosapsatira mawu kuti zivute zitani simungagonane naye. Musamalole kulandira mphatso kwa anyamata amene akungofuna kuti mufewe basi kuti mukagonane nawo. Anyamata otere angathe kudzakutembenukirani n’kunena kuti mugone nawo basi chifukwa choti mwawadyera zawo.”—Anatero Lara wa ku Britain.

Yehova angakuthandizeni ngati mukuonetsa kuti mwatsimikizadi kukana zolimba. Wamasalmo Davide ananena mawu otsatirawa kuchokera pa zimene anaona yekha pamoyo wake: “Kwa munthu wokhulupirika mumamuchitiranso zinthu mokhulupirika.”—Salmo 18:25, NW.

Werengani lemba ili: 2 Mbiri 16:9. Onani kuti Yehova n’ngokonzeka kuthandiza anthu amene mtima wawo uli wowongoka kwa iyeyo.

Muziona Patali

Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Kodi mungatsatire bwanji malangizo amenewo? Mungatero poona patali.

“Musamayerekeze n’komwe kukhala ndi anthu amene amakamba zinthu zotere.”—Anatero Naomi, wa ku Japan.

“Pewani zochitika ndiponso anthu amene angakugwetseni m’mavuto. Mwachitsanzo, ineyo ndikudziwapo anthu ena amene anachita zoipa chifukwa choti anali ataledzera.”—Anatero Isha, wa ku Brazil.

“Musamawapatse zinthu monga adiresi yanu kapena nambala yanu ya foni.”—Anatero Diana, wa ku Britain.

“Osamalola kukupatirana ndi aliyense wa m’kalasi mwanu popatsana moni.”—Anatero Esther, wa ku Nigeria.

“Muzivala modzilemekeza. Zovala zanu zisamakhale zocheukitsa anyamata.”—Anatero Heidi, wa ku Germany.

“Kukhala paubwenzi wabwino ndi makolo anu ndiponso kulankhula nawo za nkhaniyi kumathandiza kwambiri.”—Anatero Akiko, wa ku Japan.

Ganizirani bwino kalankhulidwe kanu, khalidwe lanu, anzanu, ndiponso malo amene mumakonda kupitako. Kenaka dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikupereka mpata woti ena andifunsire kuti akagone nane? Kapenanso kodi ndikuchita zinazake mosadziwa zimene zingachititse kuti winawake andifunsire kuti ndikagonane naye?’

Werengani malemba awa: Genesis 34:1, 2. Onani kuti mtsikana winawake dzina lake, Dina anaona tsoka chifukwa chopezeka pa malo olakwika.

Musaiwale kuti Yehova Mulungu saona kugonana koteroko ngati nkhani yamasewera, ndipo nanunso musaione ngati nkhani yamasewera. Baibulo limati: “Wadama kapena wopanda chiyero . . . sakalowa konse mu ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.” (Aefeso 5:5) Mukapanda kugonja pochita zoyenera, mungathe kukhala ndi chikumbumtima choyera ndiponso mungadzisungire ulemu wanu. Mtsikana wina dzina lake Carly anati: “Moti n’zoona ndithu kulola kuti winawake angopezerapo mwayi wogwiritsira ntchito thupi lanu kuti athetse chilakolako chake? Ayi ndithu, yesetsani kupitirizabe kuteteza ubwenzi wanu ndi Yehova womwe mwachita khama kwambiri kuti muusunge!”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Maina omwe ali m’nkhani ino tawasintha.

^ ndime 8 Kuchita chigololo kumatanthauza kuchita zinthu monga kugonana kwenikweni, kugonana m’kamwa, kumatako, kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kuseweretsa maliseche munthu wina, ndiponso kuchita zinthu zina zokhudzana ndi maliseche, zochitidwa ndi anthu amene sanakwatirane.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Chifukwa chopanda ungwiro nthawi zina, kugonana mophwanya malamulo a m’Baibulo kumaoneka ngati chinthu chokopa, koma kodi kuchita zimenezi n’kulakwa chifukwa chiyani?

▪ Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani ngati winawake atakufunsirani kuti mukagonane?

[Bokosi patsamba 27]

▪ Baibulo limati munthu wadama “amachimwira thupi lake la iye mwini.” (1 Akorinto 6:18) Kodi zimenezi n’zoona motani? Ganizirani njira zina ndipo muzindandalike pansipa.

․․․․․

Zokuthandizani: Kuti muthe kuyankha mafunso amene ali pamwambawa, onani Nsanja ya Olonda, ya June 15, 2006, tsamba 28, ndime 14, ndi Nsanja ya Olonda ya June 15, 2002, tsamba 21, ndime 17, komanso buku la Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 188. Zonsezi n’zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 29]

KALATA YOPITA KWA MAKOLO

“Kusukulu, mnyamata wina wa m’kalasi mwathu anandiuza kuti tipite kwina kwake tikathandizane. Zinanditengera kanthawi ndithu kuti ndizindikire zimene anali kutanthauza. Panthawiyi ndinali ndi zaka 11 basi.”—Anatero Leah.

Ana amayamba kuuzidwa za kugonana adakali aang’ono kwambiri. Kalekale Baibulo linaneneratu kuti: ‘Masiku otsiriza’ adzadziwika ndi “nthawi yovuta yoikika,” pamene anthu adzakhala “osadziletsa” ndiponso “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1, 3, 4) Khalidwe lofunsira munthu n’cholinga chongogonana naye basi, limene talifotokoza m’nkhaniyi, ndi limodzi mwa makhalidwe ambiri amene akusonyeza kuti ulosi umenewu n’ngoona.

Masiku ano, dziko n’losiyana zedi ndi mmene linalili m’nthawi yanu. Komabe, mavuto ake ena ndi ofanana. Choncho simuyenera kuthedwa nzeru ndi zinthu zoipa zimene ana anu amakumana nazo kulikonse. M’malo mwake, tsimikizani mtima kuwathandiza kuti achite zimene mtumwi Paulo anauza Akhristu zaka 2,000 zapitazo kuti: “Valani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu kuti muthe kuchirimika polimbana ndi machenjera a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) Zoona zake n’zakuti, Akhristu ambiri achinyamata akulimbikira kwambiri kuchita zabwino, ngakhale kuti pali anthu ambiri amene akuwalimbikitsa kuchita zoipa. Kodi inuyo mungawathandize bwanji ana anu kuti nawonso azichita zabwino?

Njira imodzi ndiyo kugwiritsa ntchito nkhani ino, kuti muyambe kukambirana nawo zimenezi. Mbali yonena kuti “werengani malembawa” ili ndi malemba abwino kwambiri ofunika kuti anawa awaganizire. Malemba ena akukamba za zitsanzo zomwe zinachitikadi, za anthu amene analimbikira kuchita zabwino ndipo anadalitsidwa, ndi enanso amene ananyalanyaza malamulo a Mulungu ndipo anakumana ndi zovuta chifukwa cha zochita zawozo. Mbali yonena kuti “werengani malembawa” ili ndi mfundo zimene zingathandize ana anu kuzindikira mwayi waukulu umene iwowo ndiponso inuyo mumakhala nawo mukamatsatira malamulo a Mulungu. Bwanji osakonza zowerenganso nkhaniyi limodzi ndi ana anu?

Nthawi zonse kumvera zimene Yehova amafuna kumatipindulitsa. (Yesaya 48:17, 18) Komano kuzinyalanyaza kumatigwetsa m’mavuto. Ofalitsa Galamukani! akukufunirani madalitso a Yehova pamene mukuyesetsa kukhomereza malamulo a Mulungu m’mitima mwa ana anu.—Deuteronomo 6:6, 7.

[Chithunzi patsamba 28]

Muzimuuza mnyamatayo mosapsatira mawu kuti zivute zitani simungagonane naye