Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nzeru Zam’chilengedwe”

“Nzeru Zam’chilengedwe”

“Nzeru Zam’chilengedwe”

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU JAPAN

MUTU umenewu anaugogomezera kwambiri ku Aichi, m’dziko la Japan, komwe kunachitikira chionetsero chotchedwa Expo 2005. Mayiko 121 anachita nawo chionetserochi. Anthu amene anabwera kuchionetseroku anawalimbikitsa kuti aziphunzirapo kanthu pa zinthu zam’chilengedwe ndi kuti “aziyesetsa ndi mtima wonse kupeza njira zolimbikitsa chitukuko koma popanda kuwononga zachilengedwe.” Chionetserochi chinachitikira pafupi ndi mzinda wa Nagoya, m’chigawo chapakati cha dziko la Japan, ndipo ankaonetsapo nkhalango, maiwe oweterapo nsomba, ndi maluwa osiyanasiyana. Kunali msewu wochititsa chidwi wodutsa pamwamba ndipo unali wautali makilomita oposa awiri ndi theka. Msewu woyenda anthu apansiwu anautcha dzina loti Msewu Wozungulira Dziko. Unali waukulu mamita pafupifupi 21, ndipo unali pamwamba pamalowa kuti anthu akamayenda azitha kuona patali zedi, koma sunkasokoneza kukongola kwa zinthu zachilengedwe zimene zinali pansi pake.

Kukhala Mbali ya Zachilengedwe

Gawo limene boma la Japan limaonetserapo zinthu zake linali m’chinyumba cha nsungwi cholukidwa ngati nyumba ya mbozi inayake yotchedwa kankhuni. Chinyumbachi anachipanga ndi nsungwi 23,000 ndipo chinaphimba nyumba imene inali m’kati mwake kuti isamawombedwe ndi dzuwa. Nsungwi zambiri pa chinyumbachi zinali zotalika pafupifupi mamita 7, ndipo chinyumbachi chinali chachitali mamita 19 kukwera m’mwamba, mamita 90 m’lifupi ndiponso mamita 70 kuchokera kumaso kufika kumbuyo, motero inali m’gulu la nyumba zazikulu kwambiri padziko lonse zopangidwa ndi nsungwi. M’chinyumbacho munali chipinda chozungulira chomwe khoma lake lonse ndi kudenga komwe, kumaoneka vidiyo. Ndiye anthu ankalowa m’chipindacho, chomwe chinali chachikulu pafupifupi mamita 13 m’mimba mwake, ndipo akatembenukira kulikonse m’chipindamo anali kuona mafilimu osiyanasiyana a zachilengedwe, omwe anali kuchititsa anthuwo kuona kuti nawonso ndi mbali ya zachilengedwe zambirimbiri m’dzikoli.

M’chinyumba cha boma la Malaysia ankasonyezamo zithunzi ndi mavidiyo a nkhalango zikuluzikulu za m’madera otentha a dziko lonse ndiponso miyala yokongola ya pansi pa nyanja yopangidwa ndi zamoyo zing’onozing’ono. M’chinyumba cha boma la Thailand munali zithunzi zoliritsa zosonyeza mafunde osakaza kwambiri, otchedwa tsunami amene anachitika pa December 26, 2004, ndipo zithunzizi zinakumbutsa anthu oziona kuti “munthu sangalamule chilengedwe.” Pogogomezera za vuto la kusoloka kwa zachilengedwe, mbali ya chionetsero ya boma la South Africa inali ndi chidole cha mtundu winawake wa nyama zangati mbidzi zomwe panopo zinasoloka. Nyamazi zinkapezeka kumwera kwa Africa mpaka m’zaka za m’ma 1800 pamene zinasoloka.

Pafupi ndi chinyumba chomwe anali kuonetserapo zinthu zokhudza mutu waukulu wa chionetserochi panali mtembo wa mtundu winawake wa njovu za m’mayiko ozizira zomwe panopo zinasoloka. Mtembowo ankauonetsera m’chifiriji chokhala ndi galasi ndipo unafukulidwa m’chipale chofewa, m’chaka cha 2002 ku Siberia m’dziko la Russia. Njovuyi anaipatsa dzina lakuti Yukagir potengera dzina la malo amene anaipezako. Njovuyo inali ndi minyanga iwiri yokhota yaikuluikulu, ndipo inali itaphinya maso ake pang’ono. Mutu wake unali udakali ndi chikopa ndiponso ubweya mwa apo ndi apo. Mtembo wa njovuyi unali wochititsa chidwi zedi ndipo unakumbutsa anthu kuti zamoyo zimatha kusoloka.

Kodi Zinthu Zidzakhala Bwino Kwambiri M’tsogolo?

Kodi anthu angalimbane bwanji ndi zinthu zomwe zingathe kudzawononga dziko lathuli, mwina poliipitsa m’njira zosiyanasiyana kapena polichititsa kuti litenthe kwambiri? Kuchionetseroku kunali chikhoma “chobiriwira” chotchedwa Phapo la Zomera, chomwe akuti chinali “chizindikiro cha chionetsero chonse cha Expo 2005.” Chikhomachi chinali chachikulu mamita 150 m’litali mwake ndipo chinali chachitali mamita 15. Chinali ndi zomera 200,000 za mitundu yokwana 200, komanso chinali ndi maluwa. Anatchulapo kuti mapapo amenewa, omwe angathe kuwasintha mwina ndi mwina malingana ndi nyengo ya pachaka, angagwire ntchito ngati “mapapo” a mzinda, komanso ngati zinthu zothandiza kusefa mpweya. Mapapowa angachite zimenezi pomapuma mpweya woipa n’kumatulutsa mpweya wabwino.

Pachionetserochi anasonyezaponso njira zakayendedwe monga mabasi amakono oyendera magetsi. Mabasiwa ankatenga anthu kuwapititsa malo osiyanasiyana koma sankatulutsa utsi uliwonse, ankangotulutsa madzi basi. Anthu okonda zinthu zamakono anasangalalanso kwambiri kuona sitima yoyamba yonyamula anthu ku Japan yomwe imayendera maginito amphamvu zedi. Sitimayi anaipatsa dzina loti Linimo ndipo inkayenda molenjekeka mamilimita pafupifupi 8 pamwamba pa njanji. Sitimayi inkayenda mwa myaa komanso popanda phokoso lililonse. Kuchionetseroku kunali matole a sitima oyendera batire, njinga zonyamula anthu ngati matakisii ndiponso mabasi omwe amatha kuyenda okha popanda dalaivala. Zinthu zamakono kwambirizi zinali kuyenda mofulumira pamzera, ndipo zinkakhala ziwiriziwiri kapena zitatuzitatu komanso zinkayendera gasi, chifukwa sawononga chilengedwe kwambiri pomuyerekezera ndi mafuta.

Tangoganizirani zitakhala zotheka kupanga magetsi kapena feteleza pogwiritsa ntchito zinyalala zomwe zimatha kuwolerana, monga zakudya zimene timataya. Izitu n’zimene ankachita pamalo enaake pachionetserochi pogwiritsira ntchito gasi. Zinyalalazo sankaziwotcha, m’malo mwake ankangozisiya kuti ziwolerane n’kuyamba kutulutsa gasi. Gasiyu ankamusefa n’kuchotsako gasi winawake yemwe ankakonzera mabatire otulutsa mphamvu zambiri zamagetsi. Zinthu zomwe zimatsala pa ntchito imeneyi zinali feleteza ndi madzi. Ndipotu zinyalala zonse zimene zinkatayidwa pachionetserochi zinkapita ku malo amenewa kuti akazigwiritse ntchito imeneyi, ndipo pachionetserochi nyumba zina zinkayendera magetsi amenewa.

Akatswiri okonza makina otsanzira zochita za anthu, afufuza zinthu zambiri zothandiza kuti makinawa azikhala osalemera ndipo kuti afike pomachita ntchito zotumikira anthu. Pofuna kusonyeza kupita patsogolo kwa luso lopanga makina oterewa, m’kati mwa chinyumba china chachionetsero, makina seveni oterewa anayenda kupita kutsogolo ndipo anakopa anthu kwambiri atayamba kuyimba nyimbo. Ena mwa makinawa ankaimba nyimbo ndi zida monga zitoliro ndipo “tizala” tawo tinali kutabwanya mwaluso mabatani osiyanasiyana pa zitolirozo ndipo makina amodzi anali kuwomba ng’oma. Munthu wina amene anaona zimenezi anati: “Makinawo amayenda mwa myaa ndiponso mosachita kuvutikira moti angathe kupusitsa munthu kuganiza kuti ndi anthu amene akungonamizira kuti ndi makina.”

Kunalinso zinthu zina ziwiri zamakono kwambiri; choyamba chinali mapulasitiki omwe amawolerana mosavuta n’kusanduka manyowa. Mapulasitikiwa n’ngopangidwa kuchokera ku chimanga ndiponso zinthu zina zotere. Chachiwiri chinali thovu laling’ono kwambiri moti silioneka ndi maso. Thovuli n’laling’ono zedi moti kukula kwa thovu limodzi lotere n’kofanana ndi kagawo ka tsitsi la munthu ngati mutaligawa magawo 250 m’mimba mwake. Mwachilengedwe, thovu laling’ono chonchi silikhalira kuphulika. Koma ofufuza ku Japan atulukira njira yopangira thovu laling’ono chonchi koma lokhalitsa, ndipo thovuli “limathandiza kuti nsomba ndiponso zamoyo zina m’nyanja zizitha kusintha mogwirizana ndi mmene zinthu zikusinthira m’madzimo.” Ndipotu n’zochititsa chidwi kuti m’dziwe lina la nsomba lomwe anaikamo thovu lotereli anatha kuwetamo mitundu inayake ya nsomba za m’nyanja zing’onozing’ono komanso nyanja zamchere. Ofufuza akufuna kuti apeze njira zogwiritsira ntchito luso lamakonoli pa ntchito monga kuweta nsomba, ulimi, ndi ntchito zina.

Kodi Dziko Likutsatira Nzeruzi?

Ngakhale kuti pachionetserochi anagogomezera kwambiri zotsatira “nzeru zam’chilengedwe,” anthu ambiri m’dzikoli satsatira nzeruzi ayi. Anthu amene amalimbikitsa kutsatira nzeruzi sakumveka chifukwa cha phokoso la umbuli, dyera, ndi ziphuphu limene langoti buu padziko lonse. Motero, pa malo ena achionetserochi anati dziko lathuli ndi “Dziko Lovulala.” Koma ngakhale anthu a zolinga zabwino sakudziwa njira yodalirika yothetsera mavuto a anthu ndiponso a kuwonongeka kwa chilengedwe padzikoli. Baibulo limanena kuti njira zothetsera mavutowa si zoti anthu angazidziwe mwa nzeru ndi luntha lawo ayi. (Yeremiya 10:23) Koma tisataye mtima ngakhale pang’ono. N’chifukwa chiyani tikutero?

Baibulo limatiuza kuti Mlengi wathu, yemwe ali Chimake cha nzeru zonse, adzachitapo kanthu pa zochitika za padziko pano, anthu asanawonongeretu chilengedwe chake. (Chivumbulutso 4:11, 11:18) Lemba la Salmo 37:10,11 limati: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” N’zoona kuti n’chinthu chanzeru kutsatira nzeru zam’chilengedwe, koma chinthu chanzeru koposa ndicho kutsatira nzeru za Mlengi powerenga ndi kumvera Mawu ake, Baibulo Loyera. (2 Timoteyo 3:16) Anthu onse amene amachita zimenezi adzaona okha dziko lathu lodwalali likuchiritsidwa ndiponso likusinthidwa n’kukhala paradaiso.—Luka 23:43.

[Chithunzi patsamba 24]

Poonetsera thovu

[Chithunzi patsamba 24]

Mabasi oyenda okha popanda dalaivala

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Chipinda chozungulira chomwe khoma lake lonse, ndi kudenga komwe kumaoneka vidiyo

[Chithunzi patsamba 25]

Phapo la Zomera linali ndi zomera 200,000 za mitundu 200

[Chithunzi patsamba 25]

Makina otsanzira zochita za anthu anasangalatsa anthu powaimbira nyimbo