Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Achinyamata Kupeza Zomwe Amafunikira

Thandizani Achinyamata Kupeza Zomwe Amafunikira

Thandizani Achinyamata Kupeza Zomwe Amafunikira

ACHINYAMATA amafuna munthu woti azimuuza zolinga zawo, zimene amalakalaka, ndiponso mavuto awo. Amafunanso kukhala ndi anzawo a khalidwe labwino. Ndipo akamasinkhuka, achinyamata amafuna kuti azidziona kuti iwowo ndi munthu pawokha. Makolo akamathandiza ana awo pa zinthu zofunikirazi, amawateteza ku anthu amene angathe kuwavulaza, monga amene amakumana nawo pa Intaneti.

Achinyamata amafuna kunena zakukhosi kwawo. Achinyamata amaoneka ngati kuti safuna kunena zakukhosi kwawo, kapena kuti amakonda kuchita zinthu mwachinsinsi. Koma zoona zake n’zakuti, iwo amafuna kulankhula ndi winawake makamaka inuyo makolo awo, ndipo amafuna kukuuzani nkhani zazing’ono ngakhalenso zazikulu. Ndiye funso n’lakuti, Kodi inuyo mumakhala tcheru kuwamvetsera?—Yakobe 1:19.

Musatanganidwe kwambiri ndi zinthu n’kufika polephera kugwiritsira ntchito mwayi wamtengo wapatali umene mumakhala nawo wocheza ndi ana anu. Ngati kuchita zimenezi kukukuvutani, mungachite bwino kuganizira mozama malangizo a m’Baibulo akuti: “Mutsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Kodi pangakhale chilichonse chofunika kwambiri kuposa ana anu?

Musamafulumire kuganiza kuti ana amakonda kufunsa malangizo kwa anzawo kusiyana ndi kwa makolo awo. Ofufuza ena anafunsa ana asukulu oposa 17,000 oyambira sitandade 6 mpaka fomu 4 kuti atchule kuti ndani pa anthu otsatirawa amene iwowo amatengera kwambiri zochita zawo; makolo awo, anzawo, anthu otchuka, ndiponso aphunzitsi awo. Pafupifupi theka la anawa anatchula kuti amatengera kwambiri zochita za makolo awo.

Motero, n’zoonekeratu kuti makolonu muli ndi udindo wofunika zedi wochita zinthu zothandiza ana anu kudzakhala anthu olongosoka. Mayi wina anati: “Sikuti zonse zimene munganene anawo angazimvere. Komabe, simungawathandize m’njira iliyonse ngati mutangokhala chete.”

Achinyamata Amafuna Kukhala ndi Anzawo. Mtsikana wina wa zaka 15 anati: “Nthawi zambiri makolo sadziwa zimene ana awo amachita pa Intaneti, kapena kungoti alibe nazo ntchito n’komwe.” Koma masiku ano, si chinthu chanzeru kuti makolo azingokhala osadziwa kuti ana awo akucheza ndi ndani. Kodi mumadziwa anthu amene ana anu amacheza nawo kunyumba, kusukulu kapenanso pa Intaneti? Baibulo limati: “Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Inde, pali zifukwa zomveka zoti muziona mosamala anthu amene ana anu amacheza nawo.

Koma sikuti kusamala n’kuteteza chabe anawo ku zoipa. Ana amafunikiranso kukhala ndi anzawo oyenerera. Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.” (Miyambo 13:20) Motero, m’pofunika kuthandiza ana anu kupeza anzawo amakhalidwe abwino, monga ana anzawo omwe akupereka chitsanzo chabwino pankhani yokumbukira Mlengi wawo.—Mlaliki 12:1.

Yehova Mulungu amasankha mabwenzi ake mosamala, ndiye tiziyesetsa kumutsanzira. (Salmo 15:1-5; Aefeso 5:1) Inde, chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pamoyo zimene mungaphunzitse ana anu mwa kuwalangiza kapena mwa chitsanzo chanu, ndicho kusankha mabwenzi akhalidwe labwino.—2 Atesalonika 3:6, 7.

Achinyamata Amafuna Kumadziona Kuti Iwowo ndi Munthu Pawokha. Mbali yofunika kwambiri ya kusinkhuka n’njakuti mwanayo amayamba kudziona kuti ndi munthu payekha, ndipo amakhala ndi makhalidwe akeake, omusiyanitsa ndi ana ena. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Mwana adziwika ndi ntchito zake.” (Miyambo 20:11) Mbali ya udindo wanu monga kholo ndiyo kukhomereza mfundo zolungama m’mitima ya ana anu.—Deuteronomo 6:6, 7.

Taganizirani chitsanzo ichi: Nthawi zambiri makolo amachita kum’sankhira mwana wamng’ono zovala zoti avale tsiku ndi tsiku, podziwa kuti m’tsogolo mwanayo adzafika podziwa yekha kavalidwe kabwino. Koma kodi mwana wamkulu, wa zaka 30 angamachite kuvekedwa ndi makolo ake? Ayi ndithu, munthu wabwinobwino sangachite zimenezi. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha zovalachi, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Muvale umunthu watsopano,” womwe ndi wofanana ndi wa Khristu. (Akolose 3:10) Mungathandize ana anu kuvala umunthu watsopano mwa kuwalangiza mwachikondi ndi ‘kuwaphunzitsa kulingalira bwino.’ (Aefeso 6:4) Ndipo akamakula n’kuyamba kuchita zinthu pawokha, m’posavuta kuti asankhenso ‘kuvala umunthu watsopano’ womwe ndi wokongola ndi wosangalatsa.—Deuteronomo 30:19, 20.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi mfundo zomwe Mawu a Mulungu amaphunzitsa, ana anga amaziona bwanji kwenikweni?’ Kodi ndingawathandize bwanji “kukhala a maganizo abwino.” (Tito 2:12) Cholinga si choti mwana wanu akhale womvera mwachiphamaso chabe ayi. Ana ena amaoneka ngati kuti akumvera chilichonse chimene auzidwa, sachulutsa mafunso, sachita makani, kapena kuderera. Koma dziwani kuti mwana amene amangovomereza zilizonse zimene mukufuna, tsiku lina adzavomerezanso zimene dziko likufuna. Motero, phunzitsani mwana wanu “kugwiritsa ntchito luntha la kulingalira.” (Aroma 12:1) Athandizeni kuona chifukwa chimene mfundo za m’Baibulo zilili zomveka ndiponso mmene zimatithandizira.—Yesaya 48:17, 18.

N’zoona kuti kuthandiza achinyamata kuthana ndi mavuto a m’moyo wawo kumafuna khama. Komatu n’kothandiza zedi! Ana anu akamatsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene mwachita khama kuwaphunzitsa, munganene mochokera pansi pa mtima kuti ana ‘ndiwodi cholandira chochokera kwa Yehova.’—Salmo 127:3.

[Zithunzi patsamba 9]

Thandizani ana anu kuti azisankha anzawo achikhristu omwe ali ndi makhalidwe abwino