Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Ofufuza apeza kuti “munthu akamalankhula pa foni ya m’manja akuyendetsa galimoto, maganizo ake amasokonezeka mofanana ndi munthu amene waledzera, ngakhale foniyo ataichuna kuti asachite kuigwira m’manja.”—ZACHOKERA KU BUNGWE LOFALITSA NKHANI LA REUTERS, KU UNITED STATES.

M’miyezi isanu yoyambirira ya mu 2006, mbava za mfuti zabera anthu m’mabasi a mumzinda wa Guatemala City, nthawi zoposa 30,200. Mbavazi zinapha madalaivala kapena makondakitala 14, ndiponso anthu 10 okwera mabasiwa.—ZACHOKERA MU NYUZIPEPALA YA PRENSA LIBRE, KU GUATEMALA.

A bungwe Loona Zaumoyo Padziko Lonse anapeza kuti pamayiko 124 amene anachita nawo kafukufuku wawo wokhuza kutenga ndi kuyeza magazi, mayiko 56 “sanayeze magazi onse amene anthu anapereka, n’cholinga choti aone ngati ali ndi HIV, matenda otupa chiwindi a gulu la B ndi C ndiponso chindoko.”—ZACHOKERA KU BUNGWE LOONA ZAUMOYO PADZIKO LONSE, KU SWITZERLAND.

Ku Australia, anthu amene anangolowana popanda ukwati anawonjezeka. M’ma 1960 panali anthu asanu pa 100 aliwonse otero koma mu 2003 analipo anthu oposa 70 pa anthu 100 aliwonse.—ZACHOKERA KU YUNIVESITE YA MELBOURNE, KU AUSTRALIA.

Nthenda ya Shuga ndi Mliri wa Padziko Lonse

Magazini ya The New York Times, inati kafukufuku wa bungwe Loona za Matenda a Shuga Padziko Lonse akusonyeza kuti m’zaka 20 zapitazo, anthu opezeka ndi matenda a shuga padziko lonse anawonjezeka kuchokera pa 30 miliyoni kufika pa 230 miliyoni. Pa mayiko 10 amene ali ndi odwala ambiri, mayiko 7 ndi osauka. Pulezidenti wa bungweli, Martin Silink anati: “Nthenda ya shuga ndi imodzi mwa matenda amene avutitsa anthu kwambiri padziko lonse.” Lipoti la m’magaziniyi linati: “M’mayiko ena osauka kwambiri, anthu akangodwala matenda amenewa, sachedwa kufa.”

Njanji Yodutsa Pamwamba Kwambiri Kuposa Ina Iliyonse

Mu July 2006, anatsegulira njanji yodutsa pamwamba kwambiri ya sitima zapamtunda. Njanjiyi imachokera mumzinda wa Beijing kupita ku Lhasa, lomwe ndi likulu la dziko la Tibet ndipo uwu ndi mtunda wa makilomita pafupifupi 4,000. Nyuzipepala ya The New York Times inati: “Pokonza njanjiyi panagona luso lalikulu zedi, chifukwa choti yadutsa m’dera lokhala ndi madzi oundana omwe amatha kusungunuka mosayembekezereka ndiponso njanjiyi yadutsa m’mwamba kwambiri mpaka kufika mamita 4,800.” Vuto limodzi limene akatswiri okonza njanjiyi anakumana nalo linali loonetsetsa kuti maziko ake azikhalabe pamadzi oundana kwa chaka chonse, kuti ikhazikike bwinobwino. Chifukwa choti panjanjiyi sitima imayenda pamwamba kwambiri, amachita kupopera mpweya mu sitimamo kuti anthu azitha kupuma bwinobwino ndipo pampando uliwonse amaikaponso botolo la mpweya la munthu amene wakhalapo.

“Ophunzira Onamizira”

Ophunzira 10 kapena mpaka 20 pa ophunzira 100 aliwonse amene amalembetsa kuti akachite maphunziro a zinenero zosiyanasiyana payunivesite ina ku France “sapezeka panthawi ya maphunzirowa,” inatero nyuzipepala ya Le Figaro. Ena amangonamizira kuti ndi ophunzira pofuna kuti aziwatsitsirako mtengo wa ndege, basi, hotela, kapenanso woonerera mafilimu. Pofuna zimenezi, ophunzira onamizirawa amalembetsa kuchita maphunziro a zinenero zimene ambiri amazithawa, monga Chibelarasha, Chifinishi, kapenanso Chiswahili. Zachinyengozi n’zofala chifukwa choti payunivesiteyi saona kuti ndani sakubwera m’kalasi. Nyuzipepalayo inati: “Ophunzirawa amalembetsa sukuluyi pa Intaneti ndipo pakangopita masiku angapo, amawatumizira makhadi osonyeza kuti ndi ophunzira a pa yunivesiteyo.

‘Tinabisika M’phanga’

Asayansi a ku Israel akukhulupirira kuti atulukira mitundu yatsopano yokwana 8 ya tizilombo. Tizilomboti anatipeza m’phanga lina “limene lakhala lobisika” kwa zaka zochuluka zedi. Inatero nyuzipepala ya The Jerusalem Post. Anthu okumba miyala anapeza una wopita pansi umene unakafika m’chiphanga chachikulu makilomita awiri ndi theka mlitali mwake, ndipo mbali ina ya m’kati mwa chiphangachi inali ndi dziwe lalikulu. Pa tizilombo tatsopanoti, pali tina tofanana ndi zinkhanira, ndipo tilipo mitundu iwiri yokhala ngati nkhanu za m’nyanja ya m’chere komanso mitundu iwiri yokhala ngati nkhanu za m’mitsinje, ndiponso pali mitundu inayi ya tizilombo tapamtunda.