Chinthu Chokhalitsa Kuposa Luso la Zosemasema ndi Zoumbaumba
Chinthu Chokhalitsa Kuposa Luso la Zosemasema ndi Zoumbaumba
Yosimbidwa ndi Rakel Koivisto
Mu 1950, mfundo zanga zokhudza mmene chiboliboli cholemekeza anthu amene anamwalira pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, zinaposa za anthu ena onse m’dziko lathu. M’chaka chotsatira, chiboliboli chachikulu cha mwala chomwe ndinasema chinaonetsedwa pa mwambo wofunika kwambiri ku Tuusula, m’dziko la Finland. Koma ineyo sindinapezeke nawo pamwambowo. Tandilolani ndifotokoze chifukwa chake.
NDINABADWA m’chaka cha 1917, ndipo ndine mwana womaliza m’banja lathu lomwe muli ana 8. Tinkakhala ku midzi, cha kum’mwera m’dziko la Finland. Ngakhale kuti tinali osauka, ndinali wosangalala ndipo sindinkada nkhawa. Makolo anga anali odalirika ndi oopa Mulungu, ndipo anatiphunzitsa kuti tiziona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambiri. Banja lathu lonse linkakonda kwambiri Baibulo lomwe bambo anagula.
Ndili mwana, ndinkakonda kusema tiziboliboli tamatabwa. Ndipotu azibale anga anaona kuti ndili ndi luso lapadera kwambiri, choncho anandilimbikitsa kuti ndipite ku sukulu yophunzitsa luso la zosemasema ndi zoumbaumba. Patapita nthawi, ndinavomerezedwa kukaphunzira luso limeneli ku yunivesite inayake, yomwe ili mu mzinda wa Helsinki. Sukulu yapamwamba imeneyi ndi likulu la maphunziro a luso losiyanasiyana m’dziko la Finland. Popeza ndinali kamtsikana kokulira ku midzi, ndinkachita chidwi kwambiri ndi maonekedwe komanso zochitika za pasukuluyi. Nditamaliza sukulu mu 1947, ndinaganiza kuti ndikhoza kupanga mwaluso chinthu chinachake chomwe chingakhale nthawi yaitali m’dzikoli.
Ndinasintha Zolinga Zanga
Zolinga zanga zinasinthiratu. Tsiku lina mkulu wanga Aune anabwera kwa ine akusangalala kwambiri ndipo anati: “Ndapeza choonadi!” Iye anali atapatsidwa buku lakuti “Mulungu Akhale Woona,” lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Zimenezi sizinandikhudze n’komwe. Patapita masiku ochepa, ndinaona kuti mtsikana wina yemwe ndinkaphunzira naye ku yunivesite anali ndi buku lofanana ndi limene mkulu wangayu anapatsidwa. Nditayamba kulinyoza, mtsikanayo anati: “Khala chete! Bukuli lingakuthandize kumvetsa bwino Baibulo.” Zitatero, inenso ndinapeza langa ndipo ndinaliwerenga lonse nthawi imodzi. Sindinalinyozenso, m’malo mwake, linandithandiza kuzindikira kuti anthu a Mboni ali ndi choonadi. Ndinazindikiranso kuti Yehova Mulungu angandipatse moyo wosatha, womwe luso la zosemasema silingandipatse.
Nditangoyamba kucheza ndi a Mboni, sanandiitanire ku misonkhano yawo. Choncho ndinaganiza kuti kumisonkhanoyi kumapita a Mboni okhaokha. Komabe, ndinalimba mtima n’kuwapempha ngati zingatheke kuti ndizipita nawo. Ndinasangalala kwabasi atandiuza kuti kumisonkhano imeneyi kumapita munthu aliyense. Kupezeka pa misonkhanoyi
kunalimbitsa chikhulupiriro changa ndipo ndinasankha kuti ndidzipereke kwa Yehova. Ndiyeno, pa November 19, 1950, ndinasonyeza poyera kuti ndadzipereka kwa Yehova pamene ineyo pamodzi ndi mkulu wanga tinabatizidwa. Tinasangalala kwambiri pamene azichemwali athu anayi pamodzi ndi makolo athu nawonso m’kupita kwa nthawi anakhala Mboni.Ndichite Chiyani Pamoyo Wanga?
Pamene ndinkaphunzira Baibulo ndi a Mboni, luso langa losema ziboliboli linkapitabe patsogolo. Nditamaliza maphunziro anga ku yunivesite, ndinayamba ntchito yothandiza pulofesa wa maphunziro a luso la zosemasema. Ndiyeno, monga mmene ndalongosolera kuchiyambi kwa nkhaniyi, mfundo zanga zokhudza chiboliboli cholemekeza anthu amene anamwalira pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, zinaposa za anthu ena onse m’dziko lathu. Ndinaganiza kuti mutu wa nkhani yokhudza chibolibolichi ukhale wakuti “Ulendo Umene Sanabwerekonso.” Ndinasankha mutu umenewu kusonyeza mmene ndinasinthira maganizo anga pankhani ya nkhondo. (Yesaya 2:4; Mateyo 26:52) Komano pamene chibolibolichi, chomwe n’chachitali mamita asanu, chinaonetsedwa pa mwambo wolemekezeka kwambiri, ine sindinapezekepo. Ndinatero chifukwa pamwambo umenewu pankachitika zinthu zosonyeza kukonda dziko lako, ndipo zimenezi n’zosemphana ndi mfundo zimene ndinaphunzira m’Baibulo.
Ndinkapeza mwayi woti ndikanatha kuyamba ntchito yabwino kwambiri chifukwa anthu ambiri ankandidziwa chifukwa cha luso langa la zosemasema. Komabe, ndinaganiza kaye mofatsa n’cholinga choti ndiyambe kuchita zinthu zofunika kwambiri. Ngakhale kuti ndinkakonda ntchito yangayi, ndinkafuna kwambiri kuthandiza ena mwauzimu. N’chifukwa chaketu mu 1953, ndinakhala mpainiya, kutanthauza kuti mlaliki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova.
Nthawi zina anthu ankandinena kuti ndikungoononga luso langa. Koma ndinazindikira kuti zinthu zilizonse zomwe ndingapeze chifukwa cha luso limeneli n’za kanthawi basi. Ngakhale ziboliboli zamiyala, m’kupita kwa nthawi zimayamba kunyenyeka pang’onopang’ono. Komano, popeza ndinayamba kuchita upainiya, ndimagwiritsa ntchito nthawi yanga yambiri pothandiza anthu ena kuti ayende pa njira ya kumoyo wosatha. (Yohane 17:3) Ngakhale zinali choncho, sindinaiwaliretu kusema ziboliboli. Nthawi zina, ndinkasema tiziboliboli n’kuika m’nyumba mwanga, ndipo tina ndinkagulitsa kuti ndipeze ndalama zodzithandizira.
Ndinasamukira ku Dera la Kumidzi
Mu 1957, patatha zaka zinayi ndikuchita upainiya ku Helsinki, ndinapemphedwa ndi ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Finland kuti ndikatumikire ku Jalasjärvi. Dera limeneli lili kumadzulo m’dziko la Finland. Kumeneko ndinafunikira kuti ndikatumikire pamodzi ndi Anja Keto, yemwe anali wamng’ono kwa ine ndi zaka 17. Ngakhale kuti sindinkamudziwa Anja, ndinavomera ndi mtima wonse kukatumikira naye limodzi. M’derali a Mboni tinali ine ndi Anja basi, choncho nthawi zambiri tinkapitira limodzi mu utumiki. Kenaka tinakhala mabwenzi a ponda apa nane m’pondepo.
Kusamukira ku Jalasjärvi kunatanthauza kuti ndikayambirenso moyo wa kumidzi, wofanana ndi womwe ndinkakhala ndisanasamukire ku likulu la dzikoli chifukwa cha luso langa la zosemasema zaka 20 zapitazo. Ku dera limeneli, nyengo ya chisanu inali yozizira kwambiri, moti nthawi zina kunkagwa chipale chofewa mpaka kufika m’chiuno, zomwe zinkachititsa kuti tizivutika kuyenda. Tinkakhala m’kanyumba kamatabwa, komwe kanali kosakongola n’komwe. Ndipo tinkatunga madzi pachitsime chomwe chinali pafupi. Nthawi zambiri kukacha, tinkapeza madzi omwe tinatunga ataundana pamwamba ponse chifukwa cha kuzizira. Komabe ngakhale zinthu zinali chonchi, tinali ndi chilichonse chofunikira pamoyo wathu. (1 Timoteyo 6:8) Amenewatu anali masiku osangalatsa kwabasi, ndipo tinkachita zinthu zambiri.
Kutanganidwa ndi Ntchito Yosangalatsa
Titayamba kumene utumiki wathu, zinthu sizinkatiyendera bwino kwenikweni chifukwa anthu a kuderali ankatisala. Pofuna kuwathandiza kuti amvetse bwino ntchito yathu, tinakonza zoonetsa mafilimu opangidwa ndi Mboni za Yehova. Ena mwa mafilimu amenewa anali akuti The New World Society in Action ndi The Happiness of the New World Society. Mafilimuwa anathandiza anthu amenewa kutidziwa bwino ndiponso kumvetsa gulu lathu. Anawathandizanso kuti aone mmene ntchito yathu imathandizira anthu padziko lonse. Ndipotu anthu ambiri ankasonkhana tikamaonetsa mafilimuwa.
Panthawi ina, Eero Muurainen, woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova, anaonetsa filimu yakuti The New World Society in Action m’holo ina ya m’deralo. Ndiyetu kunafika chinamtindi cha anthu, moti ine ndinangodzipanikiza pa kona kumbuyo kwenikweni kwa holoyo. Chifukwa chosowa poponda, ndinangoima ndi mwendo umodzi uku n’tatsamira
khoma. Ndiyeno filimuyo itatha, anthu ambirimbiri anatipempha kuti tidzawachezere.Tinkagwiritsanso ntchito wailesi yaikulu ya kaseti yomwe tinkaikamo nkhani za Baibulo zojambulidwa pa kaseti polalikira ku nyumba za m’mafamu. Panthawi ina tinagwirizana zoti anthu akamvere nkhani zimenezi kunyumba ya banja linalake nthawi ya 7 koloko madzulo, ndipo tinaitana anthu onse a m’mudziwo. Ndiyeno mamawa kwambiri tsiku limenelo, tinanyamuka pa njinga zathu kupita kukalalikira ku mudzi wina womwe uli pa mtunda wa makilomita 25, tikumaganiza kuti tibwerako kusanade. Komano titangochoka m’mudzimo, kunagwa chimvula chomwe chinachititsa misewu kukhala matope okhaokha.
Ndiyeno pobwerera kunyumba, njinga zathuzo zinangoti matope tho mpaka matayala osazunguliranso, choncho panalibenso kuchitira mwina koma kuzinyamula basi. Chifukwa cha zimenezi tinanyamuka mochedwa kwambiri popita ku nyumba imene tinagwirizana kuti anthu akamvere nkhani. Tinanyamula wailesi yathu yaikuluyo ndipo tinakafika 10 koloko usiku. Ngakhale tinkapita, tinkaganiza kuti sitikapeza munthu ndi mmodzi yemwe. Komano titafika, tinadabwa kwabasi kupeza anthu atadzadziratu m’nyumbamo akutidikirira. Ndiyeno nkhaniyo itatha, tinakambirana ndi anthuwo mosangalala. Tinabwerera kunyumba kwathu mbandakucha titatheratu n’kutopa, koma tili n’chimwemwe chodzadza tsaya.
Midzi ya m’dera limeneli inali yotalikirana kwambiri. Choncho Mboni za m’derali zinatithandiza kuti tigule galimoto inayake ya mbiri yakale yopangidwa ku Russia. Zimenezi zinafewetsako ntchito yathu yolalikira. Kenako, galimoto yathu inadziwika kwambiri m’derali moti bishopu wa kumaloko anachenjeza anthu ake kuti asamalandire azimayi awiri oyenda pa galimoto ya buluu. Nthawi yomweyo chenjezoli linachititsa anthu kufuna kudziwa azimayi awiriwo, ndiponso chifukwa chake anali oopsa. Chifukwa cha zimenezi, tinkatha kukambirana bwino kwambiri nkhani za m’Baibulo ndi anthu ochuluka. Indedi, mawu a Yesaya awa n’ngoona: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.”—Yesaya 54:17.
M’kupita kwa nthawi, ntchito yathu inabala zipatso. Tinayamba kuchita misonkhano mlungu uliwonse ndi kagulu ka anthu achidwi. Pang’ono m’pang’ono gulu lathulo linakula. Mu 1962, mpingo wa anthu 18 unakhazikitsidwa, ndipo ambiri mwa iwo anali azimayi. Kenaka patapita zaka ziwiri, ine ndi Anja anatitumiza ku chigawo cha Ylistaro, m’dera lomwelo la Jalasjärvi.
Malo Ochititsa Chidwi
Tinkasangalala ndi dera lokongola ndi labata la kuchigawo chimene anatitumizako. Koma kwenikweni tinkasangalala kwambiri chifukwa cha anthu a kumaloko. Anali anthu odziwa kulandira alendo ndiponso ansangala. N’zoona ndithu kuti ambiri mwa anthu amenewa n’ngokonda kwambiri za chipembedzo ndiponso dziko lawo, koma nthawi zina ankatikana mokwiya kwambiri. Ena mwa anthu amenewa ankalemekeza kwambiri Baibulo. Nthawi zambiri tikamalankhula nawo n’kutsegula Baibulo, azimayi ankasiya kaye ntchito zawo, ndipo azibambo ankavula zipewa, zomwe samazivula chisawawa. Nthawi zina tikamaphunzira Baibulo ndi munthu wina, banja lake lonse, ngakhale anthu oyandikana naye nyumba, ankabwera ndi kukhala nawo paphunzirolo.
Zochita za anthu oona mtima amene ndinkakumana nawo muutumiki zinandilimbikitsa kupitiriza luso langa la ziboliboli. Ndikapeza nthawi, ndinkaumba ziboliboli zadongo. Popeza kuti ine ndimachita chidwi kwambiri ndi anthu omasuka ndiponso ansangala, pafupifupi ziboliboli zonse zomwe ndinkaumba zinali zoyerekezera anthu a makhalidwe amenewa. Zambiri mwa zibolibolizi zinkasonyeza azimayi akugwira ntchito zawo za pakhomo. Ponena za ziboliboli
zanga, magazini ina inati: “Kungoona zibolibolizi zimakupangitsa kumva bwino, kuona kuti uli pa mtendere, komanso umasangalala ndipo mtima umakhala m’malo . . . Amatha kupanga ziboliboli zosangalatsazi chifukwa choti amakonda anthu komanso ndi waluso.” Ngakhale zinthu zinali chonchi, ndinkasamala kwambiri kuti ndisaike mtima wanga wonse pantchito yosema ndi kuumba ziboliboliyi. Sindinasunthike pa chosankha changa chotumikira Yehova nthawi zonse.Mu 1973, ndinapeza mwayi wa ntchito umene sindikanayerekeza n’komwe kuukana. Ndinapemphedwa kuti ndiumbe chiboliboli chachikulu choti chikhale pa malo ofikira alendo ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova yomwe ili mu mzinda wa Vantaa, ku Finland. Ntchito yonse inali yokhudza zomwe zili pa lemba la Salmo 96:11-13. Ndinasangalalatu kwabasi kugwiritsa ntchito luso langa potamanda Yehova!
Pochita upainiya, ndinkasema ndi kuumba ziboliboli kuti ndisangalale ndiponso pofuna kupeza zosowa zanga basi. Koma mu 1970, ndinadabwa kwambiri nditapatsidwa ndalama zopumira pa ntchito yosema ndi kuumba ziboliboli. Ndinayamikira ndithu thandizo la ndalama limeneli, komabe, ndinkadzifunsa mumtima mwanga kuti, ‘Kuteroko ndikanati ndiike mtima wanga wonse pantchito ya ziboliboliyi mphoto yanga ikanakhala imeneyi basi? Kupatsidwa chabe ndalama zochuluka zoti zindithandize pamene ndapuma pa ntchito basi?’ Zimenezi sikanthu poziyerekezera ndi mphoto ya moyo wosatha.—1 Timoteyo 6:12.
Kubwereranso ku Mzinda
Moyo ndiponso utumiki wathu unasintha kwambiri m’chaka cha 1974. Tinatumizidwa ku mzinda waukulu wotchedwa Turku. Panthawi imeneyo, nyumba zambiri zinkamangidwa mu mzindawu, komanso anthu ambiri ankasamukira mu mzinda umenewu. Choncho, panafunika Mboni zina zodzalalikira kumeneku. Poyamba, sitinasangalale kwenikweni ndi gawo lathu latsopano la m’tauni. Kulalikira kwa anthu okhala mu mzinda kunali kovuta kwabasi, chifukwa anthu ochuluka anali opanda chidwi. Komano pang’ono ndi pang’ono tinazolowera gawo lathulo, ndipo tinapeza anthu ambiri amene ankayamikira kwambiri choonadi cha m’Baibulo.
Kwazaka zambiri, ine ndi Anja takhala ndi mwayi wothandiza anthu oposa 40 kudzipereka kwa Yehova. Timasangalalatu kwabasi chifukwa cha ana athu auzimu amenewa! (3 Yohane 4) Ngakhale kuti masiku ano thupi langa n’lofooka, ndimaona kuti Yehova akundichirikizabe. Kuonjezera pamenepa, abale ndi alongo mumpingo amandikonda, ndiponso mpainiya mnzanga Anja amandilimbikitsa kwambiri. (Akolose 4:11; Salmo 55:22) Pamene ndinakumana ndi Anja pafupifupi zaka 50 zapitazo, sitinaganizepo zoti tingachitire limodzi utumiki wathu wa upainiya kwa moyo wathu wonse.
Mwambi wina wa m’Chilatini umati, “Moyo n’ngwaufupi, koma ntchito za luso zimakhala kwamuyaya.” Koma ine sindimayendera mwambi umenewu. Ndimagwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo opezeka pa 2 Akorinto 4:18, omwe amati: “Zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.” Zinthu zonse zosangalatsa zomwe ndinapeza chifukwa cha luso langali ndi “zinthu zooneka,” zomwe n’zakanthawi chabe. Zinthu zimenezi sindingaziyerekezere n’komwe ndi chimwemwe chomwe ndapeza chifukwa chotumikira Yehova, ndipo sizingandipatse moyo wosatha. Ndine wosangalala kwambiri chifukwa ndinadzipereka kotheratu ku “zinthu zosaoneka,” zomwe n’zokhalitsa kuposa luso la zosemasema ndi zoumbaumba.
[Chithunzi patsamba 19]
Ndikusema chiboliboli chamwala
[Chithunzi patsamba 21]
Ndili ndi Anja (kumanzere), mu 1957
[Chithunzi patsamba 22]
Ndili ndi Anja (kumanja) masiku ano