Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzikoli Likulowera Kuti?

Kodi Dzikoli Likulowera Kuti?

Kodi Dzikoli Likulowera Kuti?

BAIBULO linaneneratu kuti makhalidwe adzalowa pansi, ndipo linafotokoza kuti: “M’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, . . . owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha.”—2 Timoteyo 3:1-5.

Mwina mukuvomereza kuti ulosi wa Baibulo umenewu ukukwaniritsidwa ndendende masiku ano. Koma chochititsa chidwi n’choti ulosi umenewu unalembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Ulosiwu umayamba ndi mawu akuti: “M’masiku otsiriza.” Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?

“Masiku Otsiriza” a Chiyani?

Mawu akuti “masiku otsiriza” afala kwambiri masiku ano. Mu Chingelezi mokha, mawu amenewa amapezeka m’mitu ya mabuku ambirimbiri. Mwachitsanzo, pali buku laposachedwapa lakuti The Last Days of Innocence—America at War, 1917-1918. (Masiku Otsiriza a Kusadziwa ZoipaDziko la America Lili pa Nkhondo, 1917-1918) Mawu oyambirira ofotokoza bukulo akunena kuti akatchula mawu akuti “masiku otsiriza,” amakhala akunena za nthawi yodziwika bwino imene makhalidwe alowa pansi kwambiri.

Bukulo likupitiriza kuti: “Chaka cha 1914, dzikoli [la United States] linali kusintha kwambiri kuposa nthawi ina iliyonse m’mbuyomo.” Eyadi, mu 1914 dziko lonse linalowa m’nkhondo yoti sinachitikepo. Bukulo likuti: “Iyi sinali nkhondo yamasewera. Sinali ya asilikali kumenyana ndi asilikali chabe, koma mtundu kumenyana ndi mtundu.” Nkhondo imeneyi, malinga ndi mmene tionere, inachitika ku mayambiriro kwa nthawi imene Baibulo limati ndi “masiku otsiriza.”

Baibulo limaphunzitsa kuti dzikoli lisanathe, padzakhala nthawi yodziwika bwino yotchedwa “masiku otsiriza.” Limanena kuti kale panali dziko limene linapita, kapena kuti linatha, ndipo limati: “Dziko la panthawiyo linawonongeka pamene linamizidwa ndi madzi.” Kodi pamenepa akunena nthawi iti, ndipo ndi dziko liti limene linatha? Limenelo linali “dziko la anthu osaopa Mulungu” la masiku a Nowa. Dziko la masiku ano nalonso lidzatha. Koma anthu amene amatumikira Mulungu adzapulumuka, monga Nowa ndi banja lake.—2 Petulo 2:5; 3:6; Genesis 7:21-24; 1 Yohane 2:17.

Yesu Ananenapo za Mapeto

Yesu Khristu ananenaponso za “masiku a Nowa,” pamene “chigumula chinafika ndi kuwaseseratu [anthu] onsewo.” Anayerekezera zinthu zimene zinkachitika Chigumula chisanafike, kapena dzikolo litatsala pang’ono kutha, ndi zinthu zimene zidzachitika pa nthawi imene anati ndi “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 24:3, 37-39) Potchula za nthawi yomweyi, Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu akuti “kutha kwa dziko” kapena “mathedwe a nthawi ya pansi pano.”—The Jerusalem Bible ndi Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.

Yesu ananeneratu mmene zinthu zidzakhalire dziko litatsala pang’ono kutha. Potchulapo za nkhondo, iye anati: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina.” Akatswiri a mbiri yakale amati zimenezi zinayamba kuchitika mu 1914. M’pake kuti buku limene tatchula kale lija linanena kuti chaka cha 1914 m’pamene panayambira ‘nkhondo imene sinali yamasewera. Sinali ya asilikali kumenyana ndi asilikali chabe, koma mtundu kumenyana ndi mtundu.’

Pofotokoza ulosi wakewo, Yesu anawonjezera kuti: “Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Zonsezi ndi chiyambi cha masautso.” Ananenanso kuti kudzakhala “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo.” (Mateyo 24:7-14) Taonadi zimenezi zikuchitika masiku athu ano. Makhalidwe alowa pansi kwambiri ndipo zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa Baibulo.

Kodi tiyenera kukhala ndi moyo wotani masiku ano pamene makhalidwe aipa kwambiri? Tamverani zimene mtumwi Paulo analembera Akhristu ku Roma pankhani ya makhalidwe oipa. Anatchula “zilakolako zamanyazi za kugonana” zimene anthu anali nazo ndipo anati: “Akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo n’kumachita zosemphana ndi chibadwa. Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi natenthetsana okhaokha mwachiwawa m’chilakolako choipa, amuna ndi amuna anzawo, kuchitirana zonyansa.”—Aroma 1:26, 27.

Akatswiri a mbiri yakale amati panthawi imeneyo pamene makhalidwe a anthu anali kuloweralowera pansi, “Akhristu kulikonse ankasowetsa mtendere anthu akunja opandiratu khalidwe chifukwa cha makhalidwe awo abwino.” Ndiye tidzifunse kuti: ‘Nanga ineyo ndi anthu amene ndimakonda kucheza nawo bwanji? Kodi ndife anthu amakhalidwe abwino kusiyana ndi anthu opanda khalidwe a dzikoli?’—1 Petulo 4:3, 4.

Nkhondo Imene Tili Nayo

Baibulo limatiphunzitsa kuti ngakhale kuti makhalidwe oipa ali paliponse, tifunikira kukhala ‘opanda chifukwa chotineneza nacho ndiponso osalakwa. Tikhale ana a Mulungu opanda chilema pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota’ uno. Kuti tichite zimenezi, tiyenera ‘kugwira zolimba mawu a moyo.’ (Afilipi 2:15, 16) Mawu a m’Baibulo amenewa amasonyeza zimene Akhristu ayenera kuchita kuti asaipitsidwe ndi makhalidwe oipa a dzikoli. Iwo ayenera kutsatira kwambiri zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa ndipo ayenera kuzindikira kuti mfundo zake n’zopindulitsa kwambiri pamoyo wawo.

“Mulungu wa dongosolo lino la zinthu,” Satana Mdyerekezi, akuyesetsa kukopa mitima ya anthu. (2 Akorinto 4:4) Baibulo limatiuza kuti iye “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” Atumiki ake, amene amamutumikira pochita zinthu ngati iyeyo, amadzisandutsanso chimodzimodzi. (2 Akorinto 11:14, 15) Amalonjeza anthu ufulu ndi kusangalala, pamene Baibulo limanena kuti, “iwo eniwo ali akapolo a chivundi.”—2 Petulo 2:19.

Musanyengedwe. Anthu amene amanyalanyaza mfundo za Mulungu zamakhalidwe abwino, amakumana ndi mavuto aakulu. M’Baibulo wamasalmo anati: “Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba [a Mulungu].” (Salmo 119:155; Miyambo 5:22, 23) Kodi tikukhulupiriradi zimenezi? Ngati tikukhulupirira, titeteze maganizo ndi mitima yathu kuti mabodza olimbikitsa makhalidwe oipa asatilowerere.

Komabe, anthu ambiri mopanda nzeru amaganiza kuti, ‘Ngati zimene ndikuchita sizikuswa malamulo, ndiye kuti palibe vuto.’ Koma zimenezi si zoona. Atate wathu wakumwamba ndiponso wachikondi amapereka malangizo amakhalidwe kuti akutetezeni, osati kuti akukhwimitsireni zinthu ayi. Iye ‘akukuphunzitsani kuti mupindule.’ Akufuna kuti mupewe mavuto ndi kuti musangalale ndi moyo. Baibulo limaphunzitsa kuti kutumikira Mulungu “kuli ndi lonjezo la moyo uno ndi umene ukubwerawo.” Umenewo ndiye “moyo weniweniwo,” moyo wosatha m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—Yesaya 48:17, 18; 1 Timoteyo 4:8; 6:19.

Choncho, taonani kuti kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa kuli ndi phindu kusiyana ndi kusatsatira, kumene kumangobweretsa mavuto. Anthu amene amamvera Mulungu, amakondedwa ndi iye ndipo amakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Mulungu akulonjeza kuti: “Wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Miyambo 1:33.

Dziko la Makhalidwe Abwino

Baibulo limanena kuti dzikoli likamadzapita, “woipa adzatha psiti.” Limanenanso kuti: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo.” (Salmo 37:10, 11; Miyambo 2:20-22) Choncho, anthu onse amakhalidwe oipa ndi onse amene amakana kutsatira zimene Mlengi wathu amaphunzitsa, adzachotsedwa pa dziko lapansi. Kenako, anthu okonda Mulungu adzakonza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso wofanana ndi amene Mulungu anaikamo anthu awiri oyambirira.—Genesis 2:7-9.

Ndiyetu tidzasangalala kukhala m’dziko lapansi lokongola la paradaiso. Anthu ena amene adzakhala ndi mwayi wokhala m’dziko limeneli, ndi anthu miyandamiyanda amene adzauka kuchokera kumanda. Timasangalala ndi malonjezo a Mulungu akuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” “[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Dziko lakale litatha, anthu oopa Mulungu anapulumuka

[Chithunzi patsamba 10]

Dzikoli likadzatha, dziko lapansi lidzakhala paradaiso