Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhala Mkhristu Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kukhala Mkhristu Kumatanthauza Chiyani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kukhala Mkhristu Kumatanthauza Chiyani?

“M’DZIKO lathu, kukhala Mkhristu kumatanthauza kupita kutchalitchi kamodzi pamlungu,” anatero Kingsley, wa m’dziko lina kuno ku Africa. Raad, wa ku Middle East, anafotokoza kuti: “Kwathu kuno anthu ambiri amaona Akhristu kuti ndi anthu omwe amatsatira zobwera ndi azungu pankhani ya kavalidwe, maphwando, ndi mmene amaonera akazi.”

Koma kodi kukhala Mkhristu kumangotanthauza kupita kutchalitchi kamodzi pamlungu, ndiponso kutsatira chikhalidwe ndi miyambo inayake basi? Kodi sizomveka kunena kuti mawu akuti “Mkhristu,” ayenera kutanthauza moyo wotsatira mfundo, maganizo, ndi makhalidwe amene Khristu analalikira ndiponso amene anali nawo? Kodi poyambirira penipeni Akhristu ankakhala motani?

Chikhristu Choyambirira Chinkakhudza Moyo Wonse wa Munthu

Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mukhalabe mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.” (Yohane 15:14) Popeza kuti zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa zinakhudza mbali zonse za moyo wa ophunzira ake, poyambirira iwo ankatchula chipembedzo chawo kuti ‘Njira.’ (Machitidwe 9:2) Patapita nthawi yochepa, “motsogoleredwa ndi Mulungu, ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu.” (Machitidwe 11:26) Dzina lawo latsopanoli linatanthauza kuti iwo ankakhulupirira kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, amene anaphunzitsa anthu chifuniro cha Atate wake wakumwamba. Chifukwa cha chikhulupiriro chimenechi, iwo anayamba kukhala moyo womwe unali wosiyana ndi wa anthu ena.

Zimene Khristu ankaphunzitsa zinalimbikitsa ophunzira ake kutsatira ziphunzitso za m’Baibulo. Zimenezi zinatanthauza kupewa “dama, chonyansa, khalidwe lotayirira, kupembedza mafano, kukhulupirira mizimu, maudani, ndewu, nsanje, kumapsa mtima, mikangano, . . . kumamwa mwauchidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotero.” (Agalatiya 5:19-21; Aefeso 4:17-24) Mtumwi Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Korinto kuti ena mwa iwo ankachita zinthu zimenezi. Ndiyeno anapitiriza kuti: “Koma mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa, mwayesedwa olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.”—1 Akorinto 6:9-11.

Munthu wina dzina lake E. W. Barnes anafotokoza m’buku lake la Chingelezi lakuti Mmene Chikhristu Chinayambira kuti: “Mabuku oyambirira onena za Chikhristu amafotokoza Akhristu kuti anali anthu amakhalidwe abwino ndi osunga malamulo a boma. Iwo ankafunika kukhala nzika zabwino ndiponso zomvera boma. Ankapewa makhalidwe oipa a anthu akunja. Iwo ankayesetsa kukhala amtendere ndiponso okhulupirika kwa anthu ena. Anaphunzitsidwa kukhala anthu aulemu, ndiponso olimbikira ntchito. Ngakhale kuti panthawiyo makhalidwe oipa anali ofala, iwo ankaonetsetsa kuti akutsatira mfundo za chipembedzo chawo, ndipo anali opanda chinyengo. Ankalemekeza ukwati ndipo aliyense m’banja ankakhala wodzisunga.” Umu ndi mmene Akhristu oyambirira analili.

Chizindikiro china cha Akhristu oyambirira chinali kugwira ntchito yawo yolalikira mwakhama. Khristu analamula otsatira ake kuti: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyo 28:19, 20) Jean Bernardi, yemwe ndi pulofesa pa yunivesite ya Sorbonne, ku Paris, m’dziko la France, anati: “[Akhristu] ankafunika kupita kulikonse ndi kukalalikira kwa munthu aliyense. Ankalalikira m’misewu ndi m’mizinda, m’misika ndiponso m’nyumba za anthu. Ankatero kaya akalandiridwa kapena ayi. Ankapita kwa osauka, ndi kwa olemera omwe. . . . Ankayenda maulendo a pamsewu, panyanja, ndi kukafika kumalekezero a dziko lapansi.”

Akhristu Oona Masiku Ano

Akhristu oona masiku ano ayenera kuonekeratu kuti makhalidwe awo ndi osiyana ndi a anthu ena, monga momwe Akhristu oyambirira analili. Mogwirizana ndi zimenezi, a Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira bwinobwino mfundo zimene Akhristu oyambirira anakhazikitsa. Anthu ena amatha kuona khama la Mboni za Yehova lokhala mogwirizana ndi ziphunzitso za m’Baibulo.

Mwachitsanzo, buku lina la Akatolika lakuti New Catholic Encyclopedia linanena kuti gulu la Mboni za Yehova limadziwika kuti ndi “limodzi mwa magulu a makhalidwe abwino koposa padziko lonse.” Nyuzipepala yotchedwa Deseret News ya mumzinda wa Salt Lake City, ku Utah, inanena kuti Mboni za Yehova “zimalimbikitsa anthu kukhala ndi mabanja olimba ndipo zimaphunzitsa anthu kukhala nzika zakhama pantchito ndiponso zoona mtima.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “A Mboni ndi anthu amene sasunthika pankhani ya makhalidwe abwino. Amakhulupirira kuti kusuta fodya, kumwa mowa mwauchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kutchova njuga, chiwerewere ndiponso kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndi makhalidwe amene amawononga moyo wauzimu wa munthu. Amaphunzitsa anthu kukhala oona mtima ndiponso olimbikira ntchito.”

Mboni zimachitanso khama kwambiri pantchito yawo yolalikira. Pankhaniyi, buku la Akatolika limene tatchula lija linanenanso kuti: “Udindo waukulu wa membala aliyense . . . ndi wochitira umboni za Yehova mwa kulengeza za Ufumu Wake umene wayandikira. . . . Kuti munthu akhale wa Mboni weniweni amafunika kuyesetsa ndithu kulalikira mogwira mtima.”

N’zoonekeratu kuti kukhala Mkhristu weniweni sikutanthauza kungokhala membala chabe wa mpingo wachikhristu. Yesu mwiniwakeyo ananeneratu kuti kudzakhala Akhristu ambiri onama. (Mateyo 7:22, 23) Mboni za Yehova zikukupemphani kuti muphunzire zimene Yesu anaphunzitsa ndi kuzigwiritsa ntchito pamoyo wanu. Izi ndi zimene kukhala Mkhristu kumatanthauza. Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, mudzakhala osangalala mukamazichita.”—Yohane 13:17.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Ndani amene Yesu anawatcha mabwenzi ake?—Yohane 15:14.

▪ Kodi Akhristu enieni amafunika kupewa makhalidwe ati?—Agalatiya 5:19-21.

▪ Kodi Akhristu amafunika kutenga mbali m’ntchito yotani?—Mateyo 28:19, 20.

[Zithunzi patsamba 26]

Akhristu enieni ndi akhama pantchito yolalikira, monga mmene Akhristu oyambirira analili