Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
FOTOKOZANI FANIZOLI
Tchulani anthu atatuwa a m’fanizo la Yesu la pa Luka 10:29-37. Lembani mayankho anu pansipa.
1. ․․․․․
2. ․․․․․
3. ․․․․․
▪ Kambiranani: N’chiyani chimakusangalatsani ndi zimene Msamariya anachita? Kodi mungachite chiyani kuti mukhale mnansi wabwino?
ZINACHITIKA LITI?
Tchulani mlembi wa buku lililonse la m’Baibulo lili pansipa, ndipo lembani mzera kuchokera pa dzina la bukulo kufika pa deti limene anamaliza kulilemba.
cha m’ma 537 B.C.E., 460, 455, 50-52 C.E., 66-70 C.E.
4. 2 Mbiri
5. Ezara
6. Agalatiya
NDINE NDANI?
7. Ndinafunsira nzeru kwa mandoda ndi kwa achinyamata koma ndinamvera zimene achinyamata anzanga anandiuza.
NDINE NDANI?
8. Paulo anandifanizira ndi chipangano, Phiri la Sinai, ndi Yerusalemu.
KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
Yankhani mafunso awa, ndipo lembani mavesi kapena vesi la m’Baibulo lomwe likusowapo.
Tsamba 9 Monga Nowa, kodi n’chiyani chimene chidzachitikira anthu amene amatumikira Mulungu? (2 Petulo 2:․․․)
Tsamba 10 Kodi olungama adzalandira chiyani? (Salmo 37:․․․)
Tsamba 12 Kodi n’chiyani chingachedwetse mkwiyo wanu anthu akakufananitsani ndi ena? (Miyambo 19:․․․)
Tsamba 26 Kodi tingatani kuti tikhale bwenzi la Yesu? (Yohane 15:․․․)
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
(Mayankho ali pa tsamba 29)
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Wansembe.
2. Mlevi.
3. Msamariya.
4. Ezara, 460 B.C.E.
5. Ezara, 460 B.C.E.
6. Paulo, 50-52 C.E.
7. Rehabiamu.—2 Mbiri 10:3-14.
8. Hagara.—Agalatiya 4:22-25.