Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Ndiziwerenga Chifukwa Chiyani? (May 2006) Ndili ndi zaka 15, ndipo nkhani imeneyi inandithandiza kwambiri. Magazini imeneyi nditapita nayo kusukulu, aphunzitsi anga anaiwerenga. Ndiyeno akuphunzitsa, ananena zimene tingachite kuti tizikonda kuwerenga, ndiponso anasonyeza Galamukani! imeneyi kwa ana onse m’kalasimo. Aphunzitsiwo anati anasangalala kwambiri kuwerenga nkhani za m’magaziniyi, ndipo analimbikitsa ana onse a m’kalasimo kuti awerenge magaziniyi.
D.A.C., Brazil
Masiku a m’mbuyomu, nthawi zambiri ndinkawerenga nkhani za m’magazini zimene ndinkaona kuti zikundisangalatsa basi. Koma tsopano ndimayesetsa kuwerenga nkhani iliyonse, ngakhale poyamba ingaoneke ngati yosasangalatsa kwenikweni. Ndipotu ndaona kuti pafupifupi nkhani zonse zimene zinkaoneka ngati zosasangalatsa, n’zimene zimandisangalatsa kwambiri. Zikomo kwambiri.
E. G., United States
Ndinasangalala kudziwa kuti masiku ano pali achinyamata amene akuchita zimene ine ndinkachita. Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 14, ndipo tsopano ndili zaka 40. Nditatsala pang’ono kubatizidwa, inenso ndinkakonda kuwerenga masamba angapo a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! tsiku lililonse. Chifukwa cha chizolowezi chimenechi, sindinaphonyepo kuwerenga nkhani ngakhale imodzi m’magazini ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndikhalebe wolimba mwauzimu.
S. O., Japan
Michael Servetus, Anafufuza Choonadi Yekhayekha (May 2006) Zikomo kwambiri chifukwa cholemba nkhani yotsegula m’masoyi. Inandilimbikitsa kwambiri kupitiriza kulalikira ndi kuyeretsa dzina la Yehova.
M. R., Brazil
Anthu ambiri amam’dziwa Servetus kuti anali katswiri pasayansi ya zamankhwala. Komabe, nkhani imeneyi yavumbula makhalidwe ena ochititsa chidwi a kadaulo ameneyu. Iye anali woona mtima komanso anafufuza choonadi mwakhama. Zikomo kwambiri chifukwa cholemba nkhani imeneyi.
M. J., Spain
Kumvera Machenjezo Kunawathandiza (June 2006) Kukhala m’gulu lachikondi la Yehova n’chinthu cha mtengo wapatali kwambiri! Ndikuyamikira kuchokera pansi pa mtima abale ndi alongo onse amene anatithandiza kukonzanso nyumba yathu, itasakazidwa ndi mphepo ya mkuntho ya Katrina. Nyumba imeneyi tsopano n’chizindikiro chooneka cha chikondi chawo.
I. F., United States
Silika, “Nsalu Yapamwamba Kwambiri” (June 2006) Kuyambira ndili mwana, ndakhala ndikudabwa kuti silika amapangidwa bwanji. Ndiyeno ndinasangalala kwambiri nditawerenga nkhani imeneyi mu Galamukani! Nkhani imeneyi inandisangalatsa kwabasi, ndipo yandithandiza kuti ndiziyamikira kwambiri chilengedwe cha Yehova.
A.C.L., Brazil
Zizindikiro Zikuluzikulu za Khansa Yapakhungu Yoopsa Kwambiri (June 8, 2005) Nditaona zithunzi za kalala za m’nkhani imeneyi, ndinatulukira kuti chiphuphu chakuda chimene chinali pa khungu langa chinali chizindikiro cha khansa yapakhungu yoopsa kwambiri. Mwamwayi, ndinachitidwa opaleshoni yochotsa khansayo chifukwa inali itangoyamba kumene. Ndikuthokoza Yehova kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha nkhani yothandizayi.
K. N., Japan