Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungu N’ngofunika Kwambiri Pamoyo

Mungu N’ngofunika Kwambiri Pamoyo

Mungu N’ngofunika Kwambiri Pamoyo

M’NYENGO inayake pachaka, yomwe zomera zambiri zimachita maluwa, njuchi zimakhala zili yakaliyakali ndipo mpweya wonse umakhala mungu wokhawokha. Matupi a anthu ena amadana ndi mungu, koma tisafulumire kunena kuti mungu n’ngwachabe. M’malo mwake tiyeni tiganizire kufunika kwake ndipotu tidabwa kuona kufunika kwa mungu pamoyo wathu.

Kodi mungu n’chiyani makamaka? Buku la Mtanthauziramawu wa Chinyanja limati, mungu kapena kuti chiku ndi “zinthu zachikasu zonga ufa, zokhala ku chingalangala chambewu zina monga chimanga kapena mchewere.” Kunena mwachidule, zomera zimapanga mungu kuti zizitha kubereka. Monga tikudziwira, pamafunika mwamuna ndi mkazi kuti mwana apangike. Chimodzimodzinso ndi zomera; kuti chipatso chipangike pamafunika kuti mungu uchoke ku mbali yaimuna ya duwa n’kufika ku mbali yaikazi. *

Tiufa ta mungu n’tating’ono kwambiri moti n’tosaoneka ndi maso. Koma n’zotheka kutiona ndi makina oonera tinthu ting’onoting’ono. Ndipo mungathe kuona kuti kukula kwake ndiponso kaumbidwe kake kamakhala kosiyanasiyana malingana ndi mtundu wa chomeracho. Mungu suwola, motero nthawi zambiri asayansi akapeza mungu wa kale kwambiri m’nthaka, amauunika bwinobwino kuti aone kusiyana kwake ndi mungu wa zomera zina. Choncho angathe kudziwa mbewu zimene anthu ankalima zaka zambirimbiri zapitazo. Kusiyanasiyana kwa mungu kumathandiza kwambiri kuti zomera zizindikire mungu wochokera ku zomera zamtundu womwewo.

Kayendedwe ka Mungu

Mbewu zambiri zimadalira mphepo kuti mungu utengedwe kuchoka ku zibalobalo zake. Pali mbewu zina zam’madzi zomwe zimadalira madziwo. Mitengo ndi zomera zina zimene zimadalira mphepo zimatulutsa mungu wankhaninkhani chifukwa choti njira imeneyi n’njosapanganika. * Anthu amene amadwala chimfine chifukwa cha mungu amavutika kwambiri panthawiyi.

Ngakhale kuti mitundu ina ya mitengo ndi udzu imadalira mphepo, zomera zina zimene sizimera zambiri pamalo amodzi zimafunikira njira ina yodalirika. Kodi mungu wa zomera zoterezi umayenda bwanji kuti ukafike ku zomera zinzake zomwe zili kutali kwambiri? Umatengedwa ndi mileme, mbalame, ndi tizilombo tosiyanasiyana, ndipotu iyi ndi njira yodalirika kwambiri. Komatu sikuti tizilomboti timangonyamula munguwu mwabule ayi.

Maluwawo amatilipira potipatsa timadzi totsekemera, tomwe tizilomboti timakonda kwambiri. Tikamamwa timadziti sitilephera kupakika mungu pa thupi lawo. Ndiye timati tikapita pa duwa lina timakasiyaponso mungu uja.

Tizilombo ting’onoting’ono n’timene timachita zimenezi, makamaka m’madera omwe si otentha kapena ozizira kwambiri. Tsiku lililonse tizilomboti timafika pa maluwa ambirimbiri n’kumamwa timadzi take ndi kudya mungu wake. * Pulofesa May Berenbaum anati: “N’kutheka kuti ntchito imene tizilomboti timachita imathandiza kwambiri kuti anthu akhale a thanzi labwino ndiponso osangalala. Komano anthu saganizira n’komwe ntchito imene tizilomboti timachita.” Nthawi zambiri mitengo ya zipatso imakhala ndi maluwa omwe amadalira mungu wochokera ku maluwa a mitengo ina kuti mitengoyo ibale zipatso zabwino. Motero, mungathe kuona kuti ntchito yoyendetsa mungu n’njofunika kwambiri pamoyo wathu.

Mmene Zomera Zimakopera Tizilombo

Maluwa amafunika kukopa tizilombo timene timagwira ntchito yoyendetsa mungu ndipo amafunikanso kutidyetsa. Kodi maluwa amachita bwanji zimenezi? Nthawi zina amatero popereka mthunzi woti tizilomboti tizibisalirapo dzuwa. Amaitaniranso timadzi ndi mungu wawowo pokhala ndi maonekedwe okopa ndiponso potulutsa kafungo kabwino. Komanso maluwa ambiri amakhala ndi madonthomadontho kapena mizeremizere yokongola yomwe imakopa ndiponso kulondolera tizilomboto pomwe pali timadzi totsekemera.

Maluwa amakopa tizilombo m’njira zosiyanasiyana. Ena amanunkha dala pofuna kukopa ntchentche. Ena amapusitsa tizilomboto pofuna kuti tiwanyamulireko mungu wawo. Mwachitsanzo, maluwa enaake amene amaoneka ngati njuchi yaikazi amapusitsa njuchi zazimuna kuti zizikopeka n’kumaterapo. Maluwa ena amatsekera tizilombo n’kutitulutsa pamene tamaliza ntchito yoyendetsa mungu m’duwalo. Katswiri wa zomera, Malcom Wilkins, anati: “Kayendedwe ka mungu kamachitika mwaluso ndiponso mwadongosolo zedi poyerekezera ndi zinthu zina zonse zimene zimachitika m’zomera.”

Mlengi anapanga zomera m’njira yoti zizikopa tizilombo tomwe timayendetsa mungu wawo. Iye akanapanda kutero sibwenzi zomerazi zikubala zipatso. Ponenapo za ntchito yodabwitsayi, Yesu anati: “Phunzirani ku maluwa akuthengo, mmene akukulira; sagwira ntchito, ndiponso sawomba nsalu; komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.”—Mateyo 6:25, 28, 29.

Chifukwa cha kuyenda kwa mungu m’maluwa ake, zomera zimatha kuberekana ndi kupanga chakudya chomwe chili chofunika pamoyo wathu. N’zoona kuti enafe timavutika ndi mungu, koma tonse tiyenera kuyamikira tizilombo tomwe timakhala yakaliyakali kuuyendetsa. Mungutu n’ngofunika kwambiri pamoyo wathu. Kayendedwe kodabwitsa ka mungu n’kofunika kwabasi kuti tizipeza zokolola zochuluka. Kayendedwe kameneka kamasonyeza luso logometsa la Mlengi wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Chomera chingathe kubala zipatso ndi mungu wochokera ku duwa la chomera china kapena mungu wochokera ku duwa lake lomwe. Komabe mbewu ya chomeracho imakhala yathanzi ndiponso yopirira ngati mungu wachokera ku duwa la chomera china.

^ ndime 6 Mwachitsanzo, mtengo wa msondodzi umakhala ndi tizibalobalo tambirimbiri ndipo chibalobalo chilichonse chimatha kutulutsa mungu wochuluka mosaneneka.

^ ndime 9 Kuti njuchi zipange uchi wokwana kilogalamu imodzi yokha, zimafunika kuyenda maulendo 10 miliyoni opita ku maluwa.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 16, 17]

Tizilombo Toyendetsa Mungu

MITUNDU INA YA NTCHENTCHE NDI ZIKUMBU

Tizilombo timeneti sitiyamikiridwa n’komwe pa ntchito yawo yaikulu yoyendetsa mungu. Ngati mumakonda kudya chokoleti, thokozani kantchentche kenakake kamene kamachita ntchito yofunika yoyendetsa mungu m’maluwa a mtengo wa zipatso zimene amapangira chokoleti.

MILEME NDI NYAMA ZINA ZANGATI MBEWA

Mitengo yambiri yaikuluikulu padziko lonse, monga mtengo wa mlambe, imadalira mileme pantchito yoyendetsa mungu m’maluwa awo. Pali mitundu ina ya mileme yokonda kupezeka m’mitengo yazipatso. Milemeyi imamwa timadzi ta m’maluwa a mitengoyo komanso imadya zipatso zake n’kumamwaza njere za zipatsozo. Pomwaza njerezi imathandizanso kuti mitengo ina imere. Ku Australia kuli nyama zina zangati mbewa zomwe zimamwa timadzi ta m’maluwa. Pomwa timadzito mungu umatsalira mu ubweya wawo motero umakafika pa duwa lililonse limene nyamazi zafikapo.

AGULUGUFE NDI AKADZIOTCHE

Chakudya chachikulu cha tizilombo tochititsa chidwiti ndi timadzi ta m’maluwa, ndipo mungu umakanirira pa matupi awo n’kumafalikira ku maluwa ena amene taulukirako. Pali maluwa enaake okongola amene amadalira akadziotche pankhani yoyendetsa mungu.

ACHOSO KAPENA ASODO

Mbalame zokongolazi zimangokhalira kuuluka m’maluwa osiyanasiyana, n’kumamwa timadzi take. Mungu umamatirira pa nthenga za m’mutu ndi za pachifuwa cha mbalamezi.

MITUNDU YOSIYANASIYANA YA NJUCHI NDI MAVU

Njuchi zimatenga mungu wambiri zedi chifukwa cha matupi awo aubweya. Motero njuchi zilibe mnzake pankhani ya kuyendetsa mungu. Mwachitsanzo, bemberezi mmodzi yekha amatha kutenga mungu wochuluka mosaneneka. Ku New Zealand kuli minda yambiri ya mtundu winawake wa khobwe chifukwa choti anapititsako abemberezi kuchokera ku England m’zaka za m’ma 1800. Khobweyu amathandiza kwambiri podyetsera ziweto za m’dzikoli.

Padziko lonse lapansi palibe kachilombo kamene kangapikisane ndi njuchi pankhani yoyendetsa mungu. Njuchi zimakonda kupita pa maluwa a zomera za mtundu umodzi umene wamera kwambiri pafupi ndi chisa chawo. Katswiri wa maphunziro a tizilombo, Christopher O’Toole anati, “chakudya chathu chochuluka chimadalira ntchito yoyendetsa mungu imene njuchi zimachita.” Pamafunika njuchi kuti ziyendetse mungu m’maluwa a mbewu monga katungulume, mitengo ina yangati mapichesi, ndi mitengo ina yosiyanasiyana. M’madera ena alimi amalipira anthu oweta njuchi chifukwa cha thandizo limene njuchi zawozo zimapereka.

[Chithunzi patsamba 18]

Duwa lokhala ngati njuchi