Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thanthwe Lochititsa Chidwi

Thanthwe Lochititsa Chidwi

Thanthwe Lochititsa Chidwi

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CANADA

KUMADZULO kwenikweni komwenso n’kumapeto kwa chilumba cha Gaspé Peninsula, chomwe chili ku Gulf of St. Lawrence, kuli thanthwe lalikulu kwambiri lotchedwa Percé Rock. Thanthweli limaoneka pa madzi a buluu a nyanja yamchere ya Atlantic. Ndipotu ndi lalikulu pafupifupi mamita 430 m’litali, mamita 90 m’lifupi, ndiponso mamita 88 kupita m’mwamba. Kwa zaka zambiri, asodzi ndiponso anthu oyenda pa nyanja akhala akugwiritsa ntchito thanthwe limeneli monga chizindikiro chodalirika chowathandiza kuti asasochere. Lakhalanso likutchulidwa mu nyimbo, m’ndakatulo, m’nkhani zolembedwa, ndiponso ena amalijambula pa zithunzi za pamanja. Buku lina linati, thanthweli “simungalimvetsetse bwino ndiponso n’lodabwitsa kwambiri.”

Panthawi inayake, anthu olimba mtima a kudera limeneli ankakwera mphepete mwa thanthweli ndi kukachotsa mazira a mbalame m’zisa. Choncho, boma la Quebec linafuna kuteteza thanthweli komanso mbalame zimene zimakhala pa thanthweli. Ndiyeno mu 1985, linalengeza kuti tsopano thanthweli, pamodzi ndi chilumba chomwe chaliyandikira chotchedwa Bonaventure, ndi malo a mbalame otetezedwa ndi boma. Ndipotu chilumba cha Bonaventure ndi malo achiwiri pamalo aakulu kwambiri padziko lonse amene mbalame zinazake za kunyanja zimaswaniranako.

Anthu ena amati kalekalelo, thanthwe la Percé Rock linali lofika kumtunda ndipo mwina linali ndi makoma anayi ooneka ngati zipilala ochilikiza thanthweli. Koma masiku ano, ndi khoma limodzi lokha lomwe lilipo. Khomali n’lotambalala kuposa mamita 30 chakumapeto kwake, kumbali yoloza kunyanja osati ku mtunda. Madzi akatsika chifukwa cha mafunde, mulu wa mchenga umene walumikiza thanthweli ndi mtunda, umaonekera. Pamaola anayi aliwonse omwe madzi amatsika, anthu olimba mtima amatha kuyenda pa mulu wamchengawu n’kukafika m’munsi mwa thanthweli. Ndiyeno amayendanso movutikira kwambiri kwa mphindi 15, kuti akafike pa khoma lokhala ngati chipilala cha thanthweli.

Alendo odzaona malo amene amafika pa thanthweli ayenera kusamala. Munthu wina wodzaona malowa, amene anachita kukwawa pa miyala kuti akafike pa chiboo chomwe chili pakhoma la thanthweli anati: “Pakangodutsa kanthawi pang’ono, mumangomva kuti ‘khovoo!’ mkokomo wa miyala ikamagwera m’madzi ngati mabomba. Ndipo miyala ina imagwera pa inzake, n’kumamveka ngati mfuti.”

Monga mmene alendo ambiri anaonera, thanthwe la Percé Rock n’lokongola mochititsa chidwi. Komabe, thanthweli ndi chitsanzo chimodzi chabe cha zinthu zokongola ndi zochititsa chidwi za padziko lapansi. Palitu zinthu zambiri ndiponso zosiyanasiyana! Mukaona zinthu zimenezi, mwina inunso mumachita chidwi ndi ‘kulingalira zodabwitsa za Mulungu.’—Yobu 37:14.

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

© Mike Grandmaison Photography