Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Zaka zoposa khumi zapitazi, alimi a Chitchaina oposa 40 miliyoni alibenso minda chifukwa cha matauni amene akukula kwambiri komanso mofulumira.—ZACHOKERA MU NYUZIPEPALA YA CHINA DAILY, KU CHINA.
▪ Padziko lonse lapansi m’chaka cha 2005, kunachitika nkhondo zikuluzikulu zokwana 28, ndiponso nkhondo zing’onozing’ono zokwana 11.—ZACHOKERA MU VITAL SIGNS 2006-2007, KU BUNGWE LA WORLDWATCH INSTITUTE.
▪ Akatswiri a bungwe la za luso lamakono la zopangapanga lotchedwa Tokyo Institute of Technology apanga kandege koyendetsedwa ndi munthu kopepuka kwambiri, kosakwana makilogalamu 55, koyendera mabatire a wailesi. Kandegeka kanauluka ulendo wokwana mamita 391 mu masekondi 59 okha.—ZACHOKERA MU NYUZIPEPALA YA MAINICHI DAILY NEWS, KU JAPAN.
▪ Ena mwa anthu a zaka zoyambira 12 mpaka 20 a ku Holland, amene amagwiritsa ntchito Intaneti, amatsegula malo enaake pa Intanetipo pamene anthu amatha kutumizapo nkhani zokhuza moyo wawo ndiponso zithunzi zawo. Atatsegula malo amenewa, “anyamata 40 pa 100 aliwonse ndi atsikana 57 pa 100 aliwonse anauzidwapo kuti avule zovala zawo zonse kapena kuti achite zinthu zina zosonyeza kugonana. Zinthu zomwe anauzidwazi zingajambulidwe ndi makamera olumikizidwa ku kompyuta amene amatumiza zithunzizo pa Intaneti.”—ZACHOKERA MU NYUZIPEPALA YA RUTGERS NISSO GROEP, NETHERLANDS.
Kodi Mungakodwe ndi Masewera a Pakompyuta?
“Ubongo wa anthu amene amasewera kwambiri masewera a pakompyuta, umakhudzidwa mofanana ndi wa anthu amene amamwa kwambiri mowa kapena mankhwala osokoneza bongo.” Anatero katswiri wa zamaganizo Ralf Thalemann, yemwe ndi mtsogoleri wa gulu lofufuza za mmene anthu amakodwera ndi zinthu zosiyanasiyana, yemwenso ndi wa pachipatala cha payunivesite inayake yotchedwa Charité, mu mzinda wa Berlin, ku Germany. Zikuoneka kuti kusewera kwambiri masewera a pakompyuta kumachititsa kuti timadzi tinatake timene timatuluka mu ubongo tiwonjezereke. Timadzi timeneti, timapangitsa munthu kuona kuti akusangalala kwambiri, ndipo m’kupita kwa nthawi, munthuyo “amakodwa” ndi masewerawa. Kafukufuku wina anasonyeza kuti zimenezi zingachitike kwa anthu 10 pa anthu 100 aliwonse omwe amachita masewera a pakompyuta.
Anthu Olemera “N’ngosatetezeka Ndiponso Amada Nkhawa”
“Anthu olemera kwambiri amaona kuti n’ngosatetezeka ndiponso amada nkhawa,” inatero nyuzipepala yotchedwa China Daily, ya mumzinda wa Beijing. Ku East China ndi South China, kunachitika kafukufuku wofufuza anthu amene chuma chawo n’chokwana madola 275 miliyoni. Anafufuza za mmene anthu olemera “amaonera kupembedza, ukwati, moyo, ntchito ndiponso ndalama.” Ndipo anapeza kuti “ambiri amakonda ndalama, komanso panthawi imodzimodziyo amadana nazo.” Ena mwa anthu amene anafunsidwa pa kafukufukuyu ananena kuti, ngakhale kuti timalemekezeka ndiponso timaona kuti zinthu zikutiyendera, “nthawi zambiri timakhumudwa chifukwa cha ndalamazi.”
Kulima kumathandiza Anthu Odwala Matenda a Maganizo
Posachedwapa, akatswiri oposa 100 ochokera m’mayiko 14 anakumana mu mzinda wa Stavanger, m’dziko la Norway, kuti aphunzire za mmene ntchito yolima imathandizira thanzi la munthu. Maphunziro amenewa anaphatikizapo zaulimi, zophunzitsa, ndi zaumoyo. Malinga ndi zimene wailesi ya ku Norway inanena, ena mwa anthu amene adwala matenda a maganizo kwa nthawi yaitali amakhala bwino akamagwira ntchito ya kumunda, moti safunikanso kupita nawo kuchipatala. Ntchito yolima imathandiza maganizo ndiponso thupi la munthu. Mafamu ang’onoang’ono oposa 600 a ku Norway ayamba kugwiritsa ntchito maphunzirowa, ndipo akupeza ndalama zochuluka kwambiri.
Ntchito ya Nsanja Zosongoka za Matchalitchi Yapezeka
“Matchalitchi a New England [ku United States] apeza njira yothetsera mavuto awo a zachuma. Matchalitchiwa akuchititsa lendi nsanja zawo zosongoka kuti zizigwiritsidwa ntchito ndi makampani a mafoni a m’manja,” inatero magazini ya Newsweek. Malo oikamo zipangizo zotumiza ndi kulandira mauthenga a m’mafoni a m’manja akusowa chifukwa cha malamulo a boma okhudza malo omwe anthu amakhalako. Ndipo anthu safuna kukhala pafupi ndi zipangizo za makampani a mafoni a m’manjawa. Ndiyeno makampaniwa akuika zipangizo zawozi m’kati mwa nsanja zosongoka za matchalitchi. Mkulu wa bungwe lolangiza matchalitchi pankhani za malonda anati: “Tchalitchi choyamba chimene chinaikidwa zipangizozi, tsopano chikugwiritsidwa ntchito ndi makampani atatu. Ndipotu tchalitchichi chimapeza ndalama zokwana madola 74,000 pachaka, pochititsa lendi nsanja zimene sizinkagwira ntchito n’komwe.”