Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Analemberatu Tsogolo Lanu?

Kodi Mulungu Analemberatu Tsogolo Lanu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Analemberatu Tsogolo Lanu?

Tsiku lina m’mawa munthu wina ndi mnzake akupita kuntchito pagalimoto anaganiza zodzera njira yachidule ya kumene mnzakeyo ankakhala poyamba. Ali m’njira anaona moto ukuyaka m’kati mwa nyumba inayake, ndipo malawi ake ankachita kutulukira pawindo. Iwo anaimitsa galimotoyo n’kutulutsamo makwerero, ndipo anakwera nyumbayo n’kupulumutsa mayi ndi ana asanu. Ponena za ngoziyi, nyuzi ina inati: “Mwina Mulungu analemberatu kuti zidzatero.”

ANTHU ambiri amaganiza kuti chilichonse chimene chimawachitikira, kaya n’chabwino kaya n’choipa, chinakonzedwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, John Calvin, yemwe anatsogolera anthu pogalukira tchalitchi cha Katolika m’ma 1500, analemba kuti: “Tikati Mulungu anakonzeratu tsogolo la munthu aliyense timatanthauza kuti analemberatu cholinga chimene ali nacho ndi munthu aliyense. Chifukwatu Mulungu sanalenge anthu onse ndi cholinga chofanana. Anakonzeratu zoti ena adzalandire moyo wosatha ndipo ena chilango chosatha.”

Kodi n’zoonadi kuti Mulungu analemberatu zochita zathu ndiponso tsogolo lathu lonse? Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pankhaniyi?

Maganizowa N’ngosamveka

Ena amene amakhulupirira zimenezi amaganiza kuti: Mulungu amadziwa zonse, ngakhale zam’tsogolo. Motero amadziwa zimene munthu aliyense adzachite pamoyo wake ndipo amadziwiratunso nthawi yeniyeni imene aliyense adzafere ndi chimene chidzamuphe. Motero iwo amaganiza kuti munthu akafuna kuchita chinachake, amachichita mogwirizana ndi mmene Mulungu anaonera kale ndi mmenenso anakonzera kale. Iwowa amati poti Mulungu amadziwa zonse ndiye kuti sangalephere kudziwa zimenezi. Koma kodi inuyo mukuona kuti maganizo amenewa n’ngomveka? Taganizirani tanthauzo la mfundoyi ngati itakhala yoona.

Ngati Mulungu anakonza kale tsogolo lanu, ndiye kuti ngati mukuyesetsa kudzisamalira mukungodzivutitsa. Komanso ndiye kuti zinthu monga kusuta fodya kapena kusasuta sikungasinthe chilichonse pa thanzi lanu kapena la ana anu. Kumanga lamba mukakwera galimoto sikungakuthandizeni m’njira iliyonse kuti mukhale otetezeka. Komatu maganizo oterewa n’ngolakwika. Pali umboni wosonyeza kuti anthu amene amachita zinthu mosamala samafa kawirikawiri chifukwa cha ngozi. Kuchita zinthu mosasamala kungakuikeni pangozi yaikulu.

Taganiziraninso mfundo ina iyi. Ngati Mulungu akanasankha kuti azidziwa chilichonse, ndiye kuti akanadziwiratu kuti Adamu ndi Hava sadzamumvera. Ndipo akanadziwa zimenezi asanawalenge n’komwe. Koma pamene Mulungu anali kuchenjeza Adamu kuti asadye zipatso za “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa” kodi Mulunguyo anali atadziwiratu kuti Adamu adzadya zipatso za mtengowo? (Genesis 2:16, 17) Pamene Mulungu anali kuuza Adamu ndi Hava kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi,” kodi ankadziwiratu kuti chiyembekezo chosangalatsa cha anthuwa chodzakhala m’paradaiso chidzalephereka? Ayi sankadziwa.—Genesis 1:28.

Tikaitsata bwinobwino mfundo yakuti Mulungu amadziwiratu zinthu zonse zimene tidzachite, timafika pa mfundo yakuti Mulunguyo ndiye amachititsa chilichonse, kaya nkhondo, kuponderezana, ndiponso kuvutika. Koma kodi n’zoona kuti Mulungu angatero? Zimene Mulungu amanena zokhudza iye mwini zimayankha funso limeneli momveka bwino.

“Sankhani”

Malemba amanena kuti “Mulungu ndiye chikondi” ndiponso kuti “akonda chiweruzo.” Iye nthawi zonse wakhala akulimbikitsa anthu ake kuti: “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma.” (1 Yohane 4:8; Salmo 37:28; Amosi 5:15) Nthawi zambirimbiri iye wakhala akulimbikitsa anthu ake okhulupirika kuti asankhe kuchita zabwino. Mwachitsanzo, Yehova atachita pangano ndi mtundu wa Isiraeli, anauza mtunduwo kudzera mwa Mose kuti: “Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu.” (Deuteronomo 30:19) Kodi Mulungu anakonzeratu pasadakhale zinthu zonse zimene mtunduwu udzasankhe kuchita? Umboni umasonyeza kuti sanatero ayi.

Yoswa, yemwe anali mtsogoleri wa anthu a Mulungu kalelo, analimbikitsa anthu amtundu wake kuti: “Mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira . . . Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” (Yoswa 24:15) Nayenso mneneri Yeremiya ananena kuti: “Mveranitu mawu a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.” (Yeremiya 38:20) Kodi Mulungu wachilungamo ndi wachikondi angalimbikitse anthu kuchita zabwino pofuna kudzalandira madalitso, koma kwinaku akudziwa kale kuti anakonzeratu zoti anthuwo adzalephere? Ayi ndithu. Atatero ndiye kutitu akungofuna kuwapusitsa anthuwo.

Motero zinthu zabwino kapena zoipa zimene mumakumana nazo pamoyo wanu, si zolembedweratu. Nthawi zambiri, zinthu ‘zimene zimangotigwera’ zimachitika chifukwa cha zochita za anthu ena, kaya zanzeru kapena zopanda nzeru. (Mlaliki 9:11) Inde, Mulungu sanakonzeretu kapena kulemberatu tsogolo lanu, ndipotu zimene mumasankha panopo n’zimene zingachititse kuti mudzakhale ndi moyo wosatha kapena ayi.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Mulungu anali atakonzeratu zoti Adamu ndi Hava adzachimwe?—Genesis 1:28; 2:16, 17.

▪ Kodi ndi makhalidwe otani a Mulungu amene amasonyeza kuti sangalemberetu tsogolo lathu?—Salmo 37:28; 1 Yohane 4:8.

▪ Kodi inuyo muli ndi udindo wotani?—Yoswa 24:15.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Pali umboni wosonyeza kuti anthu amene amachita zinthu mosamala, kawirikawiri safa chifukwa cha ngozi