Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungadye Mbozi?

Kodi Mungadye Mbozi?

Kodi Mungadye Mbozi?

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU ZAMBIA

ANTHU ena amati sangadye mbozi. Koma ena ambiri amakonda kudya takudya tankhuli timeneti topanda ndi fupa lomwe. Ndiwo za m’gulu limeneli, zimene ambiri amakonda m’madera ena a mu Africa ndi malasankhuli, kapena kuti zinkhuwala, zimene zimasanduka mtundu wina wa gulugufe wotchedwa zifukufuku. M’madera amenewa, zimapezeka kwambiri mumtengo wa chitimbe umene ena amati msekese. Kumidzi, anthu ambiri amadikirira ndi chidwi nyengo yotola tindiwo tophiriphithaphiriphitha timeneti, tokhetsa dovu komanso topatsa thanzi. Keith Leggett, wa bungwe losamalira zachilengedwe la Kalahari Conservation Society, anati: “Mungandabwe kudziwa kuti chakudya chimenechi ndi chomanga thupi kwambiri.” Mbozi zimenezi zimathandizanso kuti nthaka ikhale yachonde ndi kuteteza chilengedwe kumadera amene amakhala ouma ndi opanda chonde.

Mvula ikayamba kugwa kum’mwera kwa Africa cha kumayambiriro kwa November, zomera zimaphukira ndipo kumakhala tizilombo tambirimbiri. Mbozi mamiliyoni ambiri zimene zili m’nthaka zimasanduka zikufukufu zokongola. Pakapita milungu ingapo yokha, ana awo amachoka pa dzira kukhala mbozi, kenako kukhala malasankhuli okongola ndi onenepa ngati masoseji.

Kumadera kumene chakudya chachikulu ndi chinangwa, nsima, ndi zina zotero, malasankhuli amakhala ndiwo zabwino kwambiri ndipo amathandiza kuti chakudya chikhale chomanga thupi. Ngakhale kuti enafe malasankhuli si ndiwo zathu zapamtima, ndi ofunikabe kwambiri makamaka kumadera kumene zakudya zabwino zomanga thupi n’zodula kapena zosowa. Malasankhuli amapikisana ndi nyama kapena nsomba chifukwa amakhala ndi pafupifupi magawo atatu a magawo anayi a chakudya chomanga thupi ndi choteteza matenda, chimene munthu wamkulu amafunikira tsiku lililonse. Tindiwo timeneti ndi topatsadi thanzi!

Anthu amene amadya malasankhuli samvetsa chifukwa chake alimi a kumadera ena amalimbana ndi kupha tizilombo topatsa thanzi timeneti ndi mankhwala odula. Tizilombo timeneti timadya masamba osadyedwa mwinanso akupha, ndi kuwasandutsa chakudya chofunika kwambiri. Tizilomboti timachita zonsezi popanda zida zaulimi kapena kuitanitsa avetenale. Pokhala amatola ndi manja, malasankhuli ndi chakudya chosavuta kukolola.

Malasankhuli amathandizanso kwambiri kuti nthaka ikhale yachonde ndi kuteteza zachilengedwe. Ngakhale kuti njovu ndi zazikulu ndiponso zimadya kwambiri, malasankhuli amadya ndi kugaya chakudya chambiri kuziposa. Pamoyo wawo waufupi wa milungu 6, malasankhuli miyandamiyanda amadya chakudya chambiri kuwirikiza ka 10 kuposa njovu ndiponso amatulutsa ndowe zambiri kuwirikiza kanayi kuposa njovu zonse m’dera lomwelo. M’pake kuti panyengo yonseyi thupi la malasankhuli limakula kuwirikiza ka 4,000! Choncho, ndi zomveka kuti anthu akamatola malasankhuli mopitirira muyeso, nthaka imaguga ndipo chilengedwe chimasokonekera.

Kodi ntchito yotola malasankhuli imakhala yotani? Nthawi ya mvula iliyonse m’madera akumidzi, akazi amapita kokatola malasankhuli. Zimenezi zimachitika kawiri pachaka. Amagwira ntchito yotolayi kwa milungu ingapo. Akawatola, amawafinya, kuwawiritsa, ndi kuwayanika. Komabe, malasankhuli ena amafuna kusamala. Ubweya kapena minga imene malasankhuli ena ali nayo amachotsa. Pokonza, m’pofunikanso kusamala chifukwa malasankhuli ena amadya zomera zakupha. Akakonzedwa, munthu amatha kukhwasula ouma, ngakhale kuti nthawi zambiri amawaviika m’madzi ndi kuwawiritsa kapena kuwakazinga ndi tomato ndi anyezi.

Mukamva za malasankhuli, mwina mungalakalake mutalawa nawo zakudya zachilendo zimenezi kapena mungachite mseru. Atakupatsani, mwina mungafune kuwazemba. Koma musaiwale kuti malasankhuliwa ndi chakudya chabwino chomanga thupi ndipo amathandiza mabanja ambiri mu Africa kupeza ndalama.

[Chithunzi patsamba 26]

Malasankhuli ndi chakudya chabwino kwambiri chomanga thupi

[Chithunzi patsamba 27]

Pamoyo wake waufupi wa milungu 6, thupi la malasankhuli limakula kuwirikiza ka 4,000