Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munthu Ameneyu ndi Woyenera Kumanga Naye Banja?

Kodi Munthu Ameneyu ndi Woyenera Kumanga Naye Banja?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Munthu Ameneyu ndi Woyenera Kumanga Naye Banja?

Yankhani mafunso otsatirawa:

Kodi ndi zinthu ndi makhalidwe ati amene mukufuna kuti munthu womanga naye banja akhale nawo? Pa zimene zili pamunsipa, chongani chonchi ✔ zinthu zinayi zimene mukuona kuti n’zofunika kwambiri.

․․․․․ wokongola

․․․․․ wokonda zauzimu

․․․․․ wochezeka

․․․․․ wokhulupirika

․․․․․ wotchuka

․․․․․ wakhalidwe

․․․․․ wanthabwala

․․․․․ woganizira m’tsogolo

Muli wamng’ono, kodi munakopekapo ndi munthu wina? Pa zimene zili pamwambapa, chongani chonchi X chinthu chimodzi chimene chinakukopani kwambiri panthawi imeneyo.

PAZINTHU zili pamwambazi, palibe chinthu chimene chili cholakwika. Chilichonse chili ndi ubwino wake. Komabe, kodi simukuvomereza kuti achinyamata akakopeka ndi munthu, amatengeka kwambiri ndi zinthu zosafunika kwenikweni ngati zimene zili kumanzerezo?

Koma munthu akamakula, amayamba kukhala ndi nzeru ndipo amazindikira makhalidwe ofunika kwambiri ngati amene ali kumanjawo. Mwachitsanzo, amazindikira kuti mtsikana wokongola kwambiri atha kukhala wosakhulupirika kapena mnyamata wotchuka kwambiri m’kalasi atha kukhala wopanda khalidwe. Ngati munthu “wapitirira pachimake pa unyamata,” kapena kuti nthawi imene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu, amayamba kuganiza kwambiri za makhalidwe ofunika poyankha funso lakuti, Kodi munthu ameneyu ndi woyenera kumanga naye banja?—1 Akorinto 7:36.

Kodi Aliyense Ndi Wondiyenerera?

M’kupita kwa nthawi, mwina mungakhale ndi chidwi ndi anthu angapo. Koma sikuti onsewo angakhale oyenerera. Nanga simukufuna munthu amene mudzakhale naye moyo wanu wonse, amene muzidzalimbikitsana naye kuchita zinthu zabwino. (Mateyo 19:4-6) Kodi munthu ameneyo mungam’peze bwanji? Musanayankhe funso limeneli, ‘mudziyang’ane kaye pakalilole’ ndi kudzifufuza bwinobwino.—Yakobe 1:23-25.

Kuti mudzidziwe bwino, yankhani mafunso otsatirawa:

Kodi ndili ndi makhalidwe abwino otani?

․․․․․

Kodi ndi zinthu ziti zimene sindichita bwino?

․․․․․

Kodi ndimafunika kulimbikitsidwa pa zinthu zotani?

․․․․․

Kudzidziwa nokha si nkhani yophweka ayi, koma mafunso ngati amenewa angakuthandizeni. * Mukadzidziwa bwino, ndi pamene mungapeze munthu wokuthandizani kuchita zinthu zabwino. Koma ngati mukuona kuti mwapeza munthu womanga naye banja, kodi mungatsimikizire bwanji kuti ndi wokuyenererani?

Kodi Chibwenzi Chimenechi Chipitirira?

Kuti muyankhe funso limeneli, yang’anani mnzanuyo bwinobwino. Koma musamale, chifukwa mutha kunyengeka ndi kungoona zimene mukufuna kuona. Musapupulume! Yesetsani kuona khalidwe lake lenileni.

Anthu ambiri akakhala pa chibwenzi, safufuzana kwambiri. Amangotengeka ndi zinthu zimene onse amakonda. Amati ‘Timakonda nyimbo zofanana.’ ‘Timakonda kuchita zinthu zofanana.’ ‘Timagwirizana pa chilichonse!’ Monga tanenera kale, ngati mwapitiriradi pa chimake cha unyamata, simuona zimenezi zokha, koma mumaganizira kwambiri za makhalidwe ofunika. Mumaona “munthu wa mkati, wa mu mtima.”—1 Petulo 3:4; Aefeso 3:16.

Mwachitsanzo, ngati mukufuna kudziwa zambiri za munthuyo, zingathandize kuona mmene amachitira pamene simukugwirizana pa chinachake m’malo mongoyang’ana pa zimene mumagwirizana. Kunena kwina, mungafune kudziwa kuti kodi munthuyo amatani ngati simukugwirizana. Kodi amangoumirira zake zokha mpaka ‘kupsa mtima’ kapena kulankhula “mawu achipongwe”? (Agalatiya 5:19, 20; Akolose 3:8) Kapena kodi munthuyo amalolera pofuna kuti pakhale mtendere, malinga ngati sakuswa malamulo?—Yakobe 3:17.

Mfundo inanso yofunika kuganizira ndi yakuti: Kodi munthuyo amakonda kulamula kapena ndi wansanje? Kodi amafuna kuti muzimuuza chilichonse chimene mukuchita kapena kulikonse kumene mukupita? Mtsikana wina dzina lake Nicole anati: “Muzisamala ndi munthu wansanje ndi wokonda kulamula. Ndamvapo za anthu akukangana ali pa chibwenzi chifukwa wina sanauze mnzake kumene akupita kapena kumene ali. Ndikuganiza kuti zikamatere, ndiye kuti pali vuto lalikulu.”

Kodi munthu amene muli naye pachibwenzi anthu amamuona bwanji? Mungachite bwino kufunsa anthu odalirika mumpingo wake, amene amudziwa munthuyo kwa nthawi yaitali. Anthuwo adzakuthandizani kudziwa ngati munthuyo ali ndi “umboni wabwino.”—Machitidwe 16:1, 2. *

Kodi Mukufunika Kuthetsa Chibwenzi?

Nanga bwanji ngati munthu amene muli naye pachibwenzi akuoneka kuti sangakhale mwamuna kapena mkazi wabwino? Ngati zili choncho, mungachite bwino kuthetsa chibwenzicho. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.”—Miyambo 22:3. *

Patapita nthawi, mwina mungapeze chibwenzi china. Zikatero, mudzatha kuona zinthu bwinobwino chifukwa chakuti mwaphunzira. Mwina mwake nthawi imeneyo, mukadzadzifunsa kuti “Kodi munthu ameneyu ndi woyenera kumanga naye banja?” mudzayankha kuti inde!

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Kuti mupeze mafunso ena odzifunsa, onani Galamukani! ya January 2007, tsamba 30.

^ ndime 31 Onaninso mafunso amene ali mu mabokosi pamasamba 19 ndi 20.

^ ndime 33 Kuti mudziwe zambiri pankhani yothetsa chibwenzi, onani Galamukani! ya April 8, 2001, masamba 28 mpaka 30.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi muli ndi makhalidwe abwino ati amene angakhale othandiza muukwati?

▪ Kodi ndi makhalidwe ati amene mungakonde kuti mnzanu akhale nawo?

▪ Kodi mungatani kuti mudziwe zambiri za khalidwe ndi mbiri ya munthu amene muli naye pachibwenzi?

[Bokosi patsamba 19]

Kodi munthu ameneyu angakhale mwamuna wabwino?

ZINTHU ZOFUNIKA

Kodi amatani ngati ali ndi udindo?—Mateyo 20:25, 26.

Kodi ali ndi zolinga zotani m’tsogolo?—1 Timoteyo 4:15.

Kodi akuchita zotani kuti akwaniritse zolingazo?—1 Akorinto 9:26, 27.

Kodi anzake ndi otani?—Miyambo 13:20.

Kodi maganizo ake ndi otani pankhani ya ndalama?—Aheberi 13:5, 6.

Kodi amakonda kusangalala ndi zinthu zotani?—Salmo 97:10.

Kodi kavalidwe kake kamasonyeza chiyani za iyeyo?—2 Akorinto 6:3.

Kodi amasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova?—1 Yohane 5:3.

ZINTHU ZINANSO ZOFUNIKA

Kodi ndi wolimbikira ntchito?—Miyambo 6:9-11.

Kodi amadziwa kugwiritsa ntchito bwino ndalama?—Luka 14:28.

Kodi ali ndi mbiri yabwino?—Machitidwe 16:1, 2.

Kodi amalemekeza makolo ake?—Eksodo 20:12.

Kodi ndi munthu woganizira ena?—Afilipi 2:4.

ZINTHU ZOTI MUSAMALE NAZO

Kodi ndi wokonda kupsa mtima?—Miyambo 22:24.

Kodi amakuumirizani kuchita zinthu zosayenera zokhudza kugonana?—Agalatiya 5:19.

Kodi ndi wolalata kapena wandewu?—Aefeso 4:31.

Kodi amaona kuti sangasangalale akapanda kumwa mowa?—Miyambo 20:1.

Kodi ndi wansanje ndi wodzikonda?—1 Akorinto 13:4, 5.

[Bokosi patsamba 20]

Kodi munthu ameneyu angakhale mkazi wabwino?

ZINTHU ZOFUNIKA

Kodi amasonyeza bwanji kugonjera m’banja ndi mumpingo wake?—Aefeso 5:21, 22.

Kodi kavalidwe kake kamasonyeza chiyani za iyeyo?—1 Petulo 3:3, 4.

Kodi anzake ndi otani?—Miyambo 13:20.

Kodi maganizo ake ndi otani pankhani ya ndalama?—1 Yohane 2:15-17.

Kodi ali ndi zolinga zotani m’tsogolo?—1 Timoteyo 4:15.

Kodi akuchita zotani kuti akwaniritse zolingazo?—1 Akorinto 9:26, 27.

Kodi amakonda kusangalala ndi zinthu zotani?—Salmo 97:10.

Kodi amasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova?—1 Yohane 5:3.

ZINTHU ZINANSO ZOFUNIKA

Kodi ndi wolimbikira ntchito?—Miyambo 31:17, 19, 21, 22, 27.

Kodi amadziwa kugwiritsa ntchito bwino ndalama?—Miyambo 31:16, 18.

Kodi ali ndi mbiri yabwino?—Rute 4:11.

Kodi amalemekeza makolo ake?—Eksodo 20:12.

Kodi ndi munthu woganizira ena?—Miyambo 31:20.

ZINTHU ZOTI MUSAMALE NAZO

Kodi ndi mkazi wolongolola?—Miyambo 21:19.

Kodi amakuumirizani kuchita zinthu zosayenera zokhudza kugonana?—Agalatiya 5:19.

Kodi ndi wolalata kapena wandewu?—Aefeso 4:31.

Kodi amaona kuti sangasangalale akapanda kumwa mowa?—Miyambo 20:1.

Kodi ndi wansanje ndi wodzikonda?—1 Akorinto 13:4, 5.