Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Osauka Angayembekezere Zotani?

Kodi Osauka Angayembekezere Zotani?

Kodi Osauka Angayembekezere Zotani?

PALIBE vuto lililonse ndi kugwira ntchito mwakhama ngati malipiro ake ali ogwirizana ndi ntchitoyo. Taonani zimene wolemba Baibulo wina ananena pankhaniyi: ‘Ndidziwa kuti palibe chabwino, koma kukondwa ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.’—Mlaliki 3:12, 13.

Koma monga taonera, padzikoli anthu amawagwiritsa ntchito yakalavulagaga koma n’kumawapatsa malipiro ochepa. Ambiri akungovutikabe ndi umphawi tsiku ndi tsiku. Kawirikawiri ‘sakondwa’ ndiponso ‘saona zabwino’ chifukwa cha mmene akukhalira pa moyo wawo. Panopo dzikoli lili ndi chuma chankhaninkhani koma n’kutheka kuti theka la anthu onse padzikoli silikudyerera nawo chumachi.

Mulungu Amaganizira Anthu Osauka

Mlengi wathu Yehova Mulungu, sasangalala ndi zimene zikuchitika pa dzikozi. Yehova amachitira chifundo anthu osauka. Baibulo limati: “[Mulungu] saiwala kulira kwa ozunzika.” (Salmo 9:12) Yehova ndi Mulungu woganizira osauka.

Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Waumphawi adzipereka kwa inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.” (Salmo 10:14) Taonani kuti vesi limeneli likutchula za anthu ovutikawo pawokhapawokha. * Inde, Mulungu amaona munthu aliyense payekha kuti amuthandize pa zosowa zake. Kwa Mulungu, munthu aliyense payekha n’ngofunika ndipo n’ngoyenera kum’ganizira. Yehova amalimbikitsa anthu osiyanasiyana, osauka ndi olemera omwe, kuti aphunzire kwa iyeyo ndi kukhala mabwenzi ake.

Chinthu chimodzi chimene anthu amaphunzira kwa Mulungu ndicho kusonyeza chifundo ndi kuganizira ena. Amboni za Yehova onse amaonana ngati banja limodzi lalikulu lauzimu. Amaganizirana kwambiri, ndipo amakondana kwambiri monga Akhristu. Panthawi ina Mbuye wathu Yesu Khristu anauza om’tsatira kuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mateyo 23:8) Motero anthu onse amene amapembedza m’njira yoona amakhala mbali ya abale amene sasankhana chifukwa cha umphawi. Amasamalirana ndipo amalimbikitsana pa nthawi yamavuto.

Baibulo lili ndi mfundo zimene zingathandize kuchepetsa mavuto obwera chifukwa cha umphawi. Malemba amasonyeza kuti Mulungu amaletsa kuipitsa thupi, monga posuta fodya ndi kumwa mowa mwauchidakwa. (Miyambo 20:1; 2 Akorinto 7:1) Munthu amene amatsatira mfundo zimenezi pamoyo wake amasunga bwino ndalama zimene akanawonongera pa makhalidwe oipawa. Amapewa matenda obwera chifukwa cha kusuta ndi uchidakwa motero sawonongera ndalama kuchipatala. Baibulo limaphunzitsanso anthu kupewa kukonda chuma ndiponso umbombo. (Maliko 4:19; Aefeso 5:3) Munthu amene amamvera Mawu a Mulungu pankhani zimenezi, amapewanso kuwononga ndalama zake potchova njuga.

Baibulo lili ndi mfundo zothandiza pa moyo wa tsiku ndi tsiku, ngakhale munthu atakhala pa umphawi wotani. Taonani nkhani yotsatirayi:

M’dziko lina limene ntchito zimasowa kwambiri, mayi wina wogwira ntchito m’kampani anapempha bwana wake kuti akufuna kupita ku misonkhano yachikhristu. Zimenezi zikanaika ntchito yake pachiswe. Bwana wake akanatha kungom’chotsa ntchitoyo. Koma iyeyu ndiponso anzake kuntchitoko anadabwa kwambiri bwanayo atavomereza pempho lakelo. Komanso bwanayo anamuuza kuti amasangalala naye pantchitopo ndipo anamuyamikira kuti ndi “munthu wolimbikira kwambiri ntchito.” N’chifukwa chiyani anatero?

Mayiyu, yemwe ndi Wamboni za Yehova, ankatsatira mfundo za m’Baibulo pamoyo wake. Iye ankayesetsa ‘kufuna kuchita zinthu zonse moona mtima,’ motero sankanama kapena kuba. Zimenezi zinachititsa kuti akhale ndi mbiri yabwino. (Aheberi 13:18) Pomvera mfundo youziridwa yopezeka pa Akolose 3:22, 23, iye ankagwira ntchito yake ndi ‘moyo wake wonse.’ Zimenezi zikutanthauza kuti ankamvera bwana wake ndipo tsiku lililonse ankagwira ntchito mwakhama zedi.

N’zoona kuti tikukhala m’dziko limene anthu ake amakonda kudyera anzawo masuku pamutu. Ena mwa anthu amene amamvera kwambiri mfundo za m’Baibulo mwina angavutikebe kupeza chakudya, zovala, ndi malo okhala. Koma amakhala ndi chikumbumtima choyera kwa Mlengi wawo ndipo amayembekezera moyo wabwino m’tsogolo umene Yehova, “Mulungu amene amapereka chiyembekezo,” adzapereke.—Aroma 15:13.

Njira Yothetseratu Umphawi

Baibulo limanena kuti Yehova adzakhaulitsa anthu amene amachita zinthu zopondereza anthu osauka. Limati: “Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu; kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu . . . aumphawi zoyenera zawo, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!” (Yesaya 10:1, 2) Kaya anthu osaukawo amawanyalanyazira dala, kaya amatero chifukwa chosadziwa, Mulungu adzawononga anthu amene akuyendetsa chuma padziko pano limodzi ndi dziko loponderezali.

Mneneri Yesaya akufunsa oponderezawa funso lofunika kuliganizira bwino: “Mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang’anira, ndi chipasuko chochokera kutali?” (Yesaya 10:3) Yehova adzawawononga poseseratu dziko lawo loponderezali.

Sikuti cholinga cha Mulungu n’kudzangowononga anthu opondereza anzawo basi. Koma iye adzapatsa anthu olungama moyo wabwino kwambiri wosaponderezedwa. Adzagwiritsa ntchito boma loposa maboma onse kuthandiza anthu kukhala moyo wabwino, wosangalatsa ndiponso wa mwanaalirenji. Kuti mudzakhale opeza bwino panthawi imeneyi, simudzafunikira kukhala ndi ndalama zankhaninkhani, kudziwana ndi anthu enaake, kapena kudziwa kwambiri zamalonda. Kodi n’chiyani chingatithandize kusakayika kuti zimenezi zidzachitikadi?

Yesu Khristu, yemwe wasankhidwa ndi Yehova kuti adzalamulire anthu, ananena kuti nthawi imeneyi idzakhala “nthawi ya kukonzanso zinthu.” (Mateyo 19:28) Mawu amenewa akusonyeza kuti panthawiyi anthu adzayamba moyo watsopano. Potchula mawu akuti “nthawi ya kukonzanso zinthu,” Yesu anali kusonyeza kuti Yehova adzapatsa anthu olungama mwayi wokhala moyo umene Mlengi wathu wachikondi amafuna kuti tizikhala. Ena mwa madalitso ambiri amene Mlengiyu adzabweretse pa nthawiyi ndiwo kuchotseratu mavuto onse a zachuma amene akuvutitsa anthu masiku ano.

Baibulo limanena mwaulosi za ulamuliro wa Yesu Khristu. Iye anati: “Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”—Salmo 72:12-14.

Inuyo mungathe kukhala ndi tsogolo labwino chonchi. Koma kuti mukwaniritse zimene Mulungu amafuna kuti adzakuloleni kukhala ndi moyo m’dziko latsopanoli, m’pofunika kuti muphunzire kaye ndi kuyamba kuchita chifuniro cha Mulungu woona. Chitani zinthu mwanzeru pomvera Mawu a Mulungu. Muziyembekeza moyo wabwino kwambiri umene Mulungu akufuna kuti anthu onse adzathe kukhala nawo. Mukatero simudzanong’oneza bondo. Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzawonongeka kosatha.”—Salmo 9:18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Malemba ena awiri m’Baibulo amene amanenanso za mmene Mulungu amamvera anthu akamavutika ndi Salmo 35:10 ndiponso Salmo 113:7.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Mungathe kudzakhala ndi tsogolo labwino zedi

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

Kodi Ndisamukire Kunja?

Mawu a Mulungu sauza anthu za dera limene ayenera kumakhala kapena kumagwira ntchito. Komano mfundo za m’Baibulo zingam’thandize munthu kuona ngati ndi bwino kusamukira dziko lina chifukwa chofuna ndalama. Taganizirani mafunso otsatirawa ndi mfundo zothandiza za m’Malemba.

1. Kodi ndikungokhulupirira zam’maluwa? Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Munthu wina wa ku Eastern Europe ananena mawu otsatirawa atasamukira m’dziko lina lolemera: “Ndinamva kuti kunoko ndalama zimamera ngati masamba mumtengo. Koma chibwerereni kunoko sindinaipezebe mitengo imeneyi.”

2. Kodi ndikuganizira bwinobwino zinthu zimene banja langa limafunikira? Kodi ndikulephera kusiyanitsa pakati pa zinthu zofunikiradi ndi zinthu zongolakalaka? Inde, abambo, omwe ndi mitu yabanja, ali ndi udindo wosamalira akazi ndi ana awo. (1 Timoteyo 5:8) Komatu ndi udindo wawonso kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino ndi kuwaphunzitsa zinthu zauzimu. (Deuteronomo 6:6, 7; Aefeso 6:4) N’zotheka kuti bambo akasamukira kunja angathe kusamalira bwino banja lake pankhani ya zachuma. Koma sangathe kuphunzitsa ana ake makhalidwe abwino ndiponso mawu a Mulungu ngati saonana kwa nthawi yaitali, mwina milungu, miyezi, ngakhalenso zaka zimene.

3. Kodi ndikudziwa kuti kutalikirana ndi mkazi wanga kwa nthawi yaitali kumatiika tonse awiri pangozi yochita chigololo? Mawu a Mulungu amauza anthu okwatirana kuti aziganizirana pa nkhani ya kugonana.—1 Akorinto 7:5.

4. Kodi ndikudziwa kuti kulowa m’dziko lina moswa lamulo kungandiike m’mavuto ndi aboma am’dzikolo? Akhristu oona amayenera kumvera malamulo a dzikolo.—Aroma 13:1-7.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwa aliyense, kaya ndife olemera kapena osauka

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

Top: © Trygve Bolstad/​Panos Pictures