Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kumakaonana ndi Dokotala wa Mano?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kumakaonana ndi Dokotala wa Mano?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kumakaonana ndi Dokotala wa Mano?

KALE akatswiri a mano asanadziwe zambiri, anthu ankavutika kwambiri ndi mano kuyambira ali ana. Ambiri sankaoneka bwino chifukwa chokhala ndi mano othimbirira, opindikapindika, kapena magweru. Nkhalamba zambiri zopanda mano zinkadwala matenda osowa chakudya m’thupi kapena kufa kumene chifukwa cholephera kutafuna. Masiku ano anthu ambiri amene amakaonana ndi dokotala wa mano, sadandaula za kupweteka kwa mano, amakhala ndi mano moyo wawo wonse, ndipo amaoneka bwino akamamwetulira. Kodi akatswiri a mano anatani kuti zimenezi zitheke?

Madokotala a mano amaphunzitsa anthu mmene angasamalire mano ndiponso amawalimbikitsa kuti azikapimitsa mano awo kuchipatala. Zimenezi zathandiza kwambiri kuti anthu asamavutike ndi kupweteka kwa mano kapena magweru. Yesu anati: “Anthu athanzi safuna wochiritsa.” (Luka 5:31) Ena athandizika kwambiri ndi maphunziro a kasamalidwe ka mano ndipo safunika kukakonzetsa mano. * Ngakhale zili choncho, anthu ambiri sapita kokaonana ndi dokotola wa mano chifukwa cha ulesi, kupanda ndalama, ndi mantha. Kaya inu mumatani, ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi pali ubwino wanji wokaonana ndi dokotola wa mano? Kuti timvetse ubwino wake, tiyenera kumvetsa kuti amateteza bwanji mano athu.

Kodi Mano Amaola Bwanji?

Dokotala wa mano angakuthandizeni kuti musavutike ndi kupweteka kwa dzino kapena magweru. Mutagwirizana naye, dokotala angakuthandizeni kuchotsa zokanirira m’mano zimene zimakhala ndi mabakiteriya ooletsa mano. Mabakiteriya amachuluka akapeza zakudya zokanirira m’mano. Amasandutsa shuga kukhala asidi amene amaboola mano. Mbali ya timabowoyo ikapanga mphako, ndiye kuti dzino laola. Apa simumva kupweteka, koma mphakoyo ikangofika m’katikati mwa dzino, mumamva ululu wadzaoneni.

Mabakiteriya amene amakhala m’zokanirira m’mano amakuzunzani m’njira inanso. Ngati zokanirira m’mano sizichoka pokwecha, zimalimba ndipo nkhama zimatupa ndi kuyamba kulekana ndi mano. Zikatere, pamakhala mpata pakati pa dzino ndi nkhama pomwe zakudya zimatsakamira n’kupanga phwando la mabakiteriya amene amawononga nkhama. Dokotala wanu angaletse zimenezi kuti zisachitike. Koma ngati simusamala, nkhama zanu zingadyeke koopsa mpaka mano kuguluka. Anthu ambiri ataya mano awo mwa njira imeneyi osati chifukwa cha kuola.

Malovu amathandiza kuteteza mano kumabakiteriya amenewa. Kaya mwadya chakudya chamtundu wanji, malovu anu amafuna mphindi za pakati pa 15 ndi 45 kuti achotse zakudya zotsalira m’kamwa ndi kupha asidi m’mano. Zimenezi zimadalira kuti shuga kapena zakudya zakanirira bwanji m’mano. Zikuoneka kuti panthawi imeneyi ndi pamenenso mano anu amayamba kuwonongeka. Choncho, mano anu amawonongeka kwambiri osati chifukwa chakuti mumadya shuga wambiri, koma chifukwa chakuti mumadya pafupipafupi chakudya ndiponso zinthu zashuga. Mukagona, m’kamwa mumakhala malovu ochepa. Choncho mungawononge mano anu kwambiri ngati mutadya kapena kumwa zinthu zashuga n’kukagona popanda kutsuka m’kamwa. Komabe, akuti kutafuna chingamu chopanda shuga pambuyo pa chakudya, kumawonjezera malovu m’kamwa ndi kuteteza mano anu.

Katetezedwe ka Mano

Madokotala a mano amalimbikitsa kuti muzipita kokapimitsa mano anu kamodzi kapena kawiri pachaka malinga ndi mmene mano anu alili. Popima mano, dokotala nthawi zambiri amawajambula ndi kuona ngati mano anu ayamba kuola. Amakubayani mankhwala oletsa ululu poboola dzino, ndipo amatha kukumatani popanda kumva kupweteka. Kwa anthu amantha kwambiri, madokotala ena amagwiritsa ntchito moto wa magetsi kapena mafuta amene amachotsa malo oola akamamata dzino. Akagwiritsa ntchito zimenezi, nthawi zambiri safunikira kuboola mano kapena kubaya munthu mankhwala oletsa ululu. Kwa ana, madokotala amayang’anitsitsa mano aakulu akumbuyo omera kumene kuona ngati ali ndi ming’alu pamwamba kapena mbali zimene zingavute kutsuka ndi mswachi. Mwina dokotala anganene kuti amate manowo pofuna kuti akhale osalala ndi osavuta kutsuka ndipo zimenezi zimawateteza kuti asaole.

Akamasamalira anthu aakulu, madokotala kwenikweni amafuna kuteteza chiseyeye. Choncho akapeza kuti zokanirira m’mano zinalimba, amazipala. Anthu ambiri akamatsuka m’kamwa, sakwecha mbali zina za mano awo. Dokotala wa mano angakuuzeni mmene mungakwechere mano anu. Madokotala ena amauza anthu awo kuti apite kwa akatswiri otsuka mano kuti akawathandize.

Kukonza Mano

Ngati mano anu ndi owonongeka, anaguluka, kapena ndi opindikapindika, musade nkhawa chifukwa madokotala ali ndi njira zambirimbiri zamakono zowakonzera. Komabe, kukonza mano ndi kodula. Choncho muyenera kusamala kuti musaboole m’thumba. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amaona kuti ndi bwino kuwononga ndalama kuti akonze mano. Mwina dokotalayo angakuthandizeni kuti muyambirenso kudya bwinobwino. Kapenanso angakuthandizeni kuti muzioneka bwino mukamamwetulira. Zimenezi ndi zofunika kwambiri chifukwatu munthu ukakhala ndi mano owonongeka, moyo susangalatsa.

Mukakhala ndi dzino lakutsogolo lobenthuka kapena lothimbirira, dokotala angafune kulimata kutsogolo kwake ndi kachibenthu kuti lizioneka ngati lachilengedwe. Likamatidwa, limaoneka latsopano ndi lokongola. Koma dzino likakhala lowonongeka kwambiri, dokotala angafune kuti alivekere kachipewa dzino lonselo kuti lioneke latsopano. Kachipewaka kamakhala kagolide kapena kooneka ngati dzino lachilengedwe.

Kodi dokotala angatani ngati mano anu ena anaguluka? Angakupatseni mano amene mungamawaike kapena kuchotsa nokha. Kapenanso angakuikireni dzino lokhala ndi tizipewa tiwiri timene amativekera ku mano awiri oyandikana ndi dzino latsopanolo. Tizipewato timathandiza kuti dzino latsopanolo likhazikike pa gweru. Njira inanso imene ikufala masiku ano ndi yochita kupanga opaleshoni. Dokotola amazika kachitsulo pamalo pamene panali dzino loyamba munsagwada. Ndiyeno fupa ndi nkhama zikagwirana bwino, amalowetsa dzino lopanga lokhala ndi mazinga kukachitsuloko. Akapanga zimenezi, zimangokhala ngati munthu ali ndi dzino lachilengedwe.

Mano opindikapindika amachititsa manyazi ndipo sachedwa kugwidwa matenda chifukwa chakuti amavuta kutsuka. Munthu akakhala ndi mano opindika, nthawi zina amamupweteka ndipo amavutika kutafuna. Ngati muli ndi mano otere, musade nkhawa chifukwa madokotala amatha kuwongola mano mwa kuwamanga mawaya. Mawayawa akupangidwa bwino kwambiri masiku ano moti saonekera kwambiri ndipo safuna kumawasinthasintha.

Madokotala ena a mano amathandizanso kwambiri anthu amene ali ndi vuto lonunkha m’kamwa. Anthu ambiri amakhala ndi vuto limeneli mwa apa ndi apo pamene ena ndi vuto lawo lanthawi zonse. Pali zinthu zambiri zimene zimachititsa vutoli. Madokotala ena ali ndi zipangizo zodziwira chimene chimachititsa kuti munthu azinunkha m’kamwa. Nthawi zambiri vutoli limayamba chifukwa cha mabakiteriya amene amakhala kumbuyo kwa lilime chakum’mero. Kutsuka kapena kukwecha lilime n’kothandiza, monganso kutafuna chingamu chopanda shuga, kumene kumawonjezera malovu m’kamwa. Kutsuka m’kamwa n’kofunika kwambiri makamaka mukadya zakudya zamkaka, nyama kapena nsomba.

Mungatani Ngati Muli ndi Mantha?

Ngati mumachita mantha kuonana ndi dokotala wa mano, iye angakuthandizeni kulimba mtima. Choncho, muuzeni ngati mukuchita mantha. Muuzirenitu zizindikiro zimene muzimusonyeza ndi manja anu mukamva kupweteka kapena mukachita mantha. Ambiri aona kuti zimenezi zimawathandiza kulimba mtima.

Mwina mungachite mantha kuti akukalipirani. Mungade nkhawa kuti dotokotala akunenani chifukwa chosasamalira mano anu. Komabe, simuyenera kuchita mantha kuti akunyozani chifukwa ngati atatero, bizinesi yawo ingalowe pansi. Madokotala ambiri a mano amakhala okoma mtima.

Anthu ambiri sapita kwa dokotala wa mano chifukwa choopa kuwononga ndalama. Koma ngati mungapite panopa, mungapewe mavuto ambiri a mano ndipo simungadzawononge ndalama zambiri m’tsogolo. Kumadera ambiri kuli zipatala za mano zimene zingathandize aliyense malinga ndi m’thumba mwake. Ngakhale zipatala zoti si zapamwamba kwambiri zimakhala ndi makina ojambulira ndi oboolera mano. Madokotala amatha kukonza mano popanda munthu kumva kupweteka kwambiri. Mtengo wa mankhwala oletsa ululu si wokwera kwambiri moti anthu ambiri, ngakhale amene alibe ndalama zambiri, angakwanitse.

Ntchito ya madokotala a mano si yokupwetekani ayi koma kukuchepetserani ululu. Njira zokonzera mano masiku ano si zoopsa zija ngati zimene agogo anu angakumbukire. Popeza kuti mano abwino amathandiza munthu kukhala ndi thanzi labwino ndi moyo wosangalala, bwanji osapita kukaonana ndi dokotala wa mano? Kumeneko akakuthandizani bwino ndipo simudzakhulupirira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Nkhaniyi ikufotokoza zimene dokotola wa mano amachita poteteza mano. Koma ngati mukufuna kudziwa mmene inuyo mungatetezere mano anu, werengani nkhani yakuti “How You Can Protect Your Smile,” mu Galamukani! ya Chingelezi ya November 8, 2005.

[Chithunzi patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Dzino Labwino

Mutu

Kunja kwake

Fupa la dzino

Nkhama

M’kati mokhala timitsempha

Nsagwada

Muzu

[Chithunzi patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Dzino Loola

Mphako

Kumata dzino kumaletsa mphako kukula

[Chithunzi patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chiseyeye

Zokanirira ziyenera kuchotsedwa

Zokanirira zolimba zimavuta kuchotsa ndipo nkhama zimalekana ndi mano

Nkhama zolekana ndi mano

[Chithunzi patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kukonza Mano

Kachibenthu amakamata ku dzino

Kachipewa

Dzino lolowetsa mu fupa

Dzino lochita kuika la tizipewa tiwiri tovekedwa ku mano oyandikana kuti dzino latsopano lilimbe