Sindinenso Kapolo wa Mowa
Sindinenso Kapolo wa Mowa
Anthu nthawi zambiri amasangalala ngati pachakudya kapena paphwando pali mowa pang’ono. Komabe, anthu ena mowa umawabweretsera mavuto aakulu. Werengani nkhani ili m’munsiyi kuti mumve mmene munthu wina anamasukira ku ukapolo wa mowa.
NGAKHALE panopa, zimandipwetekabe kusimba za mavuto amene tinali nawo panyumba pathu. Bambo ndi mayi amati akamwa, bambo ankakonda kumenya mayi. Zikatero, nthawi zambiri bambo ankandiponyeranso zibakera. Pamene analekana banja n’kuti ndili ndi zaka zinayi zokha, koma ndikukumbukira kuti anakandisiya kwa agogo.
Ndinaona kuti palibe amene akundifuna. Ndili ndi zaka 7, ndinkakonda kupita mozemba kuchipinda chapansi kukamwa vinyo wopanga tokha. Ndikamwa vinyoyo, mavuto anga amakhala ngati atha. Ndili ndi zaka 12, mayi ndi agogo anga anakangana kwambiri chifukwa cha ine. Mayi analusa kwambiri mpaka anandiponyera chifosholo chokhala ngati foloko. Koma ndinachilewa. Kameneka sikanali koyamba kuti moyo wanga ukhale pangozi. Komabe, mabala amene ndinali nawo chifukwa chomenyedwa sanali opweteka kwambiri poyerekezera ndi ululu umene ndinkamva mu mtima wanga.
Pofika zaka 14, ndinkangokhalira kumwa mowa. Ndipo nditafika zaka 17, ndinathawa pa nyumba. Mowa unandipatsa ufulu ndipo ndinali munthu waukali, wovutitsa anthu m’mabala. Palibe chimene ndinkasangalala nacho ngati mowa. Tsiku limodzi lokha, ndinkamwa vinyo malita asanu, mowa mabotolo angapo, ndiponso zakumwa zina zaukali.
Nditakwatira, mkazi wanga anali pa mavuto aakulu chifukwa chakuti ndinkamwa kwambiri. Panyumbapo tinkangokhalira kuzazirana ndipo ndinkamenya mkazi wanga ndi ana omwe. Moyo wake unali wofanana ndi umene ndinakulira. Ndalama zanga zonse zinkathera ku mowa. Tinalibe ndi bedi yomwe, moti tinkagona pansi. Moyo wanga unali wopanda pake ndipo ndinalibenso mtima wofuna kukonza zinthu.
Tsiku lina nditacheza ndi munthu wina wa Mboni za Yehova, ndinam’funsa chifukwa chake anthufe tili ndi mavuto ochuluka. Iye anandisonyeza m’Baibulo malemba onena za dziko lopanda mavuto, limene Mulungu walonjeza. Zimenezi zinandigwira mtima, ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Nditayamba kugwiritsa ntchito zimene ndinali kuphunzira, ndinachepetsa kumwa mowa ndipo zinthu zinayamba kuyenda bwino
m’banja mwathu. Komabe, ndinadziwa kuti ngati ndikufuna kutumikira Yehova Mulungu m’njira imene amafuna, ndinayenera kuthetsa vuto langa lomwa mowa. Ngakhale kuti zinali zondivuta, ndinasiyiratu kumwa mowa patatha miyezi itatu. Patapitanso miyezi ina 6, ndinadzipereka kwa Mulungu ndipo ndinabatizidwa.Nditamasuka ku ukapolo wa mowa, ndinatha kubweza ngongole zanga zonse. Patapita nthawi, ndinagula nyumba. Ndinagulanso galimoto, imene timakwera popita ku misonkhano ndi kuulaliki wa khomo ndi khomo. Panopa, ndine munthu waulemu wake.
Nthawi zina ndikamacheza ndi anzanga, amandipatsa mowa. Ambiri sadziwa nkhondo yaikulu imene ndili nayo kuti ndikangomwa botolo limodzi lokha, nditha kuyambiranso moyo wanga wakale. Chilakolako cha mowa ndikadali nachobe. Kuti ndikane mowa, ndimafunika kupemphera kwambiri ndiponso kulimba mtima. Ndikamva ludzu, ndimamwa kwambiri zinthu zilizonse zosaledzeretsa. Patha zaka 10 tsopano osamwa mowa.
Yehova amachita zimene munthu sangathe. Wandithandiza kupeza ufulu umene sindinayembekezere. Mtima umandipwetekabe ndikakumbukira ubwana wanga, ndipo nthawi zonse ndimalimbana ndi maganizo amenewo. Komabe, cholimbikitsa n’chakuti ndili ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu, anzanga apamtima mumpingo, ndiponso banja labwino limene timapembedzera limodzi. Mkazi wanga ndi ana amandilimbikitsa ndi mtima wonse pankhondo yolimbana ndi mowa. Mkazi wanga amati: “Kale, moyo wanga unali pa moto. Koma lero ndimathokoza Yehova chifukwa chotithandiza kukhala ndi banja labwino. Ine, mwamuna wanga, ndi ana athu awiri, tonse ndife osangalala.”—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa ndi munthu wina.
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Pofika zaka 14, ndinkangokhalira kumwa mowa
[Mawu Otsindika patsamba 22]
Yehova amachita zimene munthu sangathe
[Bokosi/Zithunzi patsamba 22]
KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI ZA MOWA?
▪ Baibulo sililetsa mowa. Limati “vinyo wokondweretsa mtima wa munthu,” ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Salmo 104:14, 15) Baibulo limasonyezanso kuti mpesa umaimira moyo wabwino ndi wotetezeka. (Mika 4:4) Ndipotu, chozizwitsa choyamba cha Yesu Khristu chinali kusandutsa madzi kukhala vinyo paphwando la ukwati. (Yohane 2:7-9) Ndiponso, mtumwi Paulo atamva za “kudwaladwala” kwa Timoteyo, anamuuza kuti azimwa “vinyo pang’ono.”—1 Timoteyo 5:23.
▪ Chimene Baibulo limaletsa ndi kumwa kwambiri mowa:
‘Zidakwa . . . sizidzalowa mu ufumu wa Mulungu.’—1 Akorinto 6:9-11.
“Musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa”—Aefeso 5:18.
“Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa. Usayang’ane pavinyo alikufiira. Alikung’azimira m’chikho. Namweka mosalala. Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba. Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota.”—Miyambo 23:29-33.
Monga mmene taonera m’nkhaniyi, anthu ena amene anali ndi vuto la kumwa mowa achita bwino kusiyiratu kumwa.—Mateyo 5:29.