Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndili ndi Matenda Ovutika Kudya? (October 2006) Nkhani imeneyi inandikhumudwitsa kwambiri. Ndakhala ndikulimbana ndi matenda ovutika kudya moyo wanga wonse. Nditaiwerenga ndinamva kuti ndikanathetsa vutoli ndili mwana. Koma mpaka pano ndikulimbanabe ndi nthenda imeneyi ndipo ndikuona kuti sindingathenso kuithetsa. Nkhaniyi ikusonyeza ngati kuti munthu akhoza kuthetsa matenda amenewa ngati ali ndi chikhulupiriro cholimba.
J. J., United States
Yankho la “Galamukani!”: Nkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa,” kwenikweni zimalembedwera achinyamata, koma malangizo a m’Baibulo opezeka m’nkhani zimenezi amathandiza anthu onse. Tikudziwa kuti matenda ovutika kudya ndi ovuta kwambiri kuwathetsa. Nkhaniyo sinanene kuti amene ali ndi matenda amenewa alibe chikhulupiriro. Inangofotokoza kuti anthu odwala matendawa angapemphere kwa Yehova kuti awathandize. Kuwonjezera pa kupemphera kwa Mulungu, analimbikitsidwanso kupempha thandizo kwa ‘kholo kapena wachikulire wina.’ Komanso nkhaniyo inati, “si zophweka kuti munthu afike pochira,” ndiponso inati matendawa angayambirenso. Popeza mukulimbanabe ndi matendawa mpaka pano, zikusonyeza kuti simunataye mtima ndipo mukuchita bwino.
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndidzagwire Ntchito Yotani Pamoyo Wanga? (July 2006) Ndatsala pang’ono kumaliza sukulu ndipo ndikufunikira kusankha ntchito yoti ndidzagwire. Nkhaniyi yandilimbikitsa kuti ndiyambe utumiki wa nthawi zonse. Ndaona kuti ndi ntchito yokhayi imene ili yofunika kwambiri ndiponso imene ingandibweretsere chimwemwe.
H. W., Hong Kong
Ndikuyamikira kwambiri nkhani imeneyi chifukwa yandithandiza kuona kuti m’dziko lokonda chumali, chinthu chabwino chimene wachinyamata ngati ine angachite ndi kuika zinthu zauzimu patsogolo.
A. S., Brazil
Nthawi zambiri ndimaiwala zolinga zanga za m’tsogolo chifukwa chokhala wotanganidwa tsiku lililonse. Kuwerenga nkhani imeneyi kwandithandiza kukhalanso ndi mtima wofuna kuchita zonse zimene ndingathe potumikira Yehova. Zikomo kwambiri chifukwa choganizira achinyamatafe.
E M., Japan
Mmene Mungakhalire ndi Banja Losangalala (July 2006) Nkhani zimenezi ndi zabwino kwabasi. Munagwiritsa ntchito chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu ndiponso mmene ankachitira zinthu ndi atumwi ake posonyeza zimene anthu amene ali pa banja ayenera kuchita. Pitirizani ntchito yabwinoyi. Mwezi uliwonse timayembekezera kulandira magazini amenewa.
S. C., United States
Ndinali Wotaya Mtima Koma Tsopano Ndine Wosangalala (July 2006) Monga m’bale González, inenso ndakhala ndikulimbana ndi vuto lodzikayikira. Ndinkaganiza kuti, ‘Yehova sangandikonde chifukwa cha zoipa zanga zakale.’ N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova ndi wachisomo, wokhululuka ndi wachikondi. Chifukwa cha malangizo, thandizo lachikondi lochokera ku mpingo ndi mzimu woyera wa Yehova, ndathandizidwa kugwiritsa ntchito choonadi cha m’Baibulo pamoyo wanga. Zikomo kwambiri potipatsa chakudya chauzimu panthawi yake.
T. A., United States