Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziona Ndalama Moyenera

Tiziona Ndalama Moyenera

Zimene Baibulo Limanena

Tiziona Ndalama Moyenera

BAIBULO limati: “Ndalama zitchinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Ndalama zingatitchinjirizedi kuti tisakhale pa umphawi chifukwa chakuti zingatithandize kupeza chakudya, zovala ndi pogona. Ndithudi, ndalama zingakuthandizeni kugula pafupifupi chinthu chilichonse. Lemba la Mlaliki 10:19 limati: “Ndalama zivomera zonse.”

Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama kuti tithe kudzisamalira ndi kusamaliranso banja lathu. (1 Timoteyo 5:8) Kugwira ntchito mwakhama ndi mokhulupirika kumathandiza munthu kukhala ndi moyo wosangalala, wolemekezeka ndi wotetezeka.—Mlaliki 3:12, 13.

Kugwira ntchito mwakhama kumatithandizanso kuti tithe kukhala owolowa manja. Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Timakhaladi osangalala tikamagwiritsa ntchito ndalama zathu mokondwera kuthandiza osowa, makamaka Akhristu anzathu, kapena tikagulira mphatso munthu amene timam’konda.—2 Akorinto 9:7; 1 Timoteyo 6:17-19.

Yesu analimbikitsa otsatira ake kukhala ndi chizolowezi chopatsa nthawi zonse. Iye anati: “Khalani opatsa.” (Luka 6:38) Timafunikanso kukhala opatsa kuti tithandize nawo pantchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu mwa kupereka chuma chathu. (Miyambo 3:9) Zoonadi, kukhala opatsa m’njira imeneyi, kungatithandize kuti Yehova ndi Mwana wake akhale “mabwenzi” athu.—Luka 16:9.

Pewani “Kukonda Ndalama”

Anthu odzikonda amakhala ouma manja ndipo akapatsa ena zinthu nthawi zambiri amakhala ndi zolinga zadyera. Vuto lawo n’loti amakonda kwambiri ndalama, ndipo m’malo mosangalala amakhala anthu opanda chimwemwe. Lemba la 1 Timoteyo 6:10 limati: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.” Kodi n’chifukwa chiyani kukonda ndalama sikuthandiza anthu kukhala osangalala? Nanga kuipa kwake n’kotani?

Munthu wokonda kwambiri ndalama sakhutira ndi chuma chake. Lemba la Mlaliki 5:10 limati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva.” Choncho, anthu okonda kwambiri ndalama amangogwiritsidwa mwala. Ndiponso, chifukwa chokonda kwambiri ndalama sagwirizana bwino ndi anthu ena, sakhala ndi banja losangalala, ndipo amasowa tulo. Baibulo limati: “Tulo ta munthu wogwira ntchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.” (Mlaliki 5:12) Koposa zonse, Mulungu sasangalala ndi munthu wokonda kwambiri ndalama.—Yobu 31:24, 28.

M’Baibulo ndi m’mabuku ena muli nkhani zambiri za anthu amene anachita zinthu zoipa monga kuba, kulandira ziphuphu, kuchita uhule, kupha, kupereka anzawo ndi kunama chifukwa chofuna ndalama. (Yoswa 7:1, 20-26; Mika 3:11; Maliko 14:10, 11; Yohane 12:6) Yesu ali padziko lapansi, anapempha wolamulira wina wachinyamata “wolemera kwabasi” kuti amutsate. N’zachisoni kuti mnyamata ameneyu anakana kutsatira Yesu chifukwa choopa kutaya chuma chake. N’chifukwa chake Yesu anati: “Zidzakhalatu zovuta zedi kuti anthu a ndalama adzalowe mu ufumu wa Mulungu!”—Luka 18:23, 24.

“M’masiku otsiriza” ano, Akhristu ayenera kusamala kwambiri chifukwa monga mmene Baibulo linanenera, anthu ambiri ndi “okonda ndalama.” (2 Timoteyo 3:1, 2) Akhristu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, satengeka ndi mtima wadyera chifukwa ali ndi chuma choposa ndalama.

Chuma Choposa Ndalama

Mfumu Solomo itanena kuti ndalama zimatchinjiriza, inanenanso kuti “nzeru itchinjiriza” chifukwa “isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Kodi Solomo anatanthauza chiyani? Anali kunena za nzeru yobwera chifukwa chodziwa Malemba molondola ndi kuopa Mulungu. Mosiyana ndi ndalama, nzeru yochokera kwa Mulungu ingateteze munthu ku mavuto ambiri ndipo angakhale ndi moyo wautali. Komanso, anthu amene ali ndi nzeru imeneyi amakhala ngati avala korona, ndipo amapatsidwa ulemu. (Miyambo 2:10-22; 4:5-9) Nzeruyi imatchedwa “mtengo wa moyo” chifukwa chakuti imathandiza munthu kuti ayanjidwe ndi Mulungu.”—Miyambo 3:18.

Anthu amene amakonda nzeru imeneyi ndiponso amayesetsadi kuifunafuna, amaipeza. Baibulo limati: “Mwananga, . . . ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziwadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”—Miyambo 2:1-6.

Popeza kuti Akhristu enieni amaona kuti nzeru ndi yamtengo wapatali kuposa ndalama, amakhala ndi zinthu zimene anthu okonda ndalama sakhala nazo kwenikweni monga mtendere, chisangalalo ndi chitetezo. Lemba la Aheberi 13:5 limati: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo panthawiyo. Pakuti [Mulungu] anati: ‘Mulimonse sindidzakusiyani, ngakhale kukutayani konse.’” Chitetezo chotere sitingachigule ndi ndalama.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi ndalama zimatchinjiriza motani?—Mlaliki 7:12.

▪ Kodi nzeru yochokera kwa Mulungu imaposa bwanji ndalama?—Miyambo 2:10-22; 3:13-18.

▪ Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kukonda kwambiri ndalama?—Maliko 10:23, 25; Luka 18:23, 24; 1 Timoteyo 6:9, 10.