Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsatirani Khristu!”

“Tsatirani Khristu!”

Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova Wakuti

“Tsatirani Khristu!”

Misonkhano ya masiku atatu imeneyi inayamba kuchitika ku United States m’mwezi wa May ndipo idzapitiriza kuchitika m’mizinda yambiri padziko lonse mpaka chaka cha 2008. M’madera ambiri misonkhano imeneyi izidzayamba Lachisanu ndi nyimbo zamalimba nthawi ya 9:20 kum’mawa. Pulogalamu ya tsiku lililonse idzafotokoza kwambiri za Yesu.

Pulogalamu ya Lachisanu ili ndi mutu wakuti, ‘Yang’anitsitsani Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa Chikhulupiriro Chathu, Yesu.’ (Aheberi 12:2) Nkhani ya malonje ndi yakuti, “N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira ‘Khristu’?” Ndiyeno padzakhala nkhani yosiyirana ya zigawo zitatu yakuti, “Kuzindikira Kuti Yesu Ndiye Mose, Davide ndiponso Solomo Wamkulu.” Chigawo cha m’mawa chidzatha ndi nkhani yaikulu yakuti, “Yesu Ali ndi Udindo Wapadera pa Kukwaniritsa Chifuniro cha Yehova.”

Lachisanu masana, nkhani yoyamba idzakhala yakuti, “‘Ifetu tapeza Mesiya.’” Ndipo nkhani yotsatira idzakhala yakuti, ‘Kupeza Chuma ‘Chobisidwa Mosamala mwa Iye.’” Nkhani yosiirana ya ola limodzi ya mutu wakuti, “Khalani ndi Maganizo a Khristu” ili ndi mitu yakuti, “Anawalandira Bwino,” “Anakhala Womvera Mpaka Imfa,” ndiponso “Anawakonda Mpaka Mapeto.” Chigawochi chili ndi nkhani yakuti, “Amatsatira Mwanawankhosa Kulikonse Kumene Akupita.”

Mutu wa pulogalamu ya Loweruka ndi wakuti, “Nkhosa Zanga Zimamva Mawu Anga, . . . Ndipo Zimanditsatira.” (Yohane 10:27) Nkhani ina yosiyirana ya ola limodzi ya mutu wakuti, “Tsatirani Chitsanzo cha Yesu Muutumiki,” idzakhala ndi malangizo otithandiza kuti utumiki wathu uziyenda bwino. Pambuyo pa nkhani zakuti, “‘Anakonda Chilungamo Ndipo Anadana ndi Kusamvera Malamulo’—Kodi Inunso Mumatero?” ndiponso “‘Tsutsani Mdyerekezi’ Monga mmene Yesu Anachitira,” chigawo cha m’mawachi chidzatha ndi nkhani ya ubatizo. Ndipo pamapeto pake anthu amene ali oyenerera adzabatizidwa.

Pulogalamu yamasana ya Loweruka idzayamba ndi nkhani yosiirana yakuti “Musatsatire . . . ” Mbali zake sikisi ndi zakuti “Unyinji wa Anthu,” “Mtima Wanu ndi Maso Anu,” “Zinthu Zachabe Zosatsimikizirika,” “Aphunzitsi Onyenga,” “Nkhani Zonama,” ndi “Satana.” Nkhani zotsatira ndi izi: “‘Kuphunzitsidwa ndi Yehova’ Kumaposa Maphunziro Ena Onse” ndi “Athandizeni Kubwerera ku Gulu la Nkhosa.” Tsiku limeneli lidzatha ndi nkhani yofotokoza mfundo zazikulu zimene zaphunziridwa pa msonkhanowu, ya mutu wakuti “Ubwere Udzakhale Wotsatira Wanga.”

Mutu wa Lamlungu ndi wakuti “Pitiriza Kunditsatira Ine.” (Yohane 21:19) Pambuyo pa nkhani yakuti, “Musapereke Zifukwa Zodzikhululukira Polephera Kutsatira Khristu,” padzabwera nkhani yosiyirana ya mbali sikisi yakuti, “Mfundo Zamtengo Wapatali za mu Ulaliki wa Paphiri” idzafotokoza mawu ena amene Yesu ananena monga akuti: “Osangalala Ali Iwo Amene Amazindikira Zosowa Zawo Zauzimu,” “Ukayanjane ndi M’bale Wako Choyamba,” ndi “Khalani Opatsa, Inunso Anthu Adzakupatsani.” Pulogalamu ya m’mawa idzatha ndi nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Ndani Amene Akutsatiradi Khristu?” Mbali yosangalatsa kwambiri ya chigawo cha masana idzakhala sewero la nkhani ya m’Baibulo ya Gehazi, wantchito wadyera wa mneneri Eliya ndipo ochita seweroli adzavala mogwirizana ndi mmene anthu ankavalira panthawi ya m’Baibulo. Msonkhanowu udzatha ndi nkhani yakuti, “Pitirizani Kutsatira Khristu, Mtsogoleri Wathu Wosagonjetseka.”

Yambiranitu panopo kukonzekera kukapezeka pa msonkhanowu. Kuti mudziwe malo a kufupi ndi kwanu amene kukachitikire msonkhanowu, funsani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kwanuko kapena tilembereni kalata. Magazini ya March 1 ya Nsanja ya Olonda, ili ndi mndandanda wa malo onse amene msonkhanowu ukachitikire ku Malawi ndi ku Mozambique.