Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zinandisiyitsa Moyo Wotchuka

Zimene Zinandisiyitsa Moyo Wotchuka

Zimene Zinandisiyitsa Moyo Wotchuka

Yosimbidwa ndi Marcelo Neím

NDINABADWIRA mu mzinda wa Montevideo, m’dziko la Uruguay. Ngakhale kuti makolo anga anali oopa Mulungu, sanali m’chipembedzo chilichonse. Ndili ndi zaka pafupifupi zinayi, mayi anga anamwalira pa ngozi inayake, choncho ndinaleredwa ndi achibale amene anayesetsa kundiphunzitsa makhalidwe abwino. Nditafika zaka 20, ndinayamba kuyenda m’mayiko osiyanasiyana n’cholinga choti ndidziwe mayikowo ndiponso zikhalidwe zawo.

Nditafika ku Colombia, ndinayamba kugwira ntchito yothandizira gulu lochita zionetsero za masewera osiyanasiyana. Akatswiri ochita masewerawa ankaoneka osangalala kwambiri anthu akamawachemerera. Motero inenso ndinkasirira kuti ndikhale ngati iwowo. Ndiye ndinayamba kusewera pa njinga. Poyamba ndinkaseweretsa njinga yaikulu, kenako yaing’ono, mpaka ndinafika pomasewera pa kanjinga kakang’ono zedi komwe kanali kotalika masentimita 12 basi. Kanjinga kameneka n’kamodzi mwa tinjinga ting’onoting’ono kwambiri padziko lonse, moti kankakwana pa chikhato changa. M’kupita kwa nthawi, ndinatchuka ndithu m’madera ambiri a ku South America. Ndili ndi zaka 25, ndinapita ku Mexico komwe ndinachita masewerawa m’magulu angapo ndithu.

Ndinasintha Kwambiri

Ndinkakonda kwambiri masewerawa chifukwa ndinkatha kupita m’madera osiyanasiyana, kukhala ndiponso kudya m’mahotela apamwamba zedi. Ngakhale zinali choncho, ndinkaona kuti moyo wanga unalibe cholinga chenicheni chifukwa ndinalibe chiyembekezo chilichonse cha m’tsogolo. Ndiyeno, tsiku lina masana chinthu china chinachitika chimene chinasintha moyo wanga. Munthu yemwe ankayendetsa mwambo wa masewera anandipatsa buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand! * limene anapatsidwa ndi munthu wina. Titamaliza zionetserozo, ndinayamba kuwerenga bukulo mpaka mbandakucha. Ngakhale kuti bukuli linkandivuta kwambiri kumvetsa, ndinachita chidwi ndi mmene linalongosolera chilombo chofiiritsa ndiponso mkazi wachiwerewere. (Chivumbulutso 17:3–18:8) Ndiyeno tsiku lina ndikukonza m’kanyumba kokoka pa galimoto komwe ndinagula, ndinapezamo buku lina lofalitsidwanso ndi a Mboni, lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.* Ilitu linali losavuta kumvetsa ndipo nditaliwerenga, ndinazindikira kuti ndiyenera kulalikira. Nthawi yomweyo ndinayamba kuuza aliyense amene ndinkakumana naye zimene ndinawerengazo.

M’kupita kwa nthawi, ndinaona kuti m’pofunika kuti ndifufuze Mboni za Yehova. Mwamwayi, ndinapeza nambala ya telefoni m’buku la Revelation Climax ya mtsikana wamboni amene anapereka bukuli kwa mnzanga yemwe ankayendetsa mwambo wa masewera uja. Motero ndinayimba foniyo ndipo bambo ake anandiitanira ku msonkhano wa Mboni za Yehova womwe unachitikira mu mzinda wa Tijuana, ku Mexico. Ndinachita chidwi kwambiri ndi chikondi chimene ndinaona kumeneko ndipo zinali zoonekeratu kuti chipembedzo choona n’chimenechi. Kudera lililonse limene gulu lathu lochita zionetsero linapitako, ndinkafika ku Nyumba ya Ufumu ya m’deralo ndipo ndinkatengako mabuku n’kumagawira.

Ndiyeno chinthu chinanso chinachitika chimene chinandikhutiritsa kwambiri kuti ndapezadi chipembedzo choona. Anthu a Mboniwo anandiitanira ku Chikumbutso cha imfa ya Khristu ndipo anandilongosolera kuti Akhristu amafunikira kupezeka pa mwambo umenewu. Komatu madzulo omwe Chikumbutso chinali kuchitika, inalinso nthawi imene tinafunikira kuyamba mwambo wa masewera athu. Ndiye ndinaona kuti zidzandivuta kwambiri kupezeka pa Chikumbutso. Ndinapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima za nkhaniyi, ndipo chinachake chinachitika mosayembekezereka. Kutangotsala maola awiri kuti tiyambe kuchita mwambo wa masewera, magetsi anathima. Motero ndinatha kupezeka pa Chikumbutso, ndipo pambuyo pake ndinakachita masewerawo. Apatu ndinaona kuti Yehova anayankha pemphero langa.

Panthawi ina ndili pa mzere ku banki ndinkagawa timapepala tamawu a Mulungu. Ndiyeno mkulu wina wa mumpingo wa Mboni za Yehova atandiona, anandiyamikira chifukwa cha khama langali. Anandilimbikitsa kuti ndiyenera kumalalikira m’njira yolongosoka, motsogozedwa ndi mpingo. Ndipo mwachikondi, anandilongosolera kuti ndiyenera kusintha zina ndi zina pamoyo wanga kuti ndizilalikira ndi mpingo. Panthawi imene ndinkaganiza zoti ndisinthe zina ndi zina pamoyo wanga, ndinaitanidwa kuti ndikayambe ntchito ya malipiro apamwamba kwambiri m’gulu lina lochita zionetsero za masewera la ku United States. Pamenepa ndinavutika maganizo kuti ndisankha chiyani. Ndimafuna ndithu kupita ku United States, koma ndikanapita, sindikudziwa ngati ndikanapitiriza n’komwe njira ya choonadi imene ndinayamba kutsatira. Chimenechi chinali chiyeso changa choyamba ndipo sindinafune kukhumudwitsa Yehova. Motero ndinachoka m’gululi n’kuyamba kusonkhana mokhazikika ngakhale kuti anzanga amene ndinkachita nawo masewerawa anakhumudwa kwambiri. Nditatero, ndinameta tsitsi langa lomwe linali lalitali, ndiponso ndinasintha zina ndi zina pamoyo wanga kuti nditumikire bwino Yehova.

Ndine Wosangalala Ndipo Sindinong’oneza Bondo

Mu 1997 nditatsala pang’ono kubatizidwa kuti ndikhale wa Mboni za Yehova, ndinakumana ndi chiyeso china. Ndinapeza mwayi winanso wopita ku United States, mumzinda wa Miami, kuti akandionetse ndikuchita masewerawa papulogalamu inayake yotchuka ya pa TV ndipo anandilipirira zinthu zonse zofunikira pa ulendowu. Komabe ndinkafuna kubatizidwa ndiponso kukwaniritsa zimene ndinalonjeza kwa Yehova. Choncho ndinakana mwayiwu. Zimenezi zinadabwitsa kwambiri anthu amene anandiitanawo.

Anthu ena andifunsapo ngati ndimanong’oneza bondo chifukwa chosiya moyo wokhala munthu wotchuka. Ndimayankha kuti moyo wanga wonse wam’mbuyomu sungafanane ngakhale pang’ono ndi mmene Yehova akundikondera komanso ubwenzi wanga ndi Iye. Moyo wanga tsopano uli ndi cholinga ngakhale kuti ntchito yolalikira nthawi zonse imene ndikugwira tsopano, si yotchukira, sichititsa anthu kundichemerera, ndiponso si yolemeretsa. Panopa ndimangoganizira za chiyembekezo chodzakhala m’paradaiso padziko lapansi ndi kudzalandira mayi anga akamadzaukitsidwa.—Yohane 5:28, 29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.