Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Pakafukufuku wina anapeza kuti kuchita opaleshoni azimayi pobereka n’koopsa kusiyana ndi kubereka popanda opaleshoni. Akuti pa mzimayi mmodzi aliyense amene amamwalira chifukwa cha mavuto okhudzana ndi kubereka popanda kuchitidwa opaleshoni, azimayi oposa atatu ochitidwa opaleshoni pobereka amamwalira.—ZACHOKERA MU MAGAZINI YA OBSTETRICS AND GYNECOLOGY, KU UNITED STATES.

Stephen Hawking, yemwe ndi katswiri wa sayansi anaika pa Intaneti funso lotsatirali, kuti aliyense amene akufuna anene yankho lake: “Padziko pano pali mavuto azandale, azachuma, azachikhalidwe, ndiponso azanyengo, ndiye kodi zidzatheka kuti anthu akhalebe ndi moyo padziko pano zaka 100 zikubwerazi?” Kenaka patangopita mwezi umodzi, iye ananena mosabisa kuti: “Inenso sindikudziwa yankho lake. N’chifukwa chaketu ndinafunsa funsoli kuti anthu aliganizire mozama, komanso kuti adziwe zoopsa zimene zingathe kutigwera m’tsogolo muno.”—ZACHOKERA MU NYUZI YA THE GUARDIAN, KU BRITAIN.

Chaka chilichonse anthu pafupifupi 14 miliyoni ndi 19 miliyoni mwa anthu 37 miliyoni a ku Tanzania amadwala malungo. “Matendawa amapha anthu pafupifupi 100,000 a m’dzikoli chaka chilichonse.”—ZACHOKERA MU NYUZI YA THE GUARDIAN, KU TANZANIA.

Nsomba Zikuteteza Anthu ku Madzi Oipa

Pofuna kudziwa ngati madzi ali abwino kumwa kapena ayi, mizinda ingapo ku North America ikugwiritsa ntchito nsomba zinazake zomwe zimatha kudziwa m’madzi mukagwera mankhwala oipa. Lipoti la bungwe lina lofalitsa nkhani (Associated Press) linati: “Nsombazi amaziika m’mathanki a madzi opita m’mizindayo. M’mathankiwa amaikamonso zipangizo zomwe zimaunika nsombazo nthawi zonse kuti zione ngati zikusintha kapumidwe, kugunda kwa mtima, ndiponso kasambiridwe chifukwa cha mankhwala enaake oopsa amene agwera m’madzimo.” Malinga ndi lipotilo, panthawi ina mumzinda wa New York City, “nsombazi zinazindikira kuti m’madzi mwagwera dontho la dizilo. Nsombazi zinazindikira zimenezi mofulumira kwambiri . . . chifukwa makina ena aliwonse akanatulukira diziloyo patadutsa maola awiri.” Ndipotu zimenezi zinathandiza anthu kuti asamwe madzi oipawo.

Akuwonjezera Mankhwala Opatsa Chibaba mu Ndudu

Pamene a zaumoyo akulimbikitsa anthu kuti asiye kusuta, makampani opanga ndudu za fodya “akhala akuwonjezera mwachinsinsi mankhwala opatsa chibaba m’ndudu zomwe akupanga” n’cholinga choti anthu azilephera kusiya kusuta. Ndipo m’zaka 6 zapitazo, makampaniwa awonjezera kwambiri mankhwalawa m’ndudu zawo,” inatero nyuzi ina (The New York Times). Posachedwapa, atafufuza bwinobwino apeza kuti makampani opanga ndudu akuyesetsa kupanga nduduzo m’njira yoti “achinyamata ambiri akangolawa fodyayo, akopekeretu nthawi yomweyo, ndiponso kuti achikulire amene amasuta, alephere kusiya.” Pakafukufukuyu anapeza kuti “pafupifupi [ndudu] zonse zopangidwa ndi makampani osiyanasiyana zili ndi mankhwala opatsa chibaba ochuluka ndithu amene angathe kum’chititsa munthu kuti azilephera kusiya kusuta.”

Mkono Wochita Kupanga Wolumikizidwa ku Ubongo

Bambo wina ku United States, amene anadulidwa mikono yonse kuchipatala chifukwa choti anachita ngozi inayake, tsopano ali ndi mkono wochita kupanga. Mkono umenewu umagwira ntchito ngati mkono weniweni ndipo umachita zinthu motsogozedwa ndi ubongo wa munthuyo. Pogwiritsa ntchito mkonowo, bamboyo amatha kukwera pa makwerero, kupaka penti zinthu zosiyanasiyana, ndiponso ngakhale kukumbatira zidzukulu zake. Gulu lina lofalitsa nkhani (Cable News Network) linati: “Mkono wochita kupanga wa bamboyu uli ndi kamakina kenakake mkati mwake kamene anakalumikiza ku minyewa ndipo zimenezi zimathandiza kuti mkonowu uzichita zinthu motsogozedwa ndi ubongo. Bamboyu amatha kuganiza kuti, ‘Pinda dzanja,’ ndipo nthawi yomweyo dzanjalo limapindikadi.” Izi zimatheka chifukwa uthenga wochokera ku ubongo umafika m’minofu ya pachifuwa yomwe imayendetsa mkonowu, ndipo minyewa imatenga uthengawu kuchokera pa minofuyo n’kupita nawo m’kamakina ka mumkono kaja. Kenaka kamakinako kamachititsa kuti mkono wochita kupangawo uzipindika mofanana ndi mmene mkono weniweni umachitira.

Mitundu Yambirimbiri Yatsopano ya Zamoyo

Malinga ndi zimene nyuzi ina (Fenua Info) ya m’dziko la Tahiti inanena, chaka chilichonse, asayansi amatulukira mitundu yatsopano ya zamoyo pafupifupi 17,000. Mitundu itatu mwa inayi iliyonse ya zamoyo zotulukiridwazo ndi tizilombo monga nyerere mphemvu ndi zina zotere. Komanso pamitundu yatsopano ya zamoyozo pali mitundu 450 ya zinyama zokhala ndi fupa lamsana. Ndipo mitundu 250 ya zinyama zimenezi ndi nsomba, pomwe mitundu 20 mpaka 30 ndi zinyama zoyamwitsa. Mitundu iwiri mwa mitundu itatu iliyonse ya zinyama zoyamwitsazi ndi mbewa ndiponso mileme. Nyuzipepalayo inapitiriza kuti, “tinganene kuti mtundu watsopano umodzi wa anyani umatulukiridwa chaka chilichonse,” ndipo asayansi akuti zimenezi n’zodabwitsa kwambiri. Pamitundu yatsopano ya zamoyoyi palinso mitengo ndi zomera zina.