Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Gombe Lochititsa Chidwi la Shark Bay

Gombe Lochititsa Chidwi la Shark Bay

Gombe Lochititsa Chidwi la Shark Bay

YOLEMBEDWA KU AUSTRALIA

GOMBE la Shark Bay ndi lalikulu ndipo lili ndi madzi osaya. Gombeli lili kumadzulo kwenikweni kwa Australia, pafupifupi makilomita 650 kumpoto kwa mzinda wa Perth. Mu 1629, munthu wina wofufuza malo wa ku Holland dzina lake Francois Pelsaert anatcha malo a chipululu amenewa kuti “ndi dera lopanda zomera zilizonse.” M’kupita kwa nthawi, anthu odzaona derali analipatsa mayina akuti gombe lopanda kanthu, losathandiza, ndi logwiritsa mwala.

Koma masiku ano, anthu oposa 120,000 amadzaona gombeli chaka chilichonse. Malo amenewa ndi ochititsa chidwi kwambiri moti mu chaka cha 1991 anawaika pa mndandanda wa malo ofunika kwambiri padziko lonse. *

Malo a Zomera Ndiponso Nyama Zosiyanasiyana

Pelsaert akanayang’ana m’madzi a kugombeli, akanapeza zomera chifukwa muli malo aakulu kwambiri okhala ndi zomera zosiyanasiyana. Malo amenewa okhala ndi makilomita 4,000 ndi akulu kwambiri padziko lonse. Mwachitsanzo, malo ena a zomera m’mphepete mwa nyanja otchedwa Wooramel ndi a makilomita 130 ndipo ali kum’mawa kwa Shark Bay.

Zomera zimenezi zimatulutsa maluwa ndipo ndi chakudya cha nyama zambiri za m’madzi. Nsomba zing’onozing’ono, zina zokhala ndi chiganamba, ndi nyama zinanso zambiri za m’madzi zimapezeka m’malo otetezeka a zomera zochuluka amenewa. Nyama zina za m’madzi zimene amati ng’ombe za m’nyanja pafupifupi 10,000 zimakhalanso kumeneko chifukwa zimapezako chakudya chambiri. Nyama zolemera makilogalamu 400 zimenezi zimachita chidwi ndi zinthu ndipo si zolusa. Zimangodya zomera za m’nyanja zochulukazo zili phe ndipo nthawi zina zimakhalapo zoposa 100 nthawi imodzi. Zikuoneka kuti tsopano nyama zimenezi zimapezeka kwambiri kudera la kumpoto kwa Australia kuposa kwina kulikonse padziko lonse. Dera limeneli limachokera ku gombe la Shark Bay limene lili kumadzulo ndipo deralo limafika ku gombe la Moreton limene lili kum’mawa. *

Kugombe la Shark Bay kuli mitundu yambirimbiri ya nsomba zotchedwa shaki. Kuli mtundu wina wolusa kwambiri ndi wina umene ndi waukulu kuposa nsomba ina iliyonse, koma suvulaza anthu. Kumeneko kulinso mtundu wina wa anamgumi wotchedwa dolphin ndipo zikusonyeza kuti zimene anthu ena amanena zoti kumene kuli shaki sikupezekanso anamgumi a mtundu umenewu ndi zabodza. Ndipo akatswiri ofufuza zam’madzi aona kuti anamgumi 7 mwa 10 alionse ali ndi zipsera chifukwa cholumidwa ndi shaki. Kugombe limeneli kumapezekanso anamgumi alinunda ambiri amene amapuma pamalopo paulendo wawo wa chaka chilichonse wopita kum’mwera. Kumapezekanso akamba ambirimbiri amene amabwera pagombeli chaka ndi chaka kuti aikire mazira.

Kodi Ndi Miyaladi?

Mosiyana ndi malo ena kugombe la Shark Bay, dziwe la Hamelin, lomwe lili kum’mwera kwenikweni kwa gombeli, limaoneka ngati ndi lopanda zamoyo zilizonse. Madzi osaya ndi ofunda a m’dziweli amakhala amchere kuposa madzi ena a m’nyanja chifukwa choti sachedwa kuuluka monga nthunzi. M’mphepete mwa madzi ake muli zimene zimaoneka ngati miyala yodera. Koma mukaziyang’anitsitsa mungaone kuti “miyala” imeneyi kwenikweni ndi zinthu zinazake zopangidwa ndi tizilombo tating’ono kapena kuti ndere. Pamalo okwana mita imodzi alionse pali ndere pafupifupi mabiliyoni atatu.

Ndere zimenezi zimasakaniza zinthu zangati mamina ndi zinthu zinazake zochokera m’madzi n’kupanga simenti, imene pang’onopang’ono zimamangira nyumba yawo yooneka ngati mwalayo. Zimatenga nthawi yaitali kwambiri kuti zimange nyumbayi ndipo ikafika masentimita 30 ndiye kuti inayambika zaka 1,000 zapitazo.

Kudziwe la Hamelin kuli nyumba za ndere zimenezi zambiri ndiponso zosiyanasiyana kuposa kumalo ena alionse padziko lapansi. Ndipo kumeneko nyumba zimenezi zidakalipobe chifukwa siziwonongedwa.

Nyama Zochititsa Chidwi Kwambiri ku Shark Bay

Anthu ambiri amabwera ku Shark Bay kudzaona mtundu wa anamgumi wochititsa chidwi wa dolphin, wokhala ndi mphuno yangati botolo umene umapezeka kugombe la Monkey Mia. Gombe limeneli lili ku doko lotchedwa Denham. Monkey Mia ndi amodzi mwa malo ochepa padziko lonse kumene anamgumi amenewa nthawi zambiri amapita ku madzi osaya kuti akasewere ndi anthu. Palibe munthu amene amadziwa kuti zimenezi zinayamba liti.

Anthu ena amati m’ma 1950 anaona anamgumi amenewa akuthamangitsira nsomba kumadzi osaya. Ngakhale masiku ano, zimenezi zimachitikabe. Ndipo mwina anthu anapezerapo mwayi pa zimenezi kuti ayambe kudyetsa ndiponso kusewera ndi anamgumiwa. Mu 1964 ku Monkey Mia, msodzi wina wamkazi wa kumeneko anaponyera nsomba namgumi amene anali kusewera pafupi ndi bwato lake. Tsiku lotsatira, namgumi ameneyu, yemwe anthu anamutcha Charlie, anabweranso ndipo m’malo mom’ponyera nsomba ina, anafika pafupi n’kudya nsomba imene inali m’dzanja la msodziyo. Posapita nthawi, anzake a Charlie anabweranso.

Kuyambira nthawi imeneyo, anamgumiwo ndi ana awo akhala akusangalatsa anthu mamiliyoni ambiri amene amabwera kudzaona malo. Asangalatsanso akatswiri a sayansi ya zamoyo oposa 100 a kumayiko osiyanasiyana amene amabwera kudzaphunzira za anamgumiwo. Ndipo akatswiri aphunzira anamgumi a dolphin a kumeneko kuposa ena onse.

Masiku ano, anamgumi amenewa amabwera kugombe la Monkey Mia pafupifupi tsiku lililonse m’mawa ndipo nthawi zambiri amabwera pamodzi ndi ana awo. Anthu ambiri obwera kudzaona malo amawadikirira mwachidwi koma anthu ochepa okha ndi amene amakhala ndi mwayi wowadyetsa. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti oyang’anira malowa akuonetsetsa kuti nyamazi zisayambe kumangodalira chakudya chimenecho. Komabe, anthu onse amene amakhalapo amatha kuona bwinobwino zimene zikuchitika. Mayi wina anati: “Zingakhale bwino kwambiri anthu akanati azisangalala motere ndi nyama zonse padziko.”

Baibulo limasonyeza kuti kulakalaka kumeneko n’kofanana ndi cholinga choyambirira cha Mulungu choti nyama zonse zigonjere ndi kukhala mwamtendere ndi anthu. (Genesis 1:28) Ngati mumakonda nyama, mungasangalale kudziwa kuti cholinga cha Mulungu chidzakwaniritsidwa, ngakhale chinadodometsedwa ndi uchimo kwa nthawi yochepa. Zimenezi zidzachitika pamene Ufumu wa Mulungu, umene ndi boma la kumwamba limene wolamulira wake ndi Yesu Khristu, udzalamulire dziko lonse lapansi.—Mateyo 6:9, 10; Chivumbulutso 11:15.

Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira dziko lonse, dziko lidzakhala lamtendere ndi lokongola, lodzaza ndi zamoyo zathanzi. Posachedwapa, malo monga gombe la Shark Bay angadzakhale ndi zinthu zambiri zimene zingasangalatse anthu odzaona malowo kuposa panopa.—Salmo 145:16; Yesaya 11:6-9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Bungwe la United Nations loona za maphunziro, sayansi, ndi chikhalidwe (UNESCO) limaika malo amene ali ndi zinthu zachikhalidwe kapena zachilengedwe zofunika kwambiri pa mndandanda wake.

^ ndime 7 Nyama zotchedwa ng’ombe za m’nyanja zimenezi zili ndi mchira wosongoka wofanana ndi wa anamgumi otchedwa Dolphin. Mchira wake si wozungulira ngati umene nyama zina zofanana nazo zili nawo.

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AUSTRALIA

SHARK BAY

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Mmene gombe la Monkey Mia limaonekera mukakhala m’mwamba

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Nyama yotchedwa ng’ombe ya m’nyanja

[Mawu a Chithunzi]

© GBRMPA

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Mabiliyoni ambiri a tizilombo tating’ono timamanga nyumba zooneka ngati mwala

[Chithunzi patsamba 17]

Anamgumi a mtundu wa Dolphin amabwera nthawi zambiri kugombe la Monkey Mia

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

© GBRMPA; satellite map: Jeff Schmaltz, MODIS Rapid Response Team, NASA/GSFC

[Mawu a Chithunzi patsamba 17]

All images, except dugong, supplied courtesy Tourism Western Australia