“Izitu N’zimene Timafunikira!”
“Izitu N’zimene Timafunikira!”
Izi n’zimene mayi wina wa ku Italy ananena atalandira buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Iye anati: “Ndinalephera kudzigwira kuti ndisalire.” Ponena za kamwana kake kakakazi, mayiyu anati: “Sanadziwe kuwerenga koma akutha kukumbukira mfundo zikuluzikulu za m’nkhani za m’bukuli chifukwa cha zithunzi zake. Amamvetsera mwatcheru chifukwa choti bukuli analilemba mokhala ngati akukambirana ndi wowerengayo, motero nthawi zambiri mwanayu amalankhulapo. Imeneyi ndi mphatso yoposa mphatso zonse zimene tikanalandira.”
Bambo wina ku Italy anafotokoza kuti iyeyo ndi mkazi wake akhala akuda nkhawa poganizira zakuti mwana wawo wamwamuna adzamuuza bwanji nkhani zokhudza kugonana. Iwo anati: “Buku latsopanoli litatuluka, tinamva ngati kuti Mulungu ankaona vuto lathuli. Titaliwerenga bwinobwino, tinakhala pansi n’kumakambirana za mmene bukuli lithandizire mwana wathu kuti aziganiza kwambiri.”
Mtsikana wina ku Japan, amene anachitidwa zachipongwe ali mwana, analemba mawu otsatirawa poyamikira bukuli: “Ndinalira kwambiri ndipo ndinathokoza Yehova mobwerezabwereza. Bukuli limafotokoza mosapita m’mbali komanso molondola mavuto amene ana amalimbana nawo m’dziko loipali. Mafunso ake amathandiza mwana kuyankha mochoka pansi pamtima. Mutu 32 ndi wothandiza kwambiri poteteza ana kwa anthu oipa ofuna kuwapezerera. Buku lofotokoza zinthu mwatchutchutchu ngati limeneli likanakhalapo zaka 20 zapitazo bwenzi moyo wanga uli wabwino kwambiri.”
Mungathe kuitanitsa buku la zithunzi zokongola limeneli, lomwe lili ndi masamba 256, aakulu mofanana ndi masamba a magazini ino. Ingolembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo zitumizeni ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.