Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anakhaladi ndi Moyo Wautali Choncho?

Kodi Anakhaladi ndi Moyo Wautali Choncho?

Kodi Anakhaladi ndi Moyo Wautali Choncho?

Baibulo limati Adamu anakhala ndi moyo kwa zaka 930, Seti zaka 912, ndipo Metusela zaka 969. Metuselayu anangotsala zaka 31 zokha kuti akwanitse zaka 1,000. (Genesis 5:5, 8, 27) Kodi izi zinali zaka zenizeni, kapena monga ena amanenera, zinali zaka zazitali mofanana ndi miyezi ya masiku anoyi?

Umboni wa m’Baibulo momwemo umasonyeza kuti izi zinali zaka zenizeni zofanana ndi zaka za masiku anozi. Taganizirani izi: Ngati zaka za nthawi imeneyo zikanakhala zofanana ndi miyezi ya masiku ano, ndiye kuti anthu otsatirawa anakhala ndi ana ali aang’ono zedi: Kenani akanakhala ali ndi zaka 6, ndipo Mahalalele ndi Enoke akanakhala ali ndi zaka zongopitirira zisanu.—Genesis 5:12, 15, 21.

Komanso anthu akale ankatha kusiyanitsa pakati pa masiku, miyezi, ndiponso zaka. (Genesis 1:14-16; 8:13) Ndipotu nkhani ya Nowa n’njolembedwa motsatirika bwino zedi, moti imatithandiza kudziwa utali wa miyezi ya nthawi imeneyo. Tikayerekezera Genesis 7:11, 24 ndi Genesis 8:3, 4 timaona kuti miyezi isanu, kuchokera pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri kufika pa 17 pa mwezi wa chiseveni, panali masiku 150. Zikuoneka kuti mwezi umene Nowa ankatchula unali wa masiku 30, ndipo miyezi 12 yotereyi inkapanga chaka.—Genesis 8:5-13. *

Koma kodi zingatheke bwanji kuti anthu akhale ndi moyo kwa zaka mpaka 900 kapena kuposa? Baibulo limatiuza kuti Mulungu anapanga anthu kuti akhale ndi moyo wosatha. Limatinso uchimo wa Adamu unachititsa anthu kukhala opanda ungwiro ndiponso kuti azifa. (Genesis 2:17; 3:17-19; Aroma 5:12) Anthu amene anakhalapo nthawi ya Chigumula isanafike anali oyandikana kwambiri ndi nthawi imene anthu anali angwiro kusiyana ndi ifeyo, ndipo n’zosakayikitsa kuti zimenezi zinathandiza kwambiri kuti akhale ndi moyo wautali. Chitsanzo ndi Metusela. Kuchokera panthawi imene Adamu analengedwa panangodutsa mibadwo 7 yokha kuti iyeyu abadwe.—Luka 3:37, 38.

Koma posachedwapa, Yehova Mulungu adzachotsa kavuto kalikonse m’matupi mwa anthu onse amene amakhulupirira magazi amene Mwana wake Yesu Khristu anakhetsa. “Malipiro a uchimo ndiwo imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndiyo moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Inde, posachedwapa, zaka 969 zimene Metusela anakhala zizidzaoneka ngati zochepa kwambiri!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani buku la Insight on the Scriptures, Volume 2, tsamba 1214, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

1000

Metusela

Adamu

Seti

900

 

 

 

800

 

 

 

700

 

 

 

600

 

 

 

500

 

 

 

400

 

 

 

300

 

 

 

200

 

 

 

100

Anthu ambiri masiku ano