Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli ndi Vuto Losiyanitsa Mitundu?

Kodi Muli ndi Vuto Losiyanitsa Mitundu?

Kodi Muli ndi Vuto Losiyanitsa Mitundu?

Rodney anati: “Ndikavala, mkazi wanga amaonetsetsa kuti mitundu ya zomwe ndavala ikugwirizana bwino. Tikamadya m’mawa, amandisankhira zipatso chifukwa sindingazindikire ngati zili zakupsa. Kuntchito ndimavutika kuti ndisankhe chizindikiro cholondola pakompyuta, popeza kuti zizindikirozo nthawi zambiri amazisiyanitsa ndi mitundu yosiyanasiyana. Ndikamayendetsa galimoto, maloboti ofiira ndi obiriwira amaoneka chimodzimodzi, choncho ndimangoona ngati limene likuyaka ndi lapamwamba kapena lapansi. Koma maloboti akakhala opingasa, zimandivuta kwambiri.”

RODNEY ali ndi vuto losiyanitsa mitundu. Anatengera kwa makolo ake vuto limene limapangitsa mbali ya diso imene kuwala kumafikirapo kuti isagwire bwino ntchito. Si Rodney yekha amene ali ndi vuto limeneli. Mwamuna mmodzi mwa amuna 12 aliwonse amene makolo awo ena anali a ku Ulaya ndiponso pafupifupi mkazi mmodzi mwa akazi 200 aliwonse, ali ndi vutoli. * Rodney ndiponso anthu ena ambiri amene ali ndi vutoli, amatha kuona mitundu ina yosiyanasiyana, osati chabe mtundu wakuda ndi woyera. Koma saona mitundu ina bwinobwino monga mmene anthu opanda vutoli amaonera.

Mbali imene pamafikira kuwala m’diso la munthu ili ndi maselo osongoka a magulu atatu, omwe amatha kuzindikira mitundu. Gulu lililonse limatha kuzindikira kuwala kwa mtundu umodzi mwa mitundu ikuluikulu yomwe ndi wobiriwira, wofiira, ndi wabluu. Kuwala kwa mitundu yosiyanasiyana kumachititsa maselo omwe amazindikira mitunduyo kudziwitsa ubongo ndipo kenako munthu amatha kuona mitundu imeneyo. * Koma anthu amene ali ndi vuto losiyanitsa mitundu, maselo awo ndi ofooka kapena sagwira bwino ntchito ndipo satha kuzindikira bwino mitundu. Anthu ambiri amene ali ndi vuto limeneli amavutika kusiyanitsa pakati pa mitundu yachikasu, yobiriwira, yofiira, yaolenji, ndi yabulawuni. Munthu amene ali ndi vutoli satha kuona chuku chobiriwira pabuledi wabulawuni kapena patchizi chachikasu ndipo satha kusiyanitsa pakati pa mzungu wa tsitsi loyera ndi maso abluu ndi wa tsitsi lofiira ndi maso obiriwira. Ngati maselo ozindikira mtundu wofiira ndi ofooka kwambiri, munthu amaona duwa lofiira ngati lakuda. Koma anthu ambiri amene ali ndi vutoli amatha kuzindikira mtundu wabluu.

Ana Akakhala ndi Vuto Losiyanitsa Mitundu

Anthu ambiri amene ali ndi vuto losiyanitsa mitundu anabadwa nalo ndipo anatengera kwa makolo awo. Koma ana ambiri amene ali ndi vutoli, mosazindikira amaphunzira mmene angadziwire mitundu. Mwachitsanzo, ngakhale kuti satha kusiyanitsa mitundu ina, angathe kuona kuwala kosiyana kwa mitundu imeneyo ndipo amagwirizanitsa kuwalako ndi maina a mitunduyo. Angaphunzirenso kusiyanitsa zinthu mwakuona mmene zinthuzo anazipangira m’malo mosiyanitsa ndi mtundu wake. Ndipotu, ana ambiri amangokula osadziwa kuti ali ndi vuto limeneli.

Kusukulu zambiri, makamaka m’makalasi ang’onoang’ono, amagwiritsa ntchito zinthu zophunzitsira zokhala ndi mitundu yosiyanasiyana. Chifukwa cha zimenezi, makolo ndiponso aphunzitsi angaganize molakwa kuti mwana amavutika kuphunzira koma kwenikweni ali ndi vuto losiyanitsa mitundu. Mphunzitsi wina analanga mwana wa zaka zisanu chifukwa chojambula chithunzi cha mitambo yapinki, anthu obiriwira, ndi mitengo ya masamba abulawuni. Mitundu imeneyi ingaoneke yabwinobwino kwa mwana amene ali ndi vuto losiyanitsa mitundu. Choncho, n’zomveka kuti maboma ena amalimbikitsa kuti nthawi ndi nthawi ana aang’ono azikapimidwa maso.

Ngakhale kuti palibe njira yothetsera vutoli, munthu akamakula vuto limeneli siliipiraipira kapena kuyambitsa mavuto ena amaso. * Komabe, vuto losatha kusiyanitsa mitundu ndi lokhumudwitsa kwambiri. Ngakhale zili choncho, Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira dziko lonse, Yesu Khristu adzachotsa kupanda ungwiro mwa anthu oopa Mulungu. Choncho nthawi imeneyo, anthu amene anali ndi vuto lililonse la maso adzaona ulemerero wonse wa chilengedwe cha Yehova.—Yesaya 35:5; Mateyo 15:30, 31; Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Anthu a mafuko onse angakhale ndi vuto losiyanitsa mitundu, koma vutoli n’lofala kwambiri kwa Azungu.

^ ndime 4 Nyama zambiri zimatha kusiyanitsa mitundu, ngakhale kuti zimaona mitunduyo mosiyana ndi mmene ife timaonera. Mwachitsanzo, agalu ali ndi magulu awiri okha a maselo ozindikira mitundu m’maso mwawo. Ali ndi gulu lozindikira mtundu wabluu ndiponso gulu lina lozindikira mtundu wa pakati pa kufiira ndi kubiriwira. Koma mbalame zina, zili ndi magulu anayi a maselo ozindikira mitundu ndipo zingathe kuzindikira mitundu ya kuwala imene anthu satha kuzindikira.

^ ndime 8 Nthawi zina matenda ndi amene amayambitsa vuto losiyanitsa mitundu. Choncho mukaona kuti mwayamba kuvutika kusiyanitsa mitundu, mungachite bwino kukaonana ndi dokotala wamaso.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

NJIRA ZOPIMIRA VUTOLI

Kuti adziwe vuto losiyanitsa mitundu limene munthu ali nalo, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito zithunzi za madontho a mitundu yosiyanasiyana. Njira imene amagwiritsa ntchito kwambiri ndi ya Ishihara yomwe ili ndi zithunzi zosiyanasiyana zokwana 38. Mwachitsanzo, munthu yemwe maso ake ali bwinobwino akaona china mwa zithunzizi masana, amaona 42 ndi 74 (zomwe zili kumanzere). Koma munthu amene ali ndi vuto limene anthu ambiri amakhala nalo, losiyanitsa mtundu wofiira ndi wobiriwira, sangaone nambala iliyonse pachithunzi chapamwamba ndipo angaone 21 pachithunzi chapansi. *

Ngati zotsatira za kuchipatala zasonyeza kuti muli ndi vutoli, dokotala wamaso angakuuzeni kuti mukapimidwenso kuti adziwe ngati vutoli munalitengera kwa makolo anu kapena ngati layamba chifukwa cha zinthu zina.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Zithunzizi tangozigwiritsa ntchito monga zitsanzo. Koma mukafuna kudziwa ngati muli ndi vutoli muyenera kupita ku chipatala.

[Mawu a Chithunzi]

Color test plates on page 18: Reproduced with permission from the Pseudoisochromatic Plate Ishihara Compatible (PIPIC) Color Vision Test 24 Plate Edition by Dr. Terrace L. Waggoner/www.colorvisiontesting.com

[Bokosi patsamba 19]

AMUNA MAKAMAKA NDI AMENE AMAKHALA NDI VUTOLI

Vuto losiyanitsa mitundu limene anthu amatengera kwa makolo limakhala mu tinthu tinatake topezeka m’maselo totchedwa X (X chromosome). Akazi ali ndi tinthu timeneti tiwiri ta X, pamene amuna ali ndi kamodzi ka X ndi kenanso ka Y. Choncho ngati mkazi watengera kwa makolo ake kanthu ka X kamene muli vuto limeneli, kanthu ka X kena kabwinobwino kangathandize kuti asakhale ndi vutoli. Koma mwamuna amene watengera kwa makolo ake kanthu ka X kamene muli vutoli, sakhala ndi kena kamene kangam’thandize kuti asakhale ndi vuto losiyanitsa mitundu limeneli.

[Zithunzi patsamba 18]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MMENE TIMAONERA MITUNDU

Mbali ya kunja kwa diso imathandiza kuwala kuti kulowe m’maso ndipo kuwalako kumafika pa mbali ina yamkati imene imathandizanso kuti kufike pamalo pomwe pali maselo amene amatha kuzindikira kuwalako

Pamene pamalowera kuwala

Mbali yothandiza kuwala kuti kufike mkati mwa diso

Malo ofikirapo kuwala

Zinthu zimaoneka zozondoka ndiye ubongo umazikonza kuti zioneke bwinobwino

MSEMPHA WA M’MASO umadziwitsa ubongo zimene maso akuona

MALO OFIKIRAPO KUWALA pali maselo osongoka ndi maselo ooneka ngati tindodo. Maselo onsewa amathandiza kuti munthu aziona bwino

Maselo ooneka ngati tindodo

Maselo osongoka

MASELO OSONGOKA amazindikira mtundu wa kuwala wofiira, wobiriwira, kapena wabluu

Mtundu wofiira

Mtundu wobiriwira

Mtundu wabluu

[Zithunzi]

Maso amene amaona bwinobwino

Maso amene ali ndi vuto losiyanitsa mitundu