Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

FOTOKOZANI FANIZO

1. M’fanizo la Yesu la pa Luka 15:11-32, kodi mwana winayo anachita chiyani ndi chuma chimene anapatsidwa?

․․․․․

2. Kodi bambo a mwanayo anamuona bwanji pamene mwanayo analapa?

․․․․․

3. Kodi mkulu wake anamva bwanji ataona zimene bambo ake anam’chitira mng’ono wakeyu?

․․․․․

▪ Kambiranani: Kodi Yehova akufanana motani ndi bambo wa m’fanizoli? Kodi inuyo mukumva bwanji ndi zimene anachita mwana wamkulu amene sanachoke pakhomo uja?

ZINACHITIKA LITI?

Tchulani munthu kapena anthu amene analemba mabuku a m’Baibulo amene ali m’munsiwa ndipo lembani mzere kuchokera pa dzina la bukulo kufika pa chaka chimene anamaliza kulilemba.

1513 B.C.E. 1473 B.C.E. 460 B.C.E. 55-56 C.E. 60-61 C.E.

4. Yobu

5. Masalmo

6. Akolose

NDINE NDANI?

7. Mzimu woipa utandionetsa masomphenya, ndinaganiza kuti Mulungu sakhulupirira atumiki ake.

NDINE NDANI?

8. Ndinachokera ku Kolose ndipo ndinapempherera molimbika mipingo ya ku Laodikaya ndi ku Herapoli.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

Tsamba 5 N’chifukwa chiyani kukhulupirira mtima wathu si chinthu chanzeru? (Yeremiya 17:․․․)

Tsamba 7 Kodi malamulo ndiponso mboni, kapena kuti zikumbutso, za Yehova zimatithandiza bwanji? (Salmo 19:․․․)

Tsamba 11 Kodi tizisamalanso za ndani? (Afilipi 2:․․․)

Tsamba 20 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu? (1 Yohane 5:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba  27)

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Anasakaza chuma chake chonse mwa kulowerera m’makhalidwe oipa.—Luka 15:11-13.

2. Anagwidwa chifundo.—Luka 15:20-24.

3. Anakwiya ndiponso anachita nsanje.—Luka 15:25-30.

4. Mose, 1473 B.C.E.

5. Davide, ana a Kora, Hemani, Asafu (ndi a m’banja mwake), Mose, Solomo, Etani, ndi enanso, 460 B.C.E.

6. Paulo, 60-61 C.E.

7. Elifazi.—Yobu 4:1, 13-18.

8. Epafura.—Akolose 4:12, 13.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Bottom circle: Image supplied courtesy Tourism Western Australia