Kodi Timangofunikira Kukhala Wabwino?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Timangofunikira Kukhala Wabwino?
MAYI wina wachitsikana dzina lake Allison anati: “Ndimayesetsa kuchita zomwe ndingathe kuti ndikhale munthu wabwino.” Mofanana ndi iyeyo, anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu amafuna tizingochita zimenezi.
Anthu ena amaona kuti ngakhale akachita tchimo lalikulu, Mulungu sadandaula nazo malinga ngati zambiri zimene amachita n’zabwino. Amaona kuti Mulungu amakonda kukhululukira anthu m’malo mowaimba mlandu.
N’zoona kuti mawu akuti “kukhala wabwino” munthu aliyense angawatanthauzire mosiyanasiyana. Koma kodi Baibulo limati chiyani? Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tisangalatse Mulungu? Kodi munthu wabwino kwa Mulungu ndi wotani?
Tizitsatira Malangizo a Mlengi Wathu
Popeza Yehova Mulungu ndiye Mlengi wathu, iye ndi amene ayenera kutipatsa malangizo a makhalidwe abwino. (Chivumbulutso 4:11) M’Baibulo, Mulungu analembamo malamulo ndi mfundo zotsogolera makhalidwe ndiponso kulambira kwathu. Mulungu anauza anthu ake kuti: “Mverani mawu anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”—Yeremiya 11:4.
Motero, ngati tikufuna kukhala munthu wabwino kwa Mulungu tifunika kuphunzira mfundo zake ndi kusintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi mfundozo. Taganizani kuti mukufuna kukhala bwenzi la munthu winawake. Choyamba mungafune kudziwa zimene iyeyo amafuna, ndiyeno mudzachita zimene zingamusangalatse. Baibulo limanena kuti mofanana ndi Abulahamu, tingakhale bwenzi la Yehova kapena kuti munthu yemwe amasangalala naye. (Yakobe 2:23) Ndipo popeza mfundo za Mulungu ndi zapamwamba, sitingayembekezere kuti iye azisinthe kuti zigwirizane ndi zimene ifeyo tikufuna.—Yesaya 55:8, 9.
Kumvera N’kofunika
Kodi n’zoona kuti Mulungu sangasangalale nafe tikamanyalanyaza malamulo ooneka ngati aang’ono? Anthu ena angaganize kuti kumvera malamulo otero n’kosafunika. Koma palibe lamulo la Mulungu limene tingalione kuti n’losafunika. Taonani kuti pa 1 Yohane 5:3, Baibulo silisiyanitsa malamulo a Mulungu, limati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa.” Tikamachita zimene tingathe kutsatira malamulo a Mulungu, timasonyeza kuti timamukonda ndi mtima wonse.—Mateyo 22:37.
Yehova si wovuta kum’sangalatsa ndipo sayembekezera kuti tizichita zinthu mwangwiro. Tikalapa zolakwa zathu mochokera pansi pamtima ndi kuyesetsa kuti tisazichitenso, iye adzatikhululukira. (Salmo 103:12-14; Machitidwe 3:19) Kodi tingasiye dala kumvera malamulo ena n’kumaganiza kuti zili bwinobwino malinga ngati tikhala omvera pa zinthu zina? Chitsanzo china cha m’Baibulo chikusonyeza kuti zimenezi n’zosatheka.
Sauli, Mfumu ya Isiraeli anasankha kumvera malamulo ena a Mulungu ndi kusiya ena. Pochita nkhondo ndi Amaleki, anauzidwa kuti asasunge ziweto zawo koma ‘aziphe.’ Ngakhale kuti anatsatira malangizo ena, Sauli sanamvere malangizo amenewo moti anasunga “nkhosa zokometsetsa, ndi ng’ombe.” N’chifukwa chiyani anatero? Iye ndi anthu ena anafuna kuti zinthu zimenezi zikhale zawo.—Mneneri Samueli atafunsa Sauli chifukwa chake sanamvere lamulo la Mulungu, Sauli anakana ndipo anati anamvera lamulolo. Anafotokoza zinthu zabwino zimene iye ndi anthu enawo anachita, ndiponso nsembe zimene anapereka kwa Mulungu. Samueli anafunsa kuti: “Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.” (1 Samueli 15:17-22) Choncho, sitingakhale wosamvera Mulungu pazinthu zina n’kumaganiza kuti zili bwinobwino chifukwa tikupereka nsembe kapena tikuchita zinthu zina zabwino.
Malamulo a Mulungu Ndi Umboni Woti Amatikonda
Yehova mwachikondi satiyembekezera kuti tizimusangalatsa m’chimbulimbuli. M’Baibulo iye amatipatsa malangizo omveka a makhalidwe abwino, ndipo zimakhala ngati akuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.” (Yesaya 30:21) Tikamatsatira malangizo ake, timapewa kugwiritsidwa mwala chifukwa chofunafuna malangizo abwino kwa anthu. Motero, tingakhulupirire kuti malangizo a Mulungu nthawi zonse amatithandiza ndipo ‘amatiphunzitsa kupindula.’—Yesaya 48:17, 18.
Kodi n’chifukwa chiyani kutsatira zimene ifeyo timaganiza kuti n’zabwino n’koopsa? Tonse ndife odzikonda mwachibadwa ndipo mtima wathu ungatinyenge. (Yeremiya 17:9) Mosavuta tingayambe kupeputsa malamulo ena a Mulungu amene timaona ngati ovuta kapena okhwimitsa zinthu.
Mwachitsanzo, anthu awiri osakwatirana angaganize kuti palibe vuto kugonana popeza sizikhudza anthu ena. Iwo angadziwe kuti zimene akuchitazo zikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo koma angaone kuti malinga ngati sizikukhudza munthu wina, Mulungu sangadane nazo. Popeza kuti akufuna kwambiri kuchita zimenezo saganiza zotsatirapo zake. Baibulo limachenjeza kuti: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”—Miyambo 14:12.
Malamulo onse a Yehova amasonyeza kuti amakonda anthu ndipo safuna kuti tizivutika. Anthu sakhala ndi moyo wosangalala chifukwa chonyalanyaza malamulo a Mulungu onena za kugonana kapena makhalidwe enanso. Ndipo moyo wa anthu ambiri wasokonekera chifukwa cha zimenezi. Koma kutsatira malamulo a Mulungu kumatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kupewa kudzivutitsa komanso kuvutitsa ena.—Salmo 19:7-11.
Ngati mukufunadi kukhala munthu wabwino kwa Mulungu, yesetsani kwambiri kutsatira malangizo ake. Mudzaona nokha kuti “malamulo [a Yehova] si olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
▪ N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo a Mlengi wathu?—Chivumbulutso 4:11.
▪ Kodi tifunikira kumvera malamulo onse a Mulungu?—1 Yohane 5:3.
▪ N’chifukwa chiyani si kwanzeru kutsatira mfundo za makhalidwe zimene ifeyo timakonda?—Miyambo 14:12; Yeremiya 17:9.
[Chithunzi patsamba 21]
Kodi muli ndi maganizo a Mulungu pankhani ya makhalidwe abwino?