Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutsogoleredwa ndi Nzeru Zapamwamba Kuposa Zachibadwa

Kutsogoleredwa ndi Nzeru Zapamwamba Kuposa Zachibadwa

Kutsogoleredwa ndi Nzeru Zapamwamba Kuposa Zachibadwa

“Ngati anthu amangoyendera zofuna zawo, ndipo alibe mfundo zimene zingawaunikire ngati zimene akuchitazo ndi zabwino kapena zoipa, malamulo amaikidwa kuti makhalidwe abwino asalowe pansi.”—ANATERO DR. DANIEL CALLAHAN.

ZINTHU zimene a Callahan anada nazo nkhawa n’zimene zikuchitika kumene. Makhalidwe abwino akulowa pansi padziko lonse ndipo maboma akukhazikitsa malamulo ambiri ndi cholinga chothetsa upandu. Pamsonkhano woyamba wonena za udindo wa amayi ku Nigeria, pulezidenti wa dzikolo ananena kuti akuda nkhawa ndi tsogolo la dziko lake. Apa sanali kunena za ndale kapena umphawi, koma za “vuto lalikulu la kulowa pansi kwa makhalidwe abwino m’banja, kuntchito, m’midzi ndi m’mizinda ndiponso m’dziko lonse.”

Pakafukufuku wina ku Britain, atafunsa amayi okwana 1,736, anapeza kuti “mabanja okhala ndi bambo, mayi ndi ana akutha chifukwa cha kulowa pansi kwa makhalidwe abwino ndiponso kuchuluka kwa mabanja a kholo limodzi.” Ku China nakonso makhalidwe abwino akulowa pansi. Magazini ya Time inanena kuti, kusiyana ndi kale anthu kumeneko amayamba kugonana ali ana ndipo amagona ndi anthu ambiri. Mtsikana wina ku China komweko anadzitama kuti anagonana ndi amuna oposa 100. Iye anati: “Moyowu ndi wanga, ndipo nditha kuchita nawo chilichonse chimene ndikufuna.”

Nawonso anthu amaudindo akutaya khalidwe lawo labwino. Javed Akbar analemba m’nyuzipepala ya Toronto Star ya ku Canada kuti: “Anthu asiya kuona atsogoleri awo ngati zitsanzo za makhalidwe abwino.” Anatinso andale, mabwana m’makampani, ngakhale atsogoleri azipembedzo “akuoneka kuti alibiretu khalidwe.”

N’chifukwa Chiyani Makhalidwe Akulowa Pansi?

Pali zinthu zambiri zimene zikuchititsa kuti makhalidwe azilowa pansi. Chimodzi ndi chakuti, anthu ali ndi mtima wosafuna kutsatira chikhalidwe. Mwachitsanzo, pakafukufuku amene anachitika kum’mwera kwa United States, ophunzira ambiri a kukoleji ananena kuti: “Palibe amene ali ndi udindo wouza mnzake kuti chabwino ndi ichi, choipa ndi chi. Aliyense amadziwa yekha.”

Munthu wina amene amalemba nkhani za ndale, dzina lake Zbigniew Brzezinski, anatchula chifukwa china. Iye analemba kuti masiku ano, anthu “amangofuna kusangalatsa mtima wawo basi, ndipo amayendera maganizo amenewa pazochita zawo zonse.” Mtima wosafuna kuuzidwa zochita, dyera, moyo wongofuna kudzisangalatsa zimaoneka ngati zabwino, koma kodi zingathandize anthu kukhala ndi moyo wosangalala ndi womvana ndi anzawo?

Yesu anati: “Nzeru imatsimikizirika kukhala yolungama mwa ntchito zake.” (Mateyo 11:19) Kodi kulowa pansi kwa makhalidwe kwathandiza anthu kukhala osangalala? Ayi. M’malo mwake, pakhala kusakhulupirirana, kusoweka kwa chitetezo, kutha kwa mabanja, ana okula popanda bambo kapena mayi, mliri wa matenda opatsirana pogonana, mimba zapathengo, mankhwala osokoneza bongo, ndi chiwawa. Zinthu zimenezi zikusonyezeratu kuti moyo wa anthu suli bwino. Wangokhala wachisoni ndi wamavuto okhaokha—Agalatiya 6:7, 8.

Yeremiya, mneneri wa Mulungu, ataona mavuto ngati amenewa kalelo, ananena mawu ouziridwa akuti: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zoonadi, Mulungu potilenga sanafune kuti tizichita zinthu tokha popanda kudalira iyeyo. Sanafune kuti tizisankha tokha kuti chabwino ndi ichi, choipa ndi ichi. Zinthu zimene ife tingati ndi zabwinobwino zitha kukhala zoipa. Pa Miyambo 14:12, Baibulo limati: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”

Mtima Wathu ndi Wonyenga

Kodi n’chifukwa chiyani timafunikira kutsogoleredwa pa nkhani ya makhalidwe? Chifukwa mtima wathu utha kutinyenga. Baibulo, pa Yeremiya 17:9, limati: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika [“wokhoza kuchita chilichonse,” NW], ndani angathe kuudziwa?” Kodi inu mungakhulupirire munthu amene mukudziwa kuti ndi wachinyengo ndipo angathe kuchita chilichonse? Simungayerekeze n’komwe! Komatu mtima wa munthu aliyense ndi wotero. N’chifukwa chake Mulungu akutichenjeza mwachikondi ndi mosapita m’mbali kuti: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.”—Miyambo 28:26.

Apa mfundo ndi yakuti: M’malo modalira nzeru zathu zopanda ungwirozi, tizitsatira nzeru yochokera kwa Mulungu ndipo idzatipulumutsa ku mavuto ambiri. Ndiponso aliyense amene akufuna, atha kupeza nzeru imeneyi mosavuta. Baibulo limati: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzam’patsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndi mosatonza.”—Yakobe 1:5.

Khulupirirani Mulungu ndi ‘Mtima Wanu Wonse’

Ponena za Mlengi wathu, Baibulo limati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Inde, Yehova ali ngati thanthwe lalikulu. Iye ndi wodalirika kwambiri ndipo angatitsogolere pamoyo wathu wauzimu komanso angatithandize kukhala ndi khalidwe labwino ngakhale ngati khalidwe la anthu likusintha. Lemba la Miyambo 3:5, 6 limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”

Zoonadi, kodi ndaninso wina angatitsogolere koposa Mlengi wathu, amene amatha kuwerenga ‘tsitsi lenilenilo la m’mutu mwathu’? (Mateyo 10:30) Iye wasonyezanso kuti ndi bwenzi lathu lenileni chifukwa amatikonda ndipo wakhala wokhulupirika kwa ife nthawi zonse ngakhale pamene sitikumvetsa mfundo zina za choonadi.—Salmo 141:5; Miyambo 27:6.

Onaninso kuti Yehova satiumiriza kugonjera malangizo ake. M’malo mwake amatilangiza mwachikondi. Iye akuti: “Ine ndine Yehova, . . . amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Kodi inuyo simukuchita chidwi ndi Mulungu wotere? Chinanso, iye watipatsa Mawu ake, Baibulo Lopatulika, lomwe ndi buku lofalitsidwa kwambiri padziko lonse lapansi kuti tisavutike kupeza nzeru zake.—2 Timoteyo 3:16.

Mawu a Mulungu Aziunikira Njira Yanu

Ponena za Malemba Opatulika, wamasalmo analemba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Nyali ya kumapazi athu imatithandiza kuona zinthu zimene zingativulaze tikaziponda, pamene nyali ya panjira pathu imaunika kutsogolo kumene tikupita. Mwachidule tingati, Mawu a Mulungu angatitsogolere pa moyo wathu mwa kutithandiza kusankha zinthu mwanzeru pankhani zilizonse zimene zingakhudze moyo wathu pakali pano ndiponso m’tsogolo.

Mwachitsanzo, taganizirani za ulaliki wa paphiri wa Yesu. M’nkhani yaifupi imeneyo, yolembedwa pa Mateyo chaputala 5 mpaka 7, Yesu Khristu analankhula za chisangalalo, chikondi, chidani, chifundo, makhalidwe abwino, pemphero, kufunafuna chuma, ndi mfundo zina zimene ndi zothandizabe mpaka pano. Mfundo zake zinali zogwira mtima mpaka “khamu la anthulo linakhudzidwa moti anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.” (Mateyo 7:28) Bwanji osapeza nthawi yowerenga nokha ulaliki umenewu? Tikukhulupirira kuti mudzaukonda kwambiri.

“Pemphanibe” Mulungu Kuti Akuthandizeni

Kunena zoona, kuchita zinthu zimene Mulungu amafuna ndi kovuta. M’pake kuti Baibulo limati tili pa nkhondo yolimbana ndi uchimo. (Aroma 7:21-24) Ngakhale zili choncho, titha kupambana nkhondoyo mothandizidwa ndi Mulungu. Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza . . . Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza.” (Luka 11:9, 10) Yehova sasiya munthu amene akuyesetsa kuyenda pa msewu wopanikiza wopita ku moyo wosatha.—Mateyo 7:13, 14.

Taganizirani chitsanzo cha Frank, amene panthawi imene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anali ndi chizolowezi chosuta fodya. Atawerenga 2 Akorinto 7:1 ndi kuona kuti chizolowezi chake chinali “choipitsa cha thupi” m’maso mwa Mulungu, anaganiza zosiya kusuta. Koma zinamuvuta kuti asiye. Tsiku lina anangopeza kuti akukwawakwawa pansi kufufuza tizidutswa ta ndudu kuti asute.

Atachita zinthu zochititsa manyazi zimenezi, Frank anazindikira kuti iye anali m’goli la ukapolo wa fodya. (Aroma 6:16) Ndiyeno, anapemphera kwa Mulungu ndi mtima wonse kuti amuthandize, anapeza mayanjano abwino mu mpingo wa Mboni za Yehova kwawo komweko, ndipo anasiya khalidwe lake loipali.—Aheberi 10:24, 25.

Thetsani Njala Yanu Yauzimu

Zimene zinachitikira Frank ndi chitsanzo chimodzi chabe chosonyeza kuti Baibulo limapereka malangizo abwino kwambiri okhudza chikhalidwe ndi moyo wauzimu. Baibulo limalimbikitsanso munthu kutsatira malangizo amenewa. N’chifukwa chake Yesu anati: “Munthu asakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”—Mateyo 4:4.

Tikamamvera Mulungu ndi kutsatira choonadi chake chamtengo wapatali, timapindula m’njira zambiri. Timakhala ndi mtima wabwino, maganizo abwino, thanzi labwino, ndi moyo wauzimu wabwino. Lemba la Salmo 19:7, 8 limati: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo . . . Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso[kuti tithe kuona zolinga za Mulungu n’kukhala ndi chiyembekezo].”

Kudzera m’Mawu ake, Yehova amatithandiza m’njira zambiri. Amatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino ndi moyo wabwino. Komanso amatiunikira kutsogolo kwathu. (Yesaya 42:9) Nkhani yotsatira ikusonyeza kuti anthu onse amene amamvera malangizo a Mulungu ali ndi tsogolo labwino kwambiri.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 4, 5]

“Kampasi” Yokusonyezani Khalidwe Labwino

Chikumbumtima ndi mphatso ya mtengo wapatali imene athu anapatsidwa. N’chifukwa chake kuyambira kalekale anthu a mitundu ndi mafuko osiyanasiyana akhala ndi malamulo achikhalidwe osasiyana kwenikweni. (Aroma 2:14, 15) Komabe, sikuti chikumbumtima chimalondola nthawi zonse, nthawi zina chimatha kusintha malinga ndi zikhulupiriro za chipembedzo chonyenga, nzeru za anthu, tsankho, ndi zikhumbo zoipa. (Yeremiya 17:9; Akolose 2:8) Choncho, monga mmene woyendetsa ndege amafunikira kusamalira ndi kukonza zipangizo zake, ifenso tifunika kusamalira ndi kukonza kampasi yathu yamakhalidwe ndi yauzimu mogwirizana ndi miyezo yolungama ya Yehova Mulungu, “woweruza wathu.” (Yesaya 33:22) Mfundo za makhalidwe zimene anthu amatsatira, zimasintha m’kupita kwa nthawi, koma miyezo yolungama ya Mulungu siisintha. Iye akutiuza kuti: “Ine Yehova sindisinthika”—Malaki 3:6.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

Malangizo Otitsogolera Kuti Tikhale ndi Moyo Wabwino

MOYO WOSANGALALA

“Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.”—MATEYO 5:3.

“Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”—MACHITIDWE 20:35.

“Osangalala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—LUKA 11:28.

KUKHULUPIRIRANA

“Aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake.”—AEFESO 4:25.

“Wakubayo asabenso.”—AEFESO 4:28.

“Ukwati ukhale wolemekezeka pakati pa onse, ndi kama wa ukwati akhale wosaipitsidwa.”—AHEBERI 13:4.

KUKHALA BWINO NDI ANZATHU

“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—MATEYO 7:12.

“[Mwamuna] akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini; . . . mkazi akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.”—AEFESO 5:33.

“Pitirizani . . . kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse.”—AKOLOSE 3:13.

KUPEWA NDI KUTHETSA MIKANGANO

“Musabwezere choipa pa choipa.”—AROMA 12:17.

“Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. . . . Sichisunga zifukwa.”—1 AKORINTO 13:4, 5.

“Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.”—AEFESO 4:26.