Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbalame Zili ndi Nzeru Zachibadwa Zodabwitsa

Mbalame Zili ndi Nzeru Zachibadwa Zodabwitsa

Mbalame Zili ndi Nzeru Zachibadwa Zodabwitsa

“Kayendedwe ka mbalame mwina tingati ndi chinthu chochititsa chidwi kwambiri pazinthu zonse zachilengedwe.”—INATERO COLLINS ATLAS OF BIRD MIGRATION.

PA December 9, 1967, munthu wina akuyendetsa ndege anaona mbalame pafupifupi 30 za mtundu wa chinsansa zikulowera ku dziko la Ireland koma zikuuluka pamwamba kwambiri mamita 8,200 kuchoka pansi. N’chifukwa chiyani zinali kuuluka pamwamba kwambiri chonchi, pamene panali pozizira kwambiri? Choyamba, zinali kufuna kupewa mvula yamatalala yomwe imakonda kugwa chapansi pake. Chachiwiri, zinali kufuna kuuluka mu mphepo yopezeka m’mwambamo imene imazithandiza kuuluka pa liwiro la makilomita pafupifupi 200 paola limodzi. Mbalamezo zinayenda ulendo wawo wamakilomita 1,300, kuchoka ku dziko Iceland kukafika ku Ireland, pafupifupi maola 7.

Ndiponso pali mbalame zina za kumadera ozizira zimene zimayenda maulendo aatali kuposa mbalame zina zonse. Mbalame zimenezi zimaswanirana kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi ku Arctic Circle, koma nthawi yozizira zimasamukira kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansi ku Antarctic. Timbalame ta kunyanja timeneti timayenda ulendo wa makilomita pakati pa 40,000 ndi 50,000 pachaka. Mtunda umenewu tingauyerekeze ndi ulendo wozungulira dziko lonse lapansi.

Mbalame zoyera zamtundu wa chumba nazonso zimaswanirana kumpoto kwa Ulaya, koma nthawi yozizira zimasamukira ku South Africa, ndipo zimayenda mtunda wa makilomita 24,000 kupita ndi kubwera. Mbalame zikwizikwi zamtunduwu zimadutsa m’dziko la Israel miyezi ya September mpaka November ndi March mpaka May, kutsatira nyengo imene inkadziwika nthawi za m’Baibulo.—Yeremiya 8:7.

Kodi ndani anazipatsa nzeru zochita zimenezo? Zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, Mulungu anafunsa Yobu, munthu wolungama, kuti: “Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako, natambasula mapiko ake kumka kum’mwera? Kodi chiwombankhanga chikwera m’mwamba pochilamulira iwe, nichimanga chisanja chake m’mwamba?” Poyankha, Yobu anatamanda Mulungu chifukwa cha nzeru zodabwitsa za mbalame ndi zinyama zina, ndipo m’pake kuti anatero.—Yobu 39:26, 27; 42:2.

Anthu Ali ndi Nzeru Kuposa Mbalame

Mulungu analenga anthufe mwapamwamba kwambiri, moti sititsogoleredwa ndi chibadwa chokha ngati mbalame. M’malo mwake ife tili ndi ufulu wosankha zochita ndipo tili ndi chikumbumtima komanso mtima wachikondi. (Genesis 1:27; 1 Yohane 4:8) Chifukwa cha mphatso zimenezi, timatha kusankha kuchita zinthu zabwino zimene nthawi zina zimasonyeza chikondi ndi mtima wodzipereka.

Khalidwe la munthu kwenikweni limayambira pa mfundo zamakhalidwe kapena zikhulupiriro zimene munthu anaphunzitsidwa kapena zimene sanaphunzitsidwe kuyambira ali mwana. Ndiye chifukwa chake anthu amasiyana maganizo. Zinthu zimene ena amati ndi zabwino ena amati ndi zoipa, zimene ena amati ndi zololeka ena amati ndi zosaloleka. Kusiyana maganizo kumeneku kumayambitsa kusamvana, kusalolerana, ngakhalenso chidani makamaka pankhani ya chikhalidwe, kukonda fuko ndiponso chipembedzo.

Anthufe tikanakhala kuti timatsatira mfundo zofanana zamakhalidwe ndiponso zogwirizana ndi Baibulo, ngati mmene timatsatirira malamulo achilengedwe, dzikoli likanakhala labwino kwambiri. Koma kodi alipo amene ali ndi mphamvu ndi nzeru zokhazikitsira malamulo oti aliyense atsatire? Ngati alipo, kodi wakhazikitsa kale malamulowo kapena adzawakhazikitsa m’tsogolo? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani zotsatira.