Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muloleni Mulungu Akutsogolereni ku “Moyo Weniweni”

Muloleni Mulungu Akutsogolereni ku “Moyo Weniweni”

Muloleni Mulungu Akutsogolereni ku “Moyo Weniweni”

MUNTHU wotsogolera anzake afunika kukhala wokhulupirika. Anthu amene akudziwa Yehova, Mlembi Wamkulu wa Baibulo, amakhulupirira kuti iye ndi wodalirika kwambiri kuposa aliyense. Iye ‘sanama.’ (Tito 1:2; 2 Timoteyo 3:16) Umboni wakuti Yehova ndi wokhulupirika unaperekedwa ndi Yoswa, munthu woopa Mulungu amene anatsogolera Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Polankhula ndi anthuwo, anati: “Mudziwa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pamawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.

Kuyambira masiku a Yoswa mpaka pano, ulosi wambiri wa m’Baibulo wakwaniritsidwa. Kukwaniritsidwa kwa ulosi kumeneku ndi maziko olimba okhulupirira ulosi umene udzakwaniritsidwe m’tsogolo. Ulosi wambiri wonena za m’tsogolo, ndi wokhudza cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi ndi zimene adzachitire anthu omvera.

Kodi Kutsogoleredwa ndi Mulungu Kuli ndi Phindu Lotani?

Yehova, yemwe ndi chikondi, akufuna kuti tikhale ndi moyo wosangalala kuyambira panopa mpaka muyaya. (Yohane 17:3; 1 Yohane 4:8) Mulungu akufuna kuti tikhale ndi “moyo weniweni,” kapena kuti moyo wosatha. (1 Timoteyo 6:12, 19) Ndiye chifukwa chake Mboni za Yehova zoposa 6 miliyoni zikumvera lamulo la Mulungu ndipo zikulalikira mosangalala “uthenga wabwino . . . wa ufumu” kwa anansi awo. (Mateyo 24:14) Pakali pano zikuchita ntchito imeneyi m’mayiko 235, kapena kuti m’mitundu yonse ya padziko lapansi.

Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba ndipo Yesu Khristu ndiye wolamulira wake. (Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15) Muulamuliro umenewu, oipa onse amene safuna kutsatira malangizo olungama a Yehova, adzawonongedwa. (Salmo 37:10; 92:7) Kenako, dziko lonse lapansi “lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.

Tangoganizirani za mtendere ndi mgwirizano umene udzakhalepo anthu onse padziko lapansi akamadzalambira Mulungu “ndi mzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Pamapeto pake, anthu adzakhala ndi “moyo weniweni” umene Mulungu walonjeza.

Koma Malemba ananeneratu kuti, ndi anthu ochepa chabe amene adzalole kutsogoleredwa ndi Mulungu n’kupeza moyo. (Mateyo 7:13, 14) Kodi inunso mukufuna kudzapulumuka nawo? Ngati ndi choncho, Mboni za Yehova zikukupemphani kuti muphunzire nazo Malemba ndi kulola kuti Mulungu azikutsogolerani. Potero, mudzaona nokha kuti Yehova ndi wabwino. (Salmo 34:8) Mongadi mmene mbalame zimayendera motsogoleredwa ndi chibadwa chawo mpaka kukafika ku ulendo wawo, Yehova nayenso adzatsogolera anthu ake okhulupirika kulowa m’Paradaiso.—Luka 23:43.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

“Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.”—MATEYO 5:5

“Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—SALMO 37:11

“Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.”—CHIVUMBULUTSO 21:3, 4

“Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—MIYAMBO 2:21, 22