“Yehova, Ndiloleni Kuti Ndikutumikireni”
“Yehova, Ndiloleni Kuti Ndikutumikireni”
Yosimbidwa ndi Danielle Hall
Ndili mwana, ndinkakonda kwambiri agogo anga aakazi amene ankakhala pafupi ndi nyumba yathu. Tsiku lililonse masana ankakonda kugona pang’ono. Ndikapita kukawachezera nthawi imeneyi, iwo ankadzuka ndipo n’kumandiwerengera nkhani za m’Baibulo titakhala pa bedi. Iwo ankakonda kundiuza kuti: “Nthawi zonse uzikumbukira kuti Yehova amakukonda. Ndipo nawenso ukamamukonda, sadzakusiya ngakhale pang’ono.” Mawu a agogowa anandikhudza mtima kwambiri ndipo sindiwaiwala.
AGOGO angawa anamwalira mu 1977, ine ndili ndi zaka zinayi. Iwo anali a Mboni za Yehova monga abale onse a bambo anga omwe ankakhala m’tauni ya Moe, m’dziko la Australia. Ngakhale kuti makolo anga sanali a Mboni, bambo ankaona kuti Mboni za Yehova ndi anthu abwino. Kenako banja lathu linasamukira m’tauni yaing’ono yotchedwa Tintenbar, yomwe ili pafupi ndi m’mphepete mwa nyanja cha ku New South Wales. Tili kumeneko, ine ndi mchimwene wanga Jamie tinkapita ku misonkhano ya a Mboni limodzi ndi bambo athu.
Ndili ndi zaka 8 makolo anga anapatukana. Bambo anabwerera ku Moe koma ine ndi Jamie tinatsala ndi mayi. Mayiwo sankakonda zophunzira Baibulo ndipo sankafuna kuti ife tipita ku misonkhano ya a Mboni. Zimenezi zinkandimvetsa chisoni kwabasi. Nthawi zonse ndinkakumbukira mawu amene ankanena
agogo anga aja chifukwa anandikhudza mtima kwambiri. Ndinkadziwa kuti ndimam’kondadi Yehova ndipo ndinkafuna kum’tumikira. Motero ndinapemphera kwa Yehovayo n’kumuuza kuti nanenso ndine Mboni. Nayenso Jamie ankamva chimodzimodzi.Kukumana ndi Mayesero Kusukulu
Kenaka, mphunzitsi wina kusukulu anauza mwana aliyense m’kalasi kuti azitchula mokweza mpingo umene amapemphera pofuna kuti mphunzitsiyo alembe m’buku mwake. Mchimwene wanga Jamie, itafika nthawi yake ananena momveka bwino kuti: “Mboni za Yehova!” Mphunzitsiyo anadabwa kwambiri ndipo anamuuza Jamie kuti abwerezenso. Jamie anabwerezadi. Kenaka mphunzitsiyo anati: “N’zosatheka zimenezo, koma tikambiranabe.” Itafika nthawi yanga, ndinanenanso mokuwa kuti: “Mboni za Yehova!” Mphunzitsiyo ataipidwa, anakauza mphunzitsi wamkulu pasukuluyi.
Mphunzitsi wamkuluyo ananena mwamphamvu kuti: “Buku la mayina a ana onse ndi ili. Makolo anu sanalembetse kuti ndinu a Mboni za Yehova.” Ifeyo tinayankha mwaulemu kuti: “Koma umenewutu ndiye mpingo wathu.” Zitatero, mphunzitsi wamkuluyo ngakhalenso aphunzitsi athu aja sanaiyambitsenso nkhaniyi.
Kusukulu ndinayesetsa kuuza anzanga zinthu zochepa za m’Baibulo zimene ndinkadziwa. Ndinkatenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, * motero nthawi zambiri ndinkamuwerengera mtsikana winawake amene ankakonda za mawu a Mulungu. Koma chifukwa choti ndinkayesetsa kutsatira makhalidwe achikhristu, ana ambiri sankagwirizana nane, ndipo nthawi zina ndinkasungulumwa kwambiri.
Kawirikawiri ndinkapemphera kwambiri kuti Yehova akhale bwenzi langa lapamtima. Tsiku lililonse ndikaweruka ku sukulu, ndinkakhala pa bedi n’kumuuza Yehova mwatsatanetsatane, zonse zimene zachitika tsiku limenelo. Nthawi zambiri ndinkalira. Misozi ili chuchuchu, ndinam’pempha Yehova kuti: “Chonde Yehova, ndiloleni kuti ndikutumikireni limodzi ndi anthu anu.” Nthawi zonse ndikamaliza kupemphera ndinkamva bwino kwambiri.
Kalata Yolimbikitsa
Ndili ndi zaka teni, Jamie anabwereranso ku Moe kukakhala ndi bambo. Panthawiyi ndinakhaliratu ndekhandekha popanda munthu wolimbikitsana naye mwauzimu. Kenaka nditapita ku nyumba yoyandikana nayo, ndinapezako magazini angapo ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Msangamsanga ndinaloweza adiresi ya nthambi ya m’dziko lathu n’kuthamangira ku nyumba kukailemba. Ndinalemba kalata yokhudza mtima kuofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, yofotokoza za moyo wanga panthawiyo ndi kupempha kuti andithandize mwauzimu. Kalata yawo yondiyankha, yomwe inali ya masamba awiri, inandikhudza mtima kwambiri moti mpaka ndinalira. Umenewu unali umboni woti Yehova ankandiona kuti ineyo pandekha ndine munthu wamtengo wapatali.
Kalatayo inandilimbikitsa kutengera chitsanzo cha m’Baibulo cha chikhulupiriro cha mtsikana wamng’ono wa ku Isiraeli amene anakhala wantchito wa Namani, kazembe wa asilikali wa ku Suriya. Ngakhale kuti anali ku ukapolo ndiponso anali kutali kwambiri ndi kwawo, iye anayandikirabe kwa Yehova Mulungu. Ndipo anasonyeza kuti anali mboni yake yeniyeni ponena za chikhulupiriro chake molimba mtima.—2 Mafumu 5:1-4.
Kalata yochokera ku ofesi ya nthambiyo inanenanso kuti: “Poti udakali mwana, uzitumikira Yehova pomvera makolo ako ndi polimbikira sukulu. Komanso, uziyandikira kwa Yehova popemphera ndi pophunzira.” Potsiriza, kalatayo inati: “Danielle, kumbukira kuti zilibe kanthu kuti tili kuti, Yehova amakhala nafe pafupi nthawi zonse. Tikudziwa kuti zimenezi iweyo umazikhulupirira.” (Aroma 8:35-39) Kalata imeneyi ndinaisunga m’kati mwa chikuto chakutsogolo cha Baibulo langa ndipo tsopano inaperepeseka. Ndakhala ndikuiwerenga kuyambira m’mbuyo monsemu ndipo nthawi zonse ndikamaiwerenga ndimalira.
Posakhalitsa, ndinalandira kalata ina. Inanena kuti bambo anga anakonza zoti ndizilandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! papositi. Apatu ndinasangalala mosaneneka! Panthawiyi ndinayamba kukhala ndi chakudya chauzimu nthawi zonse. Magazini iliyonse ikafika, ndinkawerenga nkhani iliyonse. Ena mwa magazini amtengo apataliwa
ndidakali nawo mpaka panopo. Chapanthawi yomweyi, mkulu wochokera mumpingo wa m’deralo anayamba kundiyendera. Ankandilimbikitsa kwambiri ngakhale kuti sankakhalitsa.Kusintha Kunapititsa Zinthu Patsogolo
Ngakhale kuti zinthu zinayamba kundiyendera bwino mwauzimu, ndinkafunitsitsa kulambira Yehova momasuka. Motero nditafika zaka 13, ndinapempha mayi kuti ndizikakhala ndi bambo. Mayi anga ndinkawakonda kwambiri ndipo nawonso ankandikonda, komabe ndinatsimikiza kuti ndiyenera kutumikira Mulungu. Mayiwo atavomera, ndinabwerera ku Moe ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu ena a mumpingo wa kumeneko. Nawo bambo anavomera kuti ine ndi Jamie tizipita ku misonkhano yonse ya Mboni. Amboni a m’derali anachita khama kwambiri kuti atithandize. Choncho ine ndi Jamie tinapita patsogolo kwambiri mwauzimu ndipo tinabatizidwa, koma tinasiyana ndi miyezi yochepa paubatizo wathu. Apatu pemphero langa lomwe ndinayamba kupempha ndili mwana lija linayankhidwa chifukwa ndinayamba kutumikira Yehovayo pamodzi ndi anthu ake.
Panthawiyi, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi amalume anga a Philip Taylor ndi akazi awo a Lorraine. Nawonso tinali nawo mumpingo wa Moe. Banja limeneli linkanditenga ngati mwana wawo weniweni. Banjali litasamukira ku chilumba cha Bougainville, ku Papua New Guinea, n’cholinga chokatumikira kumeneku chifukwa kunali a Mboni ochepa, ndinavomera kukatumikira nawo limodzi. Panthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 15 zokha, koma bambo ndi mayi anandilola kuti ndipitebe.
Ku Bougainville ndinapitiriza sukulu yanga mwa kungowerenga mabuku pandekha kenaka n’kudzalemba mayeso. Komano, nthawi zambiri nthawi yanga inkathera polalikira. Zinali zosangalatsa kwambiri kugwira ntchito ndi amishonale komanso apainiya. Ndinali ndisanaonepo anthu odzichepetsa kwambiri ngati anthu a kumeneku, ndipo ambiri anali ofunitsitsa kwambiri kuphunzira Baibulo.
Chaka chomwecho panabuka mavuto a zandale, moti kukhala pachilumbachi kukanaika moyo wanga pachiswe. Zinandipweteka kwambiri kuchoka pachilumbachi n’kusiyana ndi anthu ake abwinowo. Pamene ndege yaing’ono imene ndinakwera inkanyamuka ndinaona amalume anga a Philip ataima pa msewu watala n’kumandibaibitsa. Ndinalira kwambiri kwinaku ndikupemphera kwa Yehova kuti andilole kuti tsiku lina ndidzatumikire kunja ngati m’mishonale.
Mapemphero Enanso Anayankhidwa
Ndinabwerera ku Australia, nditamaliza sukulu ya sekondale ndipo ndinapeza ntchito ya muofesi ku kampani ina ya zamalamulo. Panthawiyi, bambo anali atakwatiranso ndipo anali kusamalira banja lalikulu lopeza. Jamie ankakhala ndi mayi. Kwanthawi yaitali, ndinkati ndikakhalakhala kwa amayi ndinkapitanso kwa bambo. Moyo ndinkauona kuvuta kwambiri motero ndinafuna kuufewetsa poyamba kulimbikira kwambiri zolinga zanga zauzimu. Motero mu 1994, ndinalowa utumiki wa nthawi zonse ku Moe monga mpainiya.
Ndinayambanso kusangalala. Mumpingo ndinkakonda kucheza ndi achinyamata okonda zinthu zauzimu, ndipo ankandilimbikitsa kwambiri. Ndipotu mu 1996 ndinakwatiwa ndi mmodzi wa achinyamata oterewa, dzina lake Will. Iyeyu anali munthu wamtima wabwino, wodzichepetsa ndipo anali dalitso lenileni lochokera kwa Yehova.
Tinayamba kuzolowera moyo wam’banja, ndipo tinkaona kuti chimwemwe chathu sichikanaposa pamenepa. Tsiku lina, Will anafika ku nyumba atamaliza kugwira ntchito ndi woyang’anira woyendayenda amene ankayendera mipingo m’dera lathu. Iye anakhala nane pansi n’kundifunsa kuti: “Kodi ungakonde kuti tikathandize ku mpingo wina?” Nthawi yomweyo ndinavomereza mumtima mwanga. Komabe, ndinafunsa mongocheza kuti: “Kuti? Ku Vanuatu kapena ku Fiji?” Will atayankha kuti: “Ku Morwell.” Nthawi yomweyo ndinayankha kuti: “Aa, pafupi pompa?” Tinaseka ndipo nthawi yomweyo tonse tinavomereza kuti tisamukire ku mpingo woyandikana nawowu kuti tikachite upainiya.
Zaka zitatu zimene tinakhala ku Morwell, zinali zosangalatsa ndiponso zopindulitsa kwambiri. Kenaka panachitika zinthu zinanso zimene sitinali kuziyembekezera. Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Australia inatipempha kuti tikhale apainiya apadera. Kodi anatipatsa ntchito yokatumikira kuti? Ku East Timor, kadziko kakang’ono kamene kali cha kum’mawa kwa tizilumba ta ku Indonesia. M’maso mwanga munadzadza misozi. Ndinathokoza Yehova poyankha mapemphero anga onse. Yehova anandilola kuti ndizimutumikira komanso kuti ineyo pamodzi ndi mwamuna wanga nditumikire kunja kwa dziko lathu.
Kutumikira Kunja
Tinafika ku Dili, likulu la dzikolo, mu July 2003. Mpingo wa Dili unali wokhawo m’dzikolo ndipo unali ndi apainiya apadera 13 ochokera ku Australia komanso Mboni zingapo chabe za komweko. Abale ndi alongo a ku Timor anali osauka kwambiri. Ambiri anali atataya katundu wawo ndi abale awo ena pankhondo yapachiweniweni imene inatha mu 1999, pambuyo pazaka 24. Anthu ambiri anavutitsidwanso kwambiri ndi achibale awo chifukwa cha chipembedzo chawo chatsopanochi. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri komanso anali osauka, anali anthu olemera mwauzimu ndiponso osangalala.—Chivumbulutso 2:8, 9.
Tinaona kuti anthu ambiri a ku Timor anali anthu oopa Mulungu ndipo ankalemekeza Baibulo. Ndipotu pasanatenge nthawi yaitali tinapeza maphunziro ambiri a Baibulo moti sitikanatha kuwasamalira onse. Patapita nthawi, ena mwa anthu amene tinayamba kuphunzira nawo Baibulo anayamba kutumikira nafe limodzi monga abale ndi alongo athu obatizidwa. Tinasangalala kwambiri kuwaona akupita patsogolo mwauzimu.
Kenaka mu 2006, ku Dili kunayambanso chipwirikiti. Chidani cha pakati pa mafuko awiri a kumeneku chinayambitsa nkhondo. Nyumba zambiri zinawotchedwa ndipo anthu ankangotenga katundu wa m’nyumbazi. Mboni za kumeneku zinakabisala m’nyumba za apainiya apadera aja. Nyumba yathu inakhala malo ongoyembekezera a anthu othawa nkhondoyo, ndipo panthawi ina pafupifupi 100 anabwera ku nyumba kwathuko. Malo athu aakulu omwe tinkaimitsapo galimoto tinawasandutsa khitchini, malo odyera, ndiponso Nyumba ya Ufumu yongoyembekezera.
Ngakhale kuti tinkamva kulira kwa mfuti ndi mabomba chapafupi, nyumba yathu ya apainiyayo inali yotetezeka. Tonse tinamva kuti Yehova akutiteteza. Tinkayamba tsiku lililonse pokambirana lemba la m’Baibulo. Misonkhano yathu sinasinthe ayi ndipo tinkachita maphunziro a Baibulo ndi anthu achidwi.
Patatha milungu ingapo zinali zoonekeratu kuti kunali kuika moyo pachiswe ngati abale wobadwira ku m’mawa kwa dzikoli akanakhalabe m’mzinda wa Dili. Choncho abale amene amatsogolera anakonza zoti pakhale gulu lina mumzinda winanso waukulu wotchedwa Baucau, womwe uli kummawa kwa Dili. Anthu amayenda kwa maola atatu pagalimoto kuti afike ku Baucau kuchoka ku Dili. Izi ndi zomwe zinachititsa kuti Will ndi ine tisamuke.
Tinafika ku Baucau mu July 2006, patatha pafupipafupi zaka zitatu chifikireni ku East Timor. Gulu lathu latsopanolo linali ndi apainiya anayi ndiponso Mboni 6 za ku Timor. Ngakhale kuti abale ndi alongo a ku Timor anasiya katundu wawo yense ku Dili, iwo ankaonekabe osangalala. Kunena zoona, tinkawasirira chifukwa cha kudzipereka kwawo.
Panopa, Will ndi ine tikutumikirabe ku Baucau. Timasangalala kutumikira kumeneku ndipo timaona kuti limeneli ndi dalitso linanso lochokera kwa Yehova. Ndikayang’ana m’mbuyo, ndimaona kuti mawu a agogo anga anali oona. Yehova wakhala akundisamalira zaka zonsezi. Nthawi zonse ndimathokoza Yehova chifukwa chondilola kumutumikira limodzi ndi anthu ake. Ndikulakalakanso kudzaona agogo ataukitsidwa, ndipo ndidzawathokoza kwambiri chifukwa chondiuza chinsinsi chokhalira ndi moyo wosangalala ndiponso wopindulitsa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 26]
Ndili m’manja mwa agogo anga
[Chithunzi pamasamba 28, 29]
Ndili ndi mwamuna wanga Will