Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Maria Cino yemwe ndi nduna yogwirizira yoona za maulendo ku America anati: “Kuledzera n’kumayendetsa galimoto n’chimodzi mwa zinthu zomwe zikupha anthu ambiri.” Mu 2005, ngozi 39 mwa ngozi za pamsewu 100 zilizonse kumeneko, zinachitika chifukwa choti oyendetsawo analedzera.—ZACHOKERA KU BUNGWE LA U.S. DEPARTMENT OF TRANSPORTATION.
▪ “Pakilomita iliyonse ya panyanja, pamapezeka timapepala ta pulasitiki toposa 18,000 tikuyandama.”—ZACHOKERA KU BUNGWE LA UNITED NATIONS ENVIRONMENT PROGRAMME.
▪ “Anthu a ku America amaononga maola okwana theka la biliyoni pachaka akuchita masewera a pa kompyuta nthawi yantchito ndipo zimenezi zimachititsa kuti ndalama zokwana madola 10 biliyoni zilowe m’madzi.” Nthawi imeneyi sikuphatikizapo “nthawi yomwe amaononga pa Intaneti akuchita zinthu zawo zosagwirizana ndi ntchito.”—ZACHOKERA KU BUNGWE LA MANAGEMENT-ISSUES.
Ana Akuchitiridwa Nkhanza
Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linati: “Kwa ana ambiri kuchitidwa zachiwawa kwangosanduka mbali ya moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.” Lipoti laposachedwapa la mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations linati, “pafupifupi ana 53,000 padziko lonse anafa mochita kuphedwa m’chaka cha 2002.” Komanso ana mamiliyoni amazunzidwa pogwiritsidwa ntchito yathangata, kuwasandutsa mahule, kapena kuwajambula zinthunzi zolaula. Kodi n’zotheka kupewa nkhanza zoterezi? Lipotilo linatinso: “Njira zimene zingathandize kuti ana azitetezeka ku nyumba komanso m’malo ena ndizo kuwalera bwino, kuwakonda ndiponso kuwalangiza m’njira yowathandiza osati yowavulaza.”
Anzanu Ambiri, Moyo Wautali
Lipoti la magazini ina ya zachipatala (Journal of Epidemiology and Community Health) linati munthu angathe kukhala ndi moyo wautali kwabasi ngati ali ndi anzake ambiri apamtima. Panthawi ina ku Australia anafufuza anthu pafupifupi 1,500, a zaka 70 kapena kuposa kuti adziwe mmene kugwirizana ndi anzawo kumakhudzira kutalika kwa moyo wawo. Anthuwa anawafufuza kwa zaka 10. Ndiye anapeza kuti ambiri mwa anthu amene anali ndi anzawo ochuluka apamtima ankakhala ndi moyo wotalikirapo poyerekezera ndi ena. Lipotilo linati kukhala ndi anzawo apamtima kumathandizanso anthu okalamba kulimbana ndi “mavuto a m’maganizo, nkhawa, ndiponso kudziderera.”
Anthu Ambiri ku Britain Ali ndi Ngongole Zambiri
Nyuzipepala ina ya ku London (The Daily Telegraph) inati, “pafupifupi anthu anayi pa anthu 10 aliwonse amene ali ndi ndalama kubanki amangodalira ngongole ya kubankiko pa moyo wawo. M’malo motenga ngongole pakachitika zinazake zamwadzidzidzi, anthuwa “amangoyendera ngongole nthawi zonse” moti m’dzikoli anthu 3 miliyoni ndi theka nthawi zonse amakhala ndi ngongole kubanki. Keith Tondeur, yemwe ndi mkulu wa bungwe lophunzitsa anthu kugwiritsa ntchito bwino ndalama ananena kuti chikuchititsa vuto limeneli ndi “chikhalidwe chathu chofuna kupeza zinthu panthawi yomweyo imene tikuzifuna.” Tondeur anachenjeza kuti: “Ambiri mwa ife tikugula zinthu zimene sitingazikwanitse popanda kulowa m’ngongole ndipo popeza kuti ambirife sitinaphunzitsidwe kusamalira bwino ndalama, sitidziwa n’komwe kuchuluka kwa ndalama zimene zikuwonongeka pa moyo wathu chifukwa cha khalidweli.”
Ndege Zikamayenda Usiku Dziko Limatentha Kwambiri
Magazini ina (Scientific American) inanena kuti utsi wa ndege umene umatsala mlengalenga umachititsa kuti kuzitentha. Masana, utsiwu umachititsa kuti kutentha kwa dzuwa kuzifika kwambiri padziko lapansi ndipo mlengalenga muzizizira. Komano usiku, utsiwu umatchinga mpweya wotentha kuti usapite mlengalenga, motero kumatenthanso. Ofufuza ena a ku England anapeza kuti ndege zoyenda pakati pa 6 koloko madzulo ndi 6 koloko m’mamawa zimaonjezera kwambiri kutentha. Komatu, pa zinayi zilizonse, ndi ndege imodzi yokha yomwe imauluka panthawi imeneyi.