Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Aphunzitseni mwa Chitsanzo Chanu

Aphunzitseni mwa Chitsanzo Chanu

Mfundo 7

Aphunzitseni mwa Chitsanzo Chanu

N’chifukwa chiyani? Zochita zimaphunzitsa kuposa mawu. Nthawi zambiri mawu amangomuuza munthu zoyenera kuchita. Mwachitsanzo, makolo angathe kuuza ana awo kuti azikhala aulemu ndiponso kuti azinena zoona. Komano ngati makolo omwewo amakangana kapena kukalipira kwambiri ana awo, komanso amanena zabodza pofuna kuzemba zinthu zinazake, amaphunzitsa anawo kuti limenelo ndilo khalidwe loyenera munthu wachikulire. Ndipotu Dr. Sal Severe anati: “Imodzi mwa njira zikuluzikulu zimene ana amaphunzirira zinthu ndiyo kutsanzira makolo awo.”

Kuvuta kwake: Makolo ndi anthu opanda ungwiro. Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Anthu] onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Pankhani yolamulira zonena zathu, mtumwi Yakobe anati: “Lilime, palibe munthu ndi mmodzi yemwe angathe kuliweta.” (Yakobe 3:8) Komanso, ana amakonda kuchita zinthu zomwe zimayesa kuleza mtima kwa makolo awo. Bambo wina wa ana awiri, dzina lake Larry, yemwe ndi munthu wodziwa kuugwira mtima ananena kuti: “Ine ndine munthu wougwira mtima kwabasi, koma ana anga amandipsesabe mtima.”

Mmene mungakwanitsire: Muziyesetsa kupereka chitsanzo chabwino osati changwiro. Ndipo mukalakwitsa penapake muzipezerapo mwayi wowaphunzitsa khalidwe linalake labwino. Bambo wina wa ana awiri, dzina lake Chris, ananena kuti: “Ana anga ndikawalakwira chifukwa chopsa mtima kapena ndikalakwitsa zinazake zowakhudzanso iwowo, ndinkavomereza kuti ndalakwa, n’kuwapepesa. Pochita zimenezi ndinkawathandiza kuphunzira kuti makolo nawo amalakwitsa ndiponso kuti aliyense amafunika kuchita khama kuti akhale ndi khalidwe labwino.” Kostas, yemwe tam’tchula kale uja anati: “Ndaona kuti ana anga anaphunzira kupepesa akalakwitsa chifukwa choti inenso ndinkawapepesa ndikachita zinazake chifukwa chopsa mtima.”

Yehova Mulungu ananena kuti: “Musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” (Aefeso 6:4) Munthu wamkulu akamanena zinazake koma n’kumachita zosemphana ndi zimenezo, ana amakhumudwa nazo kwambiri, mwinanso kuposa akulu. Motero, bwanji osadzifunsa mafunso otsatirawa pamapeto a tsiku lililonse: Kodi lero lonse ndikanapanda kunena chilichonse kwa ana anga, anawo akanaphunzira chiyani pa zochita zanga zokha? Kodi zimene akanaphunzirazo ndi zimene ndimayesa kuwaphunzitsa mwa mawu?

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Kodi iwe wophunzitsa nawe, sudziphunzitsa wekha?”—Aroma 2:21

[Zithunzi patsamba 9]

Makolo akamapepesa, ana nawo amaphunzira kupepesa