Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ikani Malamulo Pakhomopo Ndipo Onetsetsani Kuti Akutsatiridwa

Ikani Malamulo Pakhomopo Ndipo Onetsetsani Kuti Akutsatiridwa

Mfundo 4

Ikani Malamulo Pakhomopo Ndipo Onetsetsani Kuti Akutsatiridwa

N’chifukwa chiyani? Ronald Simons, yemwe ndi katswiri wachikhalidwe cha anthu wa pa yunivesite ya Georgia, anati: “Ana amakula bwino makolo akamawaikira malamulo osasinthasintha ndiponso akamawalanga nthawi zonse akalephera kusunga malamulowa. Popanda dongosolo lotereli, ana amangochita zilizonse zimene akufuna, saganizira ena, ndipo sakhala osangalala. Motero anthu ena onse pakhomopo sasangalala ndi zochita za anawo.” Mawu a Mulungu amanena mwachidule kuti: “Amene aleka kukwapula mwana wake adana naye; koma wom’konda sazengereza kum’langa.”—Miyambo 13:24, Malembo Oyera.

Kuvuta kwake: Pamafunika nthawi, khama, ndiponso kupirira kuti muwaikire malire anawo ndi kuonetsetsa kuti sakuchita zinthu modutsa malirewo. Ndipo zikuoneka kuti ana ali ndi chibadwa chofuna kuyesa kudutsa malire amenewa kuti aone zimene zichitike. Mike ndi Sonia, ali ndi ana awiri ndipo ananena mwachidule vuto limeneli. Iwo anati: “Ana kwenikweni ndi anthu aang’ono okhala ndi maganizo awoawo, zofuna zawozawo ndiponso chibadwa chofuna kuchita zinthu zoipa.” Makolo amenewa amakonda kwambiri ana awo. Koma anavomereza kuti: “Nthawi zina ana amachita makani ndipo saganizira ena.”

Mmene mungakwanitsire: Tsanzirani mmene Yehova ankachitira zinthu ndi mtundu wa Isiraeli. Njira imodzi imene iye anasonyezera chikondi chake kwa anthu akewa inali yoika malamulo omveka bwino oti anthuwo azitsatira. (Eksodo 20:2-17) Iye anawauziratu chilango chimene azipatsidwa akaphwanya malamulo amenewo.—Eksodo 22:1-9.

Motero, bwanji inunso osalemba ndandanda ya malamulo amene mukuona kuti ana anu ayenera kumatsatira? Makolo ena amaona kuti ndibwino kuti ndandanda imeneyi izikhala ndi malamulo ochepa chabe, mwina asanu okha basi. Ngati ndandanda ya malamulo osankhidwa bwino oti ana azitsatira pakhomopo ili yaifupi, sizivuta kuona ngati anawo akuitsatira ndipo anawo savutika kukumbukira malamulowo. Palamulo lililonse, mulembeponso chilango chomwe mwana azipatsidwa akaphwanya lamulolo. Onetsetsani kuti chizikhala chilango choyenerera komanso onetsetsani kuti muzithadi kupereka chilangocho. Muzikambirana malamulowa nthawi ndi nthawi pofuna kuti aliyense azidziwa zoyenera kuchita, kuphatikizapo makolonu.

Wina akaphwanya malamulowo, perekani chilangocho mwamsanga, koma mosapupuluma, mosachifewetsa, ndiponso mosasintha. Komano musaiwale mfundo iyi: Mukakwiya, yembekezani kaye kuti mtima wanu ukhale m’malo. (Miyambo 29:22) Komabe, musamazengereze. Musamalole kuti akunyengerereni. Chifukwatu mukatero, ana anuwo angathe kuyamba kuona kuti n’zongosewera chabe. Zimenezi n’zofanana ndi zimene Baibulo limanena, zakuti: “Popeza sam’bwezera choipa chake posachedwa atam’tsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.”—Mlaliki 8:11.

Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene mungachite kuti muzisonyeza mphamvu zanu?

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Mateyo 5:37