Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ikani Zinthu Zoti Muzichita Nthawi Zonse

Ikani Zinthu Zoti Muzichita Nthawi Zonse

Mfundo 5

Ikani Zinthu Zoti Muzichita Nthawi Zonse

N’chifukwa chiyani? Pali zinthu zinazake zimene munthu amayenera kuzichita nthawi ndi nthawi. Zinthu zake ndi monga kupita kuntchito, kupemphera, ngakhalenso kuchita zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa. Makolo amawononga ana awo ngati sawaphunzitsa kukonza nthawi yawo mwadongosolo ndi kuchita zinthu motsatira ndandanda. Komano Dr. Laurence Steinberg, yemwe ndi pulofesa wa maphunziro a kaganizidwe ka anthu, anati: “Ofufuza apeza kuti kukhala ndi malamulo ndiponso dongosolo lochitira zinthu kumachititsa ana kuona kuti n’ngotetezeka ndipo kumawaphunzitsa kukhala odziletsa komanso otha kuchita zinthu pawokha.”

Kuvuta kwake: Moyo n’ngovuta kwambiri. Makolo ambiri amagwira ntchito kwa maola ochuluka zedi, motero kawirikawiri sakhala ndi nthawi yokwanira yokhala ndi ana awo. Pamafunika kudziletsa kuti nthawi zonse muzichita zinthu zomwe munakhazikitsa. Ndipo pamafunikanso khama kuti anawo azolowere kuchita zinthu zimenezi chifukwa poyamba amavutavuta.

Mmene mungakwanitsire: Gwiritsani ntchito mfundo imene ili m’malangizo a m’Baibulo otsatirawa: “Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akorinto 14:40) Mwachitsanzo, ana ali aang’ono kwambiri, makolo ambiri amaika nthawi yokhazikika yoti anawo azigona. Komabe, ndibwino kuonetsetsa kuti nthawi yogona izikhala yosangalatsa. Mayi wa ku Greece, yemwe ali ndi ana awiri aakazi dzina lake Tatiana, anati: “Ana anga asanagone, ndimawasisita n’kumawauza zimene ndachita patsikulo iwowo ali ku sukulu. Kenaka ndimawauza kuti andifotokozere zinthu zina zimene nawonso achita tsiku limenelo. Anawo amamasuka kwambiri. Nthawi zambiri amandiuza zakukhosi kwawo.”

Mwamuna wa Tatiana, dzina lake Kostas amawawerengera nthano anawo. Iye anati: “Anawo amanenapo maganizo awo panthanoyo ndipo nthawi zambiri amayamba kunena zakukhosi kwawo. Koma ndikangowauza anawo kuti andifotokozere zakukhosi kwawo popanda kuwawerengera nthanozo, palibe zimene amandiuza.” Inde, n’zoona kuti anawo akamakula ndibwino kusintha nthawi yawo yopita kogona. Koma mukapitiriza kuchita zinthu zoyenera kuti muzizichita nthawi zonse, anawo amapitiriza kugwiritsira ntchito nthawiyi kulankhula nanu.

Komanso ndi chinthu chanzeru kuti banja lonse lizidyera pamodzi, ngakhale kamodzi kokha patsiku. Kuti muzolowere kudyera pamodzi, m’pofunika kuti muzilolera kusintha nthawi yodyera. Bambo wina wa ana awiri aakazi, dzina lake Charles, anati: “Nthawi zina ndimafika ku nyumba mochedwa pochokera kuntchito. Pofuna kuti anawo andidikirire, mkazi wanga amangowapatsa tizakudya tongoseweretsa m’kamwa n’cholinga choti tonse pabanjapo tidyere limodzi. Timakambirana zinthu zosiyanasiyana, monga zimene tachita tsiku limenelo, mavuto athu, lemba linalake la m’Baibulo, ndipo timacheza n’kumaseka. Ndithu, chizolowezi chimenechi chathandiza kwambiri kuti banja lathu likhale losangalala.”

Kuti muzolowere njira imeneyi, musalole kuti kufuna chuma kusokoneze zinthu zimene banja lanu limayenera kuchita nthawi zonse. Tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti: “Mutsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

Kodi n’zinthu zinanso ziti zimene makolo angachite kuti ana awo azikambirana nawo momasuka?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.”—1 Akorinto 14:40