Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kulambira Mulungu Kungakhale Kosangalatsa?

Kodi Kulambira Mulungu Kungakhale Kosangalatsa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kulambira Mulungu Kungakhale Kosangalatsa?

MUNTHU wina wa tchalitchi chinachake chachikhristu analemba kuti: “Ndimakhulupirira Mulungu ndiponso ndimam’konda, koma kutchalitchi ndinatopa nako.” Kodi inunso mumaganiza choncho? Mfundo ndi yakuti, anthu ena amayamba kulambira Mulungu m’njira imene iwowo akufuna chifukwa choti kupita ku tchalitchi kumawatopetsa, sikuwakhutiritsa ndiponso chifukwa chokhumudwitsidwa.

Posachedwapa, nyuzipepala ina inanena kuti anthu ambiri masiku ano akulambira Mulungu m’njira imene iwowo akufuna. Koma anthu amene akufuna kusangalaladi polambira Mulungu, amaona kuti kulambira kotere n’kosasangalatsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kulambira kotereku angakuonenso kuti n’kosakhutiritsa ndiponso n’kogwiritsa fuwa la moto.

Motero tingafunse kuti: Kodi kulambira Mulungu m’njira yogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo n’kotopetsa ndiponso n’kosasangalatsa? Ayi sichoncho. Mwachitsanzo, taonani mawu a m’Baibulo awa amene wamasalmo wina ananena: “Tiyeni tiyimbire Yehova mokondwera. . . . Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.”—Salmo 95:1, 6.

M’nyimbo yothokoza Yehova, wamasalmo wina anayimbanso kuti: “Inu nokha, . . . ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Malemba amati Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo,” ndipo nthawi zambiri olambira ake amakhala osangalala.—Salmo 83:18; 1 Timoteyo 1:11.

Chinsinsi Chachikulu Chokhalira Osangalala

Chinsinsi chachikulu chokhalira osangalala polambira Yehova chagona pa kudziwa zimene iyeyo anachita posonyeza chikondi chake kwa ife. Kodi iye anachita chiyani? Baibulo limati: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko [anthu] mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha [Yesu Khristu], kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.

Choncho, malinga ndi mmene Baibulo limanenera, chifuniro cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:3, 4) Zimenezi sikuti zimangotanthauza kuti timangofunikira kudziwa mavesi enaake a m’Baibulo basi. M’malomwake, timafunika ‘kuzindikira tanthauzo’ la zimene tikuwerenga ndipo zimenezi zimafuna kuphunzira mwakhama. (Mateyo 15:10) Tikamachita zimenezi ‘tidzam’dziwadi Mulungu.’ Tikatero timakhala osangalala kwabasi.—Miyambo 2:1-5.

M’nthawi ya atumwi, anthu a mumzinda wa Bereya, ku Makedoniya, anakhala osangalala atachita zimenezi. Mtumwi Paulo atawaphunzitsa mawu a Mulungu, “iwowa analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho.” Anthuwa akanati aziona kuti kuphunzira Malemba n’kotopetsa, sakanakhala ndi chidwi choterechi.—Machitidwe 17:11.

Yesu ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, popeza adzakhuta.” (Mateyo 5:6) Anthu ambiri masiku ano n’ngosangalala chifukwa chakuti njala yawo yauzimu yatha. Choncho, mofanana ndi anthu a ku Bereya, “ambiri a iwo [akhala] okhulupirira.”—Machitidwe 17:12.

Njira ya Moyo

M’nthawi ya atumwi, olambira Yehova enieni anatsatira “Njirayo.” Mawu amenewa, omwe timawapeza pa Machitidwe 9:2, amatanthauza njira yatsopano ya kulambira imene Akhristu oyambirirawo anatsatira. Masiku anonso, amene akufuna kukhala osangalala polambira Mulungu ayenera kuchita chimodzimodzi. Ayenera kuganiza ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi cha m’Baibulo.

N’chifukwa chaketu mtumwi Paulo analimbikitsa anthu a ku Efeso kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale.” Komatu sizokhazo ayi. Paulo anapitiriza kuti: “[Muvale] umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona ndi kukhulupirika.”—Aefeso 4:22-24. *

Tikamamvera malangizowa, n’kusintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi zimene Mulungu amafuna, timafika pokhala osangalala kwambiri ndiponso okhutira ndi kulambira kwathu. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Paulo analembera Akhristu a ku Kolose kuti anafunika kusintha zina ndi zina m’moyo wawo “kuti [aziyenda] moyenera Yehova ndi kum’kondweretsa kwathunthu.” (Akolose 1:10) Ndithudi, kudziwa kuti Mulungu akukondwera ndi zochita zathu, n’chifukwa chomveka chokhalira osangalala. Ndipotu Mulungu amatithandiza kuti tizimukondweretsa “kwathunthu.” Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa chakuti iye amatikhululukira.

Tonsefe timachimwa, ndipo timafunikira kuti Mulungu azitikhululukira. Mawu a Paulo amene timawerenga pa 1 Timoteyo 1:15 amati: “Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa.” Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife, ndipo zimenezi zinachititsa kuti tizikhululukidwa machimo athu. Choncho, munthu amene amalambira Mulungu moona, amapepukidwa mu mtima akakhululukidwa mtolo wa machimo ake. Amakhala ndi chikumbumtima choyera ndipo amasangalala chifukwa chosakayikira kuti akamayesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna, Mulunguyo adzam’khululukira.

Chinsinsi Chinanso

Munthu sasungulumwa akangoyamba kulambira Mulungu woona. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.” (Salmo 122:1) Zoonadi, kusonkhana mokhazikika pamodzi ndi olambira oona anzathu kumatithandiza kuti tikhale osangalala.

Munthu wina ananena mawu otsatirawa atasonkhana ndi Mboni za Yehova: “Anatilandira ndi manja awiri. Anthu ake anali achifundo ndipo anatithandiza mofunitsitsa. Zimenezi zinasonyeza kuti anthuwa n’ngogwirizana zedi. Kunali ana ambiri koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene ankachita zosokoneza, ndipo zimenezi ziyenera kukhala zonyaditsa kwa iwowo ndi makolo awo omwe. Ndikuyamikira kwambiri chifukwa chondiitana ku msonkhano wosangalatsa chonchi.”

Inunso, mungasangalale chifukwa cholambira Yehova pamodzi ndi anthu ena monga mmene Davide ankachitira. Iye analimbikitsa kuti: “Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kum’yimbira mokondwera.” (Salmo 100:2) Anthu onse omwe amatumikira Mulungu moona mtima, amasangalala ndi kulambira kwawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Mungamvetse tanthauzo la kusintha kwa umunthu kumeneku powerenga Aefeso chaputala 4 ndi Akolose chaputala 3.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi chinsinsi cha kulambira koona n’chiyani?—1 Timoteyo 2:3-6.

▪ Kodi dipo la Khristu limatithandiza bwanji kukhala osangalala?—1 Timoteyo 1:15.

▪ Kodi misonkhano yachikhristu ingatithandize bwanji kuti tizisangalala polambira Mulungu?—Salmo 100:1-5.

[Chithunzi patsamba 10]

Kuphunzira Baibulo pamodzi ndi anthu ena n’kosangalatsa