Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndimakonda Nyimbo, Moyo, ndi Baibulo

Ndimakonda Nyimbo, Moyo, ndi Baibulo

Ndimakonda Nyimbo, Moyo, ndi Baibulo

Yosimbidwa Ndi Boris N. Gulashevsky

Mwamuna wina wakhungu wazaka pafupifupi 65 anadwala matenda a mtima mpaka mtima wake kusiya kugunda kawiri konse. Tsiku lina atagwada, anagwetsa misozi kuthokoza Mulungu chifukwa chomudziwa. Izi ndi zimene zinandichitikira zaka 11 zapitazo.

NDINABADWA chaka cha 1930 m’mudzi wa Tsibulev, m’boma la Cherkassy, ku Ukraine. Mu 1937, mu ulamuliro wankhanza wa Stalin, bambo anagwidwa ndipo anawapeza ndi mlandu “woukira boma.” Anatilanda nyumba ndipo anzathu ankatisala. Kenako pasanapite nthawi, ambiri a anzathuwo anamangidwanso. Nthawi imeneyo anthu anali kuopana, ankangoperekana, ndipo sanali kukhulupirirana.

Patadutsa miyezi iwiri bambo ali ku ndende m’pamene mlongo wanga Lena anabadwa. Ine, mayi, Lena, ndi mchimwene wanga Nikolai tinali kukhala m’kachipinda kakang’ono kopanda mawindo ndipo munalibenso sitovu panyengo yozizira imeneyi. Kenako, tinasamukira m’nyumba ya agogo athu. Ine ndi Nikolai tinkasamalira nyumbayo, kuwaza nkhuni, ndi kukonza zinthu zikawonongeka. Ndinkakonda kugwira ntchito zamanja. Ndinkapanga nsapato ndi kupala matabwa. Ndinkakondanso nyimbo, choncho ndinapanga ndi thabwa chida choimbira chonga gitala chotchedwa balalaika ndipo ndinaphunzira kuchiimba. Kenako ndinaphunziranso gitala ndi chida chinanso chofanana ndi gitala chotchedwa mandolin.

Ndili mwana, ndinabatizidwa m’tchalitchi cha Katolika. Koma popeza kuti ndinasokonezedwa ndi ziphunzitso ndi miyambo ya tchalitchichi, ndinayamba kukhulupirira kuti kulibe Mulungu. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, ndinalowa m’gulu la Komsomol (chipani cha achinyamata achikomyunizimu), ndipo tikapeza mpata ine ndi anzanga tinkakangana ndi anthu okhulupirira Mulungu, pofuna kuwatsutsa kuti kulibe Mulungu.

Mmene Ndinakhalira Wakhungu

Dziko la Germany litaukira dziko la Soviet Union mu 1941 pankhondo yachiwiri ya padziko lonse, asilikali akamamenyana ankadutsa m’mudzi mwathu. Pa March 16, 1944, ndinavulala kwambiri kutaphulika bomba ndipo ndinasiya kuona. Ndinatayiratu mtima ndipo ndinkamva kupweteka m’thupi.

Asilikali a ku Germany atathamangitsidwa, ndinkatha kutuluka kupita kokayenda n’kumamvetsera kulira kwa mbalame. Pondimvera chisoni, mayi ankandipatsa mowa ndipo anthu ambiri ankandiitana ku mapwando awo kuti ndikawaimbire nyimbo. Ndinkasuta, ndipo ndinkamwa mowa kuti ndiiwale mavuto. Posapita nthawi ndinazindikira kuti zimenezi sizingandithandize.

Mayi anga aang’ono, amene anali mphunzitsi, anamva zoti kuli sukulu ya anthu akhungu ndipo analimbikitsa mayi anga kukandilembetsa. Mu 1946, ndinasangalala kuyamba sukulu kudera limene panopo limatchedwa Kam’yanets’-Podil’s’kyy. Ndinaphunzira kuwerenga ndi kulemba zilembo za anthu akhungu. Ndinapitirizanso kuphunzira nyimbo, ndipo ndinkatha maola ambiri kuphunzira kuimba kakodiyoni kakang’ono. Ataona khama langa, wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu anandilola kuti ndiziimba kodiyoni yake. Ndinaphunziranso kuimba piyano.

Ndinakhala ndi Nyumba Yanga

Mu 1948, ndinakwatira mphunzitsi wina pasukulupo, yemwe poyamba ankandithandiza pa maphunziro anga. Mwamuna wake anamwalira pa nkhondo ndi kumusiya ali ndi ana awiri aakazi. Nditamaliza sukulu, ndinasamukira ku nyumba kwake. Ndinayesetsa kukhala mwamuna wabwino, ndipo ndinkapeza ndalama poimba nyimbo. Mu 1952, tinali ndi mwana wamwamuna.

Ndinaganiza zomanga nyumba, ndipo ndinalemba anthu ganyu yomanga maziko ndi chipupa, koma zambiri ndinachita ndekha. Popeza ndinali wakhungu, ndinkangodalira kugwira zinthu ndi kuganiza. Ndinkatenga thabwa ndi kuyamba kuligwiragwira, kenako n’kuyerekeza kuti ndikuliona. Ndikatero, ndinkapanga chimene ndikufuna, kuphatikizapo zida zamatabwa. Koma zida zachitsulo ndinkagula ku fakitale. Ndinapanga sitovu yanjerwa, mipando, ndi zinthu zina.

Gulu Loimba Zitoliro

Ndinawonjezera maphunziro anga ndi kukhala katswiri wa zoimbaimba. Nditaphunzira kuimba zida zambirimbiri, ndinaphunziranso chitoliro. Tsiku lina, ndinakonza kachitoliro kakang’ono kansungwi. Kenako, ndinaphunzira kupanga ndekha zitoliro. Masiku amenewo, akatswiri a nyimbo sanaganize kuti munthu angapange zitoliro zoimba besi. Izi zinali choncho chifukwa chakuti, kuti zitoliro ziimbe besi, zimafunika mphako yaikulu. Koma mphakonso ikakula, mawu abesi sangamveke kwambiri. Ichi n’chifukwa chake kunalibe gulu loimba zitoliro.

Ngakhale zinali choncho, ndinatha kupanga chitoliro chapadera chokhala ndi mphako yowonjezera mphamvu ya mawu. Izi zinasonyeza kuti ndi zotheka kupanga zitoliro zotha kuimba besi ndiponso zomveka kwambiri. Kenako ndinayamba kupanga mitundu yosiyanasiyana ya zitoliro zotha kuimba chuni chosiyanasiyana.

M’mbuyomo, ndinayambitsa magulu oimba zida zozolowereka. Gulu limodzi linali la anthu akhungu okhaokha. Koma mu 1960, ndinapanga gulu loimba zitoliro zokhazokha. Limeneli linali gulu loyamba la zitoliro ku Soviet Union konse ndipo mwinanso padziko lonse.

Ndinaphunzira Malemba Koma Ndinakayikira Zinthu Zina

Mu 1960, ndinakakonzetsa zida zoimbira kwa munthu wina, amene anayamba kulankhula nane zachipembedzo. Mwachizolowezi changa, ndinakangana naye ndi kumuuza kuti kulibe Mulungu. Iye anandiuza kuti ndingomvetsera zimene iye anali kuwerenga m’Baibulo. Popeza kuti ndinali ndisanaliwerengepo, ndinamvetsera.

Ndinasangalala kwambiri kumva kuti Yakobo ankalimbikira ntchito kuti athandize banja lake. Ndinalira nditamva nkhani ya Yosefe kuti abale ake anamugulitsa kukhala kapolo, ndi za mavuto amene iye anakumana nawo, komanso zakuti anawakhululukira. (Genesis, chaputala 37, 39-45) Ndinasangalalanso kwambiri ndi lamulo lakuti, tizichitira anzathu zinthu zimene tikufuna kuti iwo atichitire. (Mateyo 7:12) Choncho, ndinayamba kudziwa Baibulo ndi kulikonda kwambiri.

Ndinayamba kupita ku tchalitchi cha Baptist ndi mnzanga uja ndipo ndinalandira Baibulo la “Chipangano Chatsopano” la anthu akhungu, lomwe ndinaliwerenga kwambiri. Komabe, ndinapeza kuti zimene linali kunena zinali zosiyana ndi zimene ankaphunzitsa kutchalitchi kuja. Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ndi Yesu ndi osiyana ndipo Mulungu ndi wamkulu kwa Yesu. (Mateyo 3:16, 17; Yohane 14:28; Machitidwe 2:32) Koma ku Baptist amaphunzitsa kuti Mulungu ndi Yesu ndi ofanana, ndipo amapanga Utatu. Ndinawerenga liwu lililonse la mu “Chipangano Chatsopano” ndi zala zanga kambirimbiri, ndipo ndinakhutira kuti m’Baibulo mulibe chiphunzitso chimenechi.

M’Baibulo lathu munali mawu akuti “helo.” Ndinayesa kuganizira za helo ngati mmene a Baptist ankaphunzitsira kuti ndi kumoto kumene anthu amazunzidwako kosatha. Zimenezi zinandichititsa mantha kwambiri. Baibulo limanena kuti Mulungu ndiye chikondi, ndipo sindinathe kumvetsa kuti iye angalenge malo amenewo. (1 Yohane 4:8) Patapita nthawi ndinayamba kukayikira kwambiri za chiphunzitso cha helo ndi ziphunzitso zinanso za a Baptist.

Moyo Wanga Unasintha Kwambiri

Pofika 1968, ana aakazi owapeza aja anali atakwatiwa ndipo nawonso anali ndi ana awo. Panthawi imeneyi, ine ndi mkazi wanga tinayamba kusamvana ndipo tinasudzulana. Ndimamva chisoni ndikakumbukira kuti sitinasonyezane chikondi ndi kuleza mtima. Kenako ndinakwatiranso kawiri konse koma maukwati onsewa anatha.

Mu 1981, ndinasamuka ku Kam’yanets’-Podil’s’kyy, kumene ndinali nditakhalako zaka 35 n’kupita ku Yoshkar-Ola, ulendo wa makilomita 600 kum’mawa kwa Moscow. Kumeneko ndinapitiriza ntchito yanga yoimba. Gulu langa lina la oimba linali ndi anthu 45 oimba zitoliro za mitundu yosiyanasiyana. Zitoliro zazing’ono zolira kwambiri zinali zazitali masentimita 20 ndi zosakwana sentimita imodzi cham’mimba mwake ndipo zazikulu kwambiri zoimba besi zinali zazitali mamita atatu ndi masentimita 20 cham’mimba mwake. Gulu lathu likamaimba, ankaliulutsa pa wailesi ndi pa TV, ndipo tinkapita kukaimba malo osiyanasiyana m’dziko lathu lonse.

Mu 1986, kunali mpikisano wa magulu oimba m’dziko lonse la Soviet Union. Pampikisano umenewu, ndinalandira setifiketi ndi mendulo chifukwa chopititsa patsogolo luso la zitoliro. Patadutsa zaka zingapo, panatulutsidwa filimu yotchedwa Solo for Pipe, or the Fairy Tale of a Musician. Nyuzipepala yakuti Mariiskaya Pravda inati: “Boris Nikolaievich Gulashevsky, mwini filimu imeneyi, analandira setifiketi yapadera chifukwa choyambitsa gulu loimba zitoliro lomwe ndi gulu loyamba kuimba zida zimenezi mu Russia monse.”

Ndinayamba Kufunafuna Choonadi

Nditasamukira ku Yoshkar-Ola, ndinalembetsa ku laibulale, kumene kunali mabuku ambiri a anthu akhungu. Ndinadziwa zambiri za ziphunzitso za Akatolika, Apentekosto, ndi Amethodist. Ndinkapitanso ku tchalitchi cha Orthodox. Koma ndinadabwa kwambiri kupeza kuti ankaphunzitsa zinthu zomwe zija ndinazimva ku tchalitchi cha Baptist, zimene ndinadziwa kale kuti si za m’Baibulo.

Alexander Men, wansembe wa tchalitchi cha Orthodox, analemba m’buku lake kuti Mulungu ali ndi dzina lake lakuti Yahweh. Anafotokozanso kuti kale kulambira kwa Ayuda kunali koyera koma kenako kunadzaipitsidwa ndi ziphunzitso zachikunja ndi kupembedza mafano. Mabuku ake anandisangalatsa kwambiri ndipo anandilimbikitsa kufunafuna choonadi.

Sindinasiye Kufunafuna Choonadi

M’gulu langa lina la oimba, munali mkazi wina dzina lake Liza, amene satha kuona bwinobwino moti pamalamulo amatengedwa kuti ndi wakhungu. Tinakwatirana mu 1990, ndipo nayenso ankakonda zinthu zauzimu. Chaka chomwecho ndinapita kukaona mayi anga, amene ankakhala ndi mlongo wanga Lena ku Baranovichi, ku Belarus. Mayi atandipempha, ndinkapita ku tchalitchi cha Katolika kumene ndinkadya misa. Imeneyi inali nthawi imene anali kusintha mfundo zachuma ndi zaboma ku Soviet Union, ndipo paulaliki wake wansembe anangolankhula zandale zokhazokha. Apanso, ndinaona kuti izi si zomwe ndinkafuna.

Mu 1994, mtima wanga unasiya kugunda kawiri konse ndipo ndinadwala kwambiri. Chaka chomwecho mayi anga anamwalira. Ngakhale ndinakumana ndi mavuto onsewa, sindinasiye kuwerenga Baibulo. Apa ndinali nditawerenga “Chipangano Chatsopano” ka 25, moti ndinasiya kuwerengetsa kuti kakwana kangati. Koma sindinasiye kuliwerenga ndipo ndinali ndi mafunso ambirimbiri. Ndinazindikira kuti sindingathe kumvetsa mfundo za m’Baibulo pandekha.

Ndinazindikira Choonadi

Mu 1996, a Mboni za Yehova anagogoda panyumba pathu ku Yoshkar-Ola. Poyamba, ndinaopa chifukwa chakuti nyuzipepala zinkalemba kuti anthu amenewa ndi ampatuko ndipo ndi oopsa. Koma kenako ndinadzifunsa kuti, ‘Angandichite chiyani amenewa?’ Ndinayamba ndi kuwafunsa kuti amati chiyani za Utatu. Iwo anayankha kuti liwulo kapena mfundo yake mulibe m’Baibulo. Ndinasangalala kwambiri kumva zimenezo chifukwa inenso ndinali ndi maganizo amenewo.

Nditawerenga lemba la Eksodo 6:3 m’Baibulo la Chirasha limenenso ndi lovomerezedwa ndi asinodi, ndinapeza dzina la Mulungu lakuti Yehova, ndipo mtima wanga unadumpha ndi chimwemwe. Ndinakhumudwa ndi chinyengo cha zipembedzo powabisira anthu dzina la Mulungu. Koma ndinasangalala kudziwa kuti a Mboni amatchedwa ndi dzina la Mlengi ndipo amauza anthu ena za dzina limenelo.—Yesaya 43:10.

Ndinawapanikiza a Mboniwo ndi mafunso. Mwachitsanzo, ndinawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani Baibulo limanena za helo? N’chifukwa chiyani Baibulo la Chirasha lotchuka kwambiri komanso lovomerezedwa ndi asinodi limanena kuti dziko lapansi lidzawotchedwa?” Ndinali ndi mafunso osatha, koma nditauzidwa mayankho ake m’Baibulo, ndinazindikira kuti ndapeza chipembedzo chimene ndinkachifuna kwa zaka zambiri. Ndinagwada uku ndikugwetsa misozi ya chisangalalo, kuthokoza Mulungu.

Posapita nthawi, a Mboni anayamba kunditengera ku misonkhano yawo. Ndinachita chidwi kuona anthu ali tcheru kumvetsera nkhani za m’Baibulo, kwinaku ali pakalapakala kutsegula Mabaibulo awo. Wokamba nkhani amati akatchula lemba la Baibulo, anthuwo ankaliyang’ana m’Baibulo mwawo. Zoterezi ndinali ndisanazionepo. Pamsonkhano umenewo, Mboni zinaimba nyimbo yotengedwa pa Yesaya 35:5 imene inayamba ndi mawu akuti: “Pomwe akhungu apenya.”

Ndinkaphunzira Baibulo ndi Mboni kanayi pamlungu. Posakhalitsa ndinamvetsa chifukwa chake Mulungu amalola mavuto ndi nkhondo komanso mmene adzathetsere mavutowo. Ndipo makamaka ndinasangalala nditadziwa lonjezo la Mulungu la Ufumu, umene udzakwaniritsa cholinga chake chakuti anthu omvera adzakhale ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Genesis 1:28; Yesaya 65:17-25; Chivumbulutso 21:1-5) Ndinayamba kumvetsa choonadi cha m’Baibulo, ndipo pa November 16, 1997, ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanga kwa Mulungu.

Ndikutumikira Mulungu Limodzi ndi Mkazi Wanga

Nditabatizidwa, Liza nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Ngakhale kuti anali kudwala matenda ofa ziwalo, anapitabe patsogolo mwauzimu ndipo anabatizidwa mu 1998. Anachita kunyamulidwa popita kumalo aubatizo komabe anali ndi cholinga chotumikira Mulungu ndi mtima wake wonse. Tinalemba dokotala amene ankamutikita minofu Liza. Ndipo mwini wakenso ankachita masewera olimbitsa thupi. M’kupita kwa nthawi anachira. Masiku ano, sikuti amangopita ku misonkhano kokha, koma amalalikiranso ku nyumba ndi nyumba ndipo amapita ngakhale kumagawo a kutali.

Tsiku lililonse ndikamapita kokalalikira, ndimapemphera kuti Mulungu andilimbikitse. Ndikamaliza kupemphera, ndimatenga ndodo yanga yoyendera ndi kunyamuka kupita kumalo okwerera basi kudzera njira imene ndinaizolowera. Ndikangomva mdidi wa munthu akubwera, ndimayambapo kukambirana naye za m’Baibulo. Ndikakwera m’basi, ndimakhala chapakatikati, ndikuyambapo kulankhula ndi anthu Mawu a Mulungu, komanso kugawira mabuku. Ndikapeza munthu wachidwi, timapatsana manambala a foni.

Osati kale kwambiri, ndinali ndi mwayi wolankhula ndi mphunzitsi wina wa nyimbo kuchipatala. Anadabwa kwambiri ndi nzeru zopezeka m’Baibulo. Mwamuna ameneyu atabwerera kwawo, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kuchipatala chomwecho, ndinakumananso ndi mkulu wapafakitale ina yemwe ali ndi mwana wakhungu. Ndinamuuza za chiyembekezo changa, ndipo anasangalala kwambiri komanso anathokoza kumva choonadi cha m’Baibulo.

Kuchokera pamene ndinabatizidwa, ndathandiza anthu 8 kukhala ofalitsa Ufumu ndipo ndaphunzitsanso Baibulo anthu ena ambiri. Yehova akupitirizabe kundithandiza ndi mkazi wanga kudzera mwa abale ndi alongo achikhristu. Iwo amatiwerengera mabuku ofotokoza Baibulo ndipo ine ndi mkazi wanga timakambirana mfundo za m’mabukuwo. Amatijambuliranso nkhani za kumisonkhano ya chigawo ndi ya mpingo. Zonsezi zatithandiza kukhomereza choonadi cha Baibulo m’mitima yathu ndi kulalikira choonadi chimenechi kwa anthu ena. Choncho, mpingo ‘umatithandiza ndi kutilimbikitsa.’—Akolose 4:11.

Ndinathera zaka zambiri pazoimbaimba, ndipo panopa ndimasangalala kuimba nyimbo za Ufumu. Ndimatha kuimba pamtima nyimbo zonse za m’buku la Chirasha la Imbirani Yehova Zitamando. Ndikukhulupirira kuti Yehova ndiye anandipeza m’dziko loipali ndi kundithandiza kutuluka mu mdima wauzimu. N’chifukwa chakenso ndikukhulupirira ndi mtima wonse kuti tsiku lina iye adzanditsegula maso n’kundichotsera mdima.

[Chithunzi patsamba 19]

Ndikuimba chitoliro chabesi

[Chithunzi patsamba 20]

Ndikuimba kodiyoni, mu 1960

[Chithunzi pamasamba 20, 21]

Gulu loimba zitoliro

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi Liza panopa