Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pakhomo Pazikhala Chikondi

Pakhomo Pazikhala Chikondi

Mfundo 2

Pakhomo Pazikhala Chikondi

N’chifukwa chiyani? Ana sakula bwino ngati sasonyezedwa chikondi. Cha m’ma 1950, katswiri wina wa sayansi ya chikhalidwe cha anthu, dzina lake M.F. Ashley Montagu analemba kuti: “Chinthu chofunika kwambiri kuti munthu akule bwino ndicho chikondi. Kuti munthu akhale wosangalala amayenera kusonyezedwa chikondi makamaka m’zaka zisanu ndi chimodzi zoyambirira za moyo wake.” Ofufuza amasiku ano amagwirizana ndi mfundo imene Montagu anatchulayi, yakuti “ana osasonyezedwa chikondi amakhala osokonezeka.”

Kuvuta kwake: Kukhala m’dziko lopanda chikondi lino kumasokoneza mgwirizano wa anthu m’banja. (2 Timoteyo 3:1-5) Mavuto a m’banja angawonjezeke chifukwa cha mavuto a zachuma ndiponso nkhawa imene mwamuna ndi mkazi amakhala nayo posamalira ana awo. Mwachitsanzo, ngati anthu okwatirana sakambirana zinthu bwinobwino, mavuto awowa angathe kukula kwambiri makamaka ngatinso akusiyana maganizo pankhani ya kulanga ana ndiponso kuwayamikira.

Mmene mungakwanitsire: Khalani ndi nthawi yocheza pamodzi ndi ana anu. Anthu okwatirana azikhalanso ndi nthawi yokhala pa awiri. (Amosi 3:3) Gwiritsani ntchito mwanzeru nthawi imene mumakhala nayo ana anu akagona. Musalole kuti TV izisokoneza nthawi yofunika kwambiri imeneyi. Musasiye kusonyezana chikondi m’banja mwanu ndipo muzitero pouzana mawu achikondi ndiponso kuchitirana zinthu mwachikondi. (Miyambo 25:11; Nyimbo ya Solomo 4:7-10) M’malo ‘momangodzudzula’ mkazi kapena mwamuna wanu, ndibwino kuyesetsa kuti tsiku lililonse muzimuyamikira.—Salmo 103:9, 10; Miyambo 31:28.

Muziuza ana anu kuti mumawakonda. Yehova Mulungu anapereka chitsanzo kwa makolo ponena poyera kuti amakonda Mwana wake, Yesu. (Mateyo 3:17; 17:5) Bambo wina wa ku Austria, dzina lake Fleck, anati: “Anatu ali ngati maluwa. Monga mmene maluwa amafunira dzuwa kuti atenthedwe, ana nawonso amafuna chikondi cha makolo kuti azimva kuti n’ngofunika m’banjamo.”

Kaya muli pabanja kapena mukulera ana nokha, mukamathandiza ana anu kukondana ndiponso kukonda Mulungu, banja lanu limakhala losangalala.

Komano kodi Mawu a Mulungu amanena chiyani pankhani ya ulamuliro wa makolo?

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Chikondi . . . ndicho chomangira umodzi changwiro.”—Akolose 3:14