Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pezani Malangizo Abwino

Pezani Malangizo Abwino

Mfundo 1

Pezani Malangizo Abwino

N’chifukwa chiyani? Makolo ena akanyamula mwana wawo wakhanda m’manja kwa nthawi yoyamba, amakhala ndi nkhawa yaikulu. Bambo wina wa ku Britain, dzina lake Brett anati: “Ndinali wosangalala kwambiri moti ndinkangoona ngati kutulo. Koma ndinalinso ndi nkhawa yaikulu poganizira za udindo umenewu, ndipo ndinkaopa kuti mwina sinditha kuukwanitsa.” Mayi wina wa ku Argentina, dzina lake Monica, anati: “Ndinkada nkhawa kwambiri poganizira kuti mwina sinditha kusamalira bwino mwana wanga. Ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi nditha kumulera bwinobwino kuti adzakhale munthu wodalirika?’”

Kodi mukutha kumvetsa chimwemwe komanso nkhawa imene makolo amenewa anali nayo? Inde, kulera mwana ndi imodzi mwa ntchito zovuta koma zosangalatsa zedi. Monga bambo wina ananenera, “muli ndi mwayi umodzi wokha wolera mwana wanu bwino.” Popeza kuti makolo angathandize kwambiri kuti ana akhale athanzi ndiponso osangalala, mungaone kuti mukufunikadi malangizo odalirika a mmene mungakwaniritsire bwino udindo wanu.

Kuvuta kwake: Zimaoneka kuti aliyense ali ndi malangizo pankhani ya kaleredwe ka ana. Kale anthu akakhala ndi mwana woyamba, ankadalira chitsanzo cha makolo awo kapena malangizo a chipembedzo chawo. Koma m’mayiko ambiri, mabanja sakuyenda bwino ndipo anthu ambiri asiya kutsatira zachipembedzo. Motero, makolo ambiri amafunsira malangizo kwa akatswiri odziwa za kulera ana. Zina mwa zinthu zimene akatswiri amenewa amanena n’zomveka ndithu. Koma nthawi zina malangizowa amakhala otsutsana ndipo sachedwa kutha ntchito.

Mmene mungakwanitsire: Funani malangizo kwa munthu amene amadziwa bwino kwambiri za kulera ana. Iyeyu ndi Mlengi wa anthu, Yehova Mulungu. (Machitidwe 17:26-28) Mawu ake Baibulo, ali ndi malangizo osapita m’mbali ndiponso zitsanzo zimene zingakuthandizeni kulera bwino ana anu. Iye analonjeza kuti: “Ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo.”—Salmo 32:8.

Kodi Mulungu amapereka malangizo otani kwa makolo, amene angawathandize kulera ana awo kuti adzakhale osangalala?

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.”—Miyambo 3:5