Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sonyezani Kuti Mukumvetsa Maganizo a Mwana Wanu

Sonyezani Kuti Mukumvetsa Maganizo a Mwana Wanu

Mfundo 6

Sonyezani Kuti Mukumvetsa Maganizo a Mwana Wanu

N’chifukwa chiyani? Ana amafuna kudziwa mmene makolo awo, omwe ndi anthu ofunikira kwambiri m’moyo wawo, amamvera za iwowo. Ngati makolo amangokhalira kukalipira ana awo, anawo sangamasuke kunena zakukhosi kwawo komanso angayambe kudzikayikira kuti sangathe kuganiza pawokha.

Kuvuta kwake: Ana amakonda kukokomeza akamanena maganizo awo ndiponso mmene akumvera. N’zoona kuti zina mwa zinthu zimene ana amanena zimaimitsa mitu makolo awo. Mwachitsanzo, mwana akapsa mtima angathe kunena kuti: “Kuli bwino ndingodzipha basi.” * Makolo ena akamva mawu ngati amenewa, amangofulumira kuyankha kuti: “Usamanene mawu amenewo, wamva?” Mwina amatero poopa kuti akasonyeza kuti akuona kuti mwanayo akunena zimenezo motsimikiza, akhala ngati kuti akum’vomereza kuti adziphedi.

Mmene mungakwanitsire: Gwiritsirani ntchito malangizo a m’Baibulo akuti tizikhala “ofulumira kumva, odekha polankhula.” (Yakobe 1:19) Onani chitsanzo cha Yehova Mulungu pankhani yomvetsera maganizo otere amene atumiki ake ambiri anali nawo. Iye anaonetsetsa kuti maganizo awowo alembedwe m’Baibulo. (Genesis 27:46; Salmo 73:12, 13) Mwachitsanzo, Yobu ali pamavuto osasimbika aja, ananena kuti ankangolakalaka atamwalira.—Yobu 14:13.

N’zodziwikiratu kuti Yobu anafunika kumuwongolera pa maganizo ake ena. Koma m’malo momuletsa kunena maganizo akewo, Yehova anam’lemekeza Yobu poleza mtima n’kumulola kuti anene zakumtima kwake. Ndipo Yobu atamaliza kunena maganizo ake onse m’pamene Yehova anamuwongolera mokoma mtima. Bambo wina wachikhristu anafotokoza zimenezi motere: “Yehova amandilola kumuuza zakukhosi kwanga zonse m’pemphero, motero inenso ndiyenera kulola ana anga kundiuza zinthu zilizonse zimene akusangalala nazo komanso zimene zikuwadetsa nkhawa.”

Nthawi ina mukadzaona kuti mwana wanu akufunika kumuuza kuti asamanene zodzipha kapena kuti asamaganizire n’komwe zimenezo, muzikumbukira lamulo lotchuka limene Yesu ananena lakuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zimenezo.” (Luka 6:31) Mwachitsanzo, taganizirani kuti winawake kuntchito kwanu wachita zokupwetekani kapena mwakhumudwa chifukwa cha zinazake, mwina zoziputa dala nokha. Ndiyeno mukuuza mnzanu wina wapamtima, kuti simutha kukwanitsa ntchito yanu. Kodi mungafune kuti mnzanuyo atani? Kodi mungafune kuti akuuzeni kuti musanene zimenezo n’kungothamangira kunena nthawi yomweyo kuti inuyo ndiye muli ndi vuto? Kapena kodi mungakonde kuti mnzanuyo anene mawu monga akuti: “Pepani, pamenepotu zinthu sizinali bwino ayi. Lero zinthu sizinakuyendereni bwino”?

Ana ndiponso akuluakulu savuta kumvera malangizo akamaona kuti munthu amene akuperekayo akuwamvetsadi ndiponso akumvetsa mavuto amene akukumana nawo. Mawu a Mulungu amati: “Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake, nuphunzitsanso milomo yake.”—Miyambo 16:23.

Kodi mungatani kuti ana anu azimvetsera malangizo onse amene mumawapatsa?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Samalani kwambiri ndi mawu aliwonse amene mwana anganene onena za kudzipha.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.”—Miyambo 18:13