Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinali ndi Cholinga Chapadera Pokaona Chilumba Chotchedwa Christmas Island

Tinali ndi Cholinga Chapadera Pokaona Chilumba Chotchedwa Christmas Island

Tinali ndi Cholinga Chapadera Pokaona Chilumba Chotchedwa Christmas Island

YOLEMBEDWA KU FIJI

CHILUMBA cha Kiritimati, chimene amachitchulanso kuti Christmas, ndi chachikulu kwambiri pa zilumba zonse 33 za m’nyanja ya Pacific zimene zapanga dziko la Kiribati. * Chilumbachi ndi chachikulu masikweya kilomita 388, ndipo kukula kwake kumafanana ndi zilumba zina zonse 32 pamodzi. Pachilumba chimenechi pali anthu pafupifupi 5,000, ndipo dziko lonse la Kiribati lili ndi anthu 92,000.

Zilumba zonse za ku Kiribati, kupatulapo chimodzi chokha, zili ndi mayiwe akuluakulu. Chilumba cha Christmas ndi chachikulu kwambiri pa zilumba zonse zokhala ndi mayiwe akuluakulu ku Kiribati komanso ndi chachikulu kwambiri pa zilumba zonse za mtunduwu padziko lonse.

Chilumba cha Christmas n’chodziwikanso kwambiri chifukwa chakuti chili pafupi ndi malo amene amayambirira kusintha deti padziko lonse otchedwa international date line. N’chifukwa chake anthu kumeneko amakhala ndi tsiku ndiponso chaka chatsopano mwamsanga kuposa anthu a kumadera ena. Ndiye kuti zinthu zimene anthu amakumbukira chaka chilichonse monga imfa ya Yesu Khristu, zimachitika mwamsanga kumeneko kusiyana ndi madera ena. *

Kuwonjezera apo, mbalame zambiri za kunyanja za kumadera otentha zimaswanirana pa chilumba chimenechi. Posachedwapa apeza kuti mbalame za kunyanja zakuda zokwana pafupifupi 25 miliyoni zimaswanirana kumeneko.

Si Chinsinsi cha Mbalame Zokha

Munthu wina wofufuza malo dzina lake James Cook anafika pa chilumba chimenechi chaka cha 1777, kutasala tsiku limodzi kuti Khirisimasi iyambe, ndipo sanapezepo munthu ngakhale mmodzi. Koma anangopezapo mbalame zambirimbiri. Iye anachipatsa chilumbachi dzina lakuti Christmas Island. * Kwa zaka zambiri, chilumbachi chinali chinsinsi cha mbalame chifukwa chakuti ndi zokhazo zimene zinkadziwa malowa.

Ulendo wina, msilikali wa bungwe loteteza zinthu zachilengedwe anationetsa malowo. Titafika ku gombe, tinaona mbalame za kunyanja zoyera zikuuluka monyada ndi mwachidwi kubwera kudzatichingamira. Zinkauluka pafupi nafe kwambiri ndipo zinkatilondola kulikonse komwe timapita.

M’mphepete mwa gombeli munali mbalame zambirimbiri zakuda za kunyanja. Mbalemezi zimabwera ku chilumbachi kudzaswa. Zikafika zimangouluka m’mwamba usana ndi usiku chapamalo amene zimaikira mazira, kudikira kuti zina zifike ndipo kenako zimatera.

Anapiye a mbalamezi amayamba kuuluka ali ndi miyezi itatu. Amati akachoka, amatha zaka zambiri asanabwerere. Amadzabwerera nawonso akadzafuna kuikira patapita zaka zapakati pa 5 ndi 7. Nthawi zambiri amakhala akungouluka m’mwamba. Sangatere ndi kuyandama m’madzi chifukwa chakuti nthenga zawo sizichedwa kunyowa.

Tinaonanso mbalame zina za mtunduwu koma zakuda, zina zikukhalira mazira zina zitaswa kale. Mbalame zakudazi zimamangira ana awo zisa koma zoyera sizimanga zisa. Zoyerazi zimaikira mazira m’nthambi za mitengo. Ubwino wake ndi wakuti ana awo amabadwa ndi zikhadabo zazikulu zimene zimawathandiza kuti asagwe mumtengo. Tinachita chidwi kwambiri kuona ana a mbalame zimenezi atamatiriramatirira ku mitengo. Makolo awonso ndi okongola ndipo amakhala oyera kwambiri komanso ali ndi milomo yaikulu yakuda.

Tikupitiriza ulendo wathu woona zinthu za pachilumbachi, tinaonanso mbalame yamtundu wina ikukhalira mazira ake pamthunzi ndipo inkatiyang’anitsitsa mwatcheru. Chilumbachi chili ndi mbalame zambiri za mtunduwu kuposa malo ena aliwonse padziko lonse. Ndipo anthu azindikira mochedwa kuti mitundu iwiri ya mbalame zinanso za kunyanja za ku Polynesia ndi za ku Phoenix zimaswanirana kumeneko. Mbalame zinanso zimene zimaswanirana kumeneko ndi mbalame za chipsepse chofiira za kumadera otentha, mbalame zamitundumitundu zimene zimakonda kujowera m’madzi, ndi mbalame za m’gulu la vuwo.

Mbalame za m’gulu la vuwo zimadziwadi kuuluka mochititsa kaso. Tinaona mbalamezi zikuuluka mwaluso popanda kukupiza mapiko awo, ndipo zimatha kuba nsomba kuchokera kwa mbalame zinzawo ndiponso zimathamangira zakudya zotayidwa ndi asodzi. Luso limeneli ndi lofunikadi kwa mbalamezi chifukwa chakuti kwenikweni sizitera m’madzi. Zili ngati mbalame zakuda za kunyanja zija m’njira yakuti nthenga zawo sizichedwa kunyowa m’madzi, koma izo zimavutikanso kunyamuka zikatera chifukwa chakuti mapiko awo ndi aatali kwambiri.

Kenako tinatulukira kuti kambalame kakang’ono kakhofi kooneka ngati chinziri kamene tinakaona kale kaja, ndi imodzi ya mbalame zoyenda maulendo ataliatali, zimene zimabwera ku chilumba cha Christmas kudzadya ndi kudzapuma m’nyengo yozizira. Zikamabwera ku chilumbachi zimakhala zitayenda ulendo wautali kuchokera kumene zimakaswanirana, ku Arctic Circle. Chifukwa cha nzeru zawo zapadera zotha kulondola malo, mbalame zimenezi zimatha kuuluka mtunda wa makilomita pafupifupi 2,100 mpaka kukafika kum’mwera kwa Honolulu, ku Hawaii.

Cholinga Chathu Chapadera

Nthawi zambiri tinkapita ku chilumba cha Christmas, osati kwenikweni kukaona mbalame, koma kukaonana ndi Mboni za Yehova zinzathu ndi kukasonkhana nazo ndiponso kukalalikira nazo limodzi. Chilumbachi chili kutali kwambiri ndipo zimenezi zili ndi mavuto ake. Mwachitsanzo, Mboni ina itamwalira zaka zingapo zapitazo, mkazi wake analimba mtima ndi kukamba yekha nkhani ya maliro chifukwa chakuti kunalibe wina aliyense amene akanakamba. Iye anafuna kuti anthu ambiri amene anabwera pa maliropo amve uthenga wa m’Baibulo wakuti akufa adzauka.—Yohane 11:25; Machitidwe 24:15.

Ngakhale kuti m’Chigibati muli mitundu itatu ya Mabaibulo omasuliridwa bwino, mabuku ofotokoza Baibulo ndi osowa. Komabe, Mboni za Yehova zimafalitsa magazini yokongola ya Nsanja ya Olonda kamodzi pamwezi m’Chigibati ndi mabuku enanso ofotokoza Baibulo. Zimenezi zimadabwitsa anthu ambiri chifukwa chakuti anthu amene amalankhula chinenero chimenechi sakwana 100,000 padziko lonse. Kagulu kakutali kameneka ka Mboni kamagwiritsa ntchito mabuku amenewa pamisonkhano yawo ndi pochita ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu imene Yesu analamula.—Mateyo 24:14; Aheberi 10:24, 25.

Alendo amavutika kuyenda ulendo wawo pachilumbachi. Ngakhale zili choncho, munthu atha kuyenda pa galimoto ulendo wochokera ku London mpaka ku Poland kudzera ku Tennessee m’maola atatu okha! Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Mayina akuti Banana, London, Paris, Poland, Tennessee, ndi Tabwakea angokhala mayina ochititsa chidwi a midzi yakomweko. Mayina amenewa amangokumbutsa anthu za malo kumene anthu oyambirira okhala m’midzi imeneyi anachokera.

Ulendo wina, dokotala wina anatikomera mtima ndi kutilola kupita naye ku Poland, ndipo zimenezi zinatipatsa mpata wolalikira. Aka kanali koyamba kulalikira kumeneko. Popeza kuti tinauzidwa kuti tikhala ku Poland maola awiri okha, tinali kuchita kuthamanga polalikira nyumba ndi nyumba ndi cholinga choti tifikire nyumba zonse. Aliyense amene tinamulalikira anasangalala ndi uthenga wa m’Baibulo ndipo analandira mabuku athu. Sanakhulupirire kuti mabuku amenewa anali m’chinenero chawo.

Timawakonda kwambiri anthu amenewa ngakhale kuti amakhala kutali kwambiri ku chilumba cha Christmas. Timakondanso kwambiri nzika zina zokongola, zokhala ndi nthenga za kuchilumba chimenechi. Kalelo James Cook ataona chilumbachi, mwina anaganiza kuti ndi malo a mbalame basi. Koma masiku ano zinthu zasintha. Anthu ambiri, mofanana ndi mbalame, amatinso kumeneko ndi kwawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Poyamba dziko la Kiribati linkatchedwa kuti Gilbert Islands. Panopa dzikoli lapangidwa ndi zilumba 16 zomwe kale zinali za ku Gilbert Islands ndi zilumba zinanso za Phoenix, Line ndi Banaba (Ocean Island).

^ ndime 5 Pomvera lamulo la Yesu, Mboni za Yehova zimakumbukira imfa ya Yesu kamodzi pachaka patsiku logwirizana ndi limene iye anafa.—Luka 22:19.

^ ndime 8 Pali chilumba chinanso chotchedwa Christmas ku nyanja ya Indian Ocean.

[Mapu patsamba 16]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Christmas Island

Banana

Tabwakea

London

Paris

Poland

International date line

[Chithunzi patsamba 16]

Mbalame za m’gulu la vuwo

[Mawu a Chithunzi]

GaryKramer.net

[Chithunzi patsamba 17]

Mbalame za kunyanja zoyera

[Mawu a Chithunzi]

©Doug Perrine/ SeaPics.com

[Chithunzi patsamba 17]

Mbalame za kunyanja zakhofi

[Mawu a Chithunzi]

Valerie & Ron Taylor/ ardea.com

[Chithunzi patsamba 18]

Tikulalikira ndi Mboni zakomweko

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

GaryKramer.net