Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubwino Wophunzitsa Ana Mawu a Mulungu

Ubwino Wophunzitsa Ana Mawu a Mulungu

Ubwino Wophunzitsa Ana Mawu a Mulungu

Makolo amene amachita khama kuphunzitsa ana awo kuyambira ali aang’ono amapindula. Mwachitsanzo, Dorian, mwana wamng’ono wa ku Peru, ku South America, anakamba nkhani yake yoyamba mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ali ndi zaka zinayi. Atayamba kupita ku sukulu, ankatha kufotokozera aphunzitsi ndi anzake chifukwa chake sakondwerera Khirisimasi powawerengera Baibulo.

Posachedwapa, ali ndi zaka zisanu, Dorian anapemphedwa kulankhula ndi ana a sukulu onse pafupifupi 500 kuti afotokoze maganizo ake pankhani ya Tsiku la Abambo. Anakonza nkhani yamphindi 10 yamutu wakuti “Udindo wa Abambo,” kuchokera m’Baibulo pa Aefeso 6:4. Pomaliza nkhani yakeyo, anati: “M’malo mokumbukira Tsiku la Abambo kamodzi pachaka, ana ayenera kumvera ndi kulemekeza makolo awo tsiku lililonse.”

Sukulu ya Utumiki wa Mulungu inayamba m’chaka cha 1943 ndi cholinga chophunzitsa ana ndi akulu omwe kulankhula bwino pagulu, ndipo yakhala ikuchitika kamodzi pamlungu kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Kuchokera nthawi imeneyo, sukuluyi yapereka maphunziro a m’Baibulo kuwonjezera pa malangizo amene makolo amapemphedwa kupereka kwa ana awo.—Miyambo 22:6.

Simon wa ku Switzerland, anayamba kuwerenga Baibulo mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu November 2005, ali ndi zaka 6. Chaka chotsatira, anafunsidwa mafunso pamsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova. Kodi amaona bwanji zinthu zauzimu?

Simon amakonda misonkhano yachikhristu. Zili choncho chifukwa chakuti amayesetsa kusaphonya msonkhano uliwonse, ngakhale ngati atatopa. Ndiponso, amapita kukalalikira ndi abale ake. Mwezi uliwonse, amagawira magazini mwina 30 kapena mpaka 50 a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anthu amisinkhu yonse. Komanso, amauza bambo ake za m’Baibulo ndi kuwalimbikitsa kupita nawo kumisonkhano.

Zoonadi, makolo amene amalera ana awo “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake” amasangalala kwambiri anawo akamalabadira ndi kubala chipatso chachilungamo.—Aefeso 6:4; Yakobe 3:17, 18.

[Chithunzi patsamba 28]

Dorian ali ku sukulu

[Chithunzi patsamba 28]

Simon ali ku Nyumba ya Ufumu