Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Masiku ano nyumba zambiri ku America zili ndi ma TV ambiri kuposa anthu. Theka la nyumba za ku America zili ndi ma TV atatu kapena kupitirira.”—ASSOCIATED PRESS, U.S.A.

Ku South Africa, ana 82 tsiku lililonse amawapeza ndi mlandu “wogwirira kapena wochitira zachipongwe ana anzawo.” Malinga ndi zimene ena akunena, akuti ambiri a ana amene amapezedwa ndi mlanduwo amati amachita nkhanzazo “chifukwa chakuti ndi zimene amaonerera pa TV.”—THE STAR, SOUTH AFRICA.

Munthu Wosagona Mokwanira Sagwira Bwino Ntchito

Anthu a ku Spain ali ndi chizolowezi chosagona mokwanira, ndipo zimenezi zikusokoneza kagwiridwe kawo ka ntchito. Dr. Eduard Estivill, amene ali ndi chipatala chothandiza anthu osowa tulo ku Barcelona, akuti poyerekezera ndi anthu onse a ku Ulaya, anthu a ku Spain amadzuka msanga, amagwira ntchito nthawi yaitali, amadya chakudya cha madzulo mochedwa, ndipo amapereweza tulo tawo ndi mphindi 40. Kusagona mokwanira kumayambitsa mavuto monga kukwiyakwiya, kuiwalaiwala, kuda nkhawa, ndi kusokonezeka maganizo. Choncho, Dr. Estivill akuchenjeza kuti “aliyense amene amagwira ntchito yofuna kuganiza kwambiri, ayenera kugona maola 7 kapena 8 patsiku.”

Kodi Ndi Bwino Kuyatsa Tirigu N’kumawotha?

Nyuzipepala ya ku Germany inati, popeza mtengo wa tirigu ukutsika koma wa mafuta ukukwera, mlimi angapulumutse ndalama ngati ayatsa tirigu wake n’kumawotha m’malo mogulitsa tiriguyo kuti agule mafuta. Mlimi amawononga ndalama zokwana masenti 20 kuti alime tirigu wolemera makilogalamu awiri ndi theka. Kuyatsa tirigu wotere kungafunditse m’nyumba mofanana ndi mafuta okwana lita imodzi koma amene angagule pamtengo wa masenti 60. Chifukwa cha zimenezi, nyuzipepalayo inafunsa funso lovuta kuyankha lakuti: Kodi “ndi bwino kuwotcha tirigu pamene anthu ena akufa ndi njala”?—Zachokera m’nyuzipepara ya Frankfurter Allgemeine Sonntagszeitung.

Kuchitira Malonda Ulendo wa Papa

Papa atapita ku Germany mu 2006, mafakitale, amalonda, ndi okopa alendo anakonzekera kuti apindule ndi ulendowo. Nawonso atchalitchi anapeza munthu woti aziwagulitsira katundu wosiyanasiyana. Anali ndi katundu woti anthu akagula azikumbukira ulendowo monga korona, makandulo, madzi opatulika, makapu a khofi, zipewa, masikipa, tizitsulo tokolowekera makiyi, ndi mbendera za Vatican. Nyuzipepala ina inati: “Tchalitchi cha Katolika chili yakaliyakali ndi malonda, ngati kuti Yesu Khristu sanathamangitsepo amalonda m’kachisi.”—Zachokera m’nyuzipepara ya Der Spiegel.

Anthu Akukakala Mtima Chifukwa Choonerera Zachiwawa

Katswiri wina wa zamaganizo pa sukulu yaukachenjede ya Iowa State University, ku U.S.A. anati: “Anthu amene amaonerera zachiwawa pakompyuta kapena pa TV amakakala mtima moti siziwakhudza n’komwe akaona anthu akuchitira chiwawa anzawo pamoyo wawo.” M’mbuyomu atafufuza, anapeza kuti kuonerera zachiwawazo “kumayambitsa mtima wachidani, mkwiyo, kugunda mtima ndi kupuma mothamanga, ndiponso khalidwe lachiwawa.” Katswiri ameneyu anaunika kugunda mtima kwa anthu amene anasonyezedwa filimu ya zochitika zenizeni zachiwawa ndi mmene anachitira ataonerera zimenezo pambuyo poti aonerera zachiwawa kapena zopanda chiwawa zina. Anapeza kuti anthu “amene amaonerera zachiwawa amazolowera chiwawa chamtundu uliwonse ndipo m’kupita kwa nthawi sadabwa chilichonse akamaonerera.”