Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Athandiza Kwambiri Pazachipatala”

“Athandiza Kwambiri Pazachipatala”

“Athandiza Kwambiri Pazachipatala”

YOLEMBEDWA KU MEXICO

A Mboni za Yehova amadziwika pa dziko lonse kuti akadwala amafuna kulandira mankhwala opanda magazi. Iwo amatero chifukwa cha zimene Baibulo limanena, koma anthu ena amatsutsa zimene a Mboni amafunazo. Komabe nkhani ina imene inalembedwa m’nyuzipepala ya Reforma ya ku Mexico City, yomwe ndi yotchuka kwambiri, inati mkulu wa madokotala ochita opaleshoni pachipatala chotchedwa National Institute of Oncology, dzina lake Dr. Ángel Herrera, anati: “Si kuti a Mboni ndi anthu opusa, kapenanso kuti amangotengeka maganizo. . . . [Iwo] athandiza kwambiri pazachipatala mwa kuchititsa ogwira ntchito zachipatala kuganizira za ubwino wopewa kutaya magazi.”

Zaka 15 zapitazo, Dr. Herrera anapanga gulu la madokotala ndi akatswiri ogonetsa anthu kuti azichita maopaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Dr. Isidro Martínez, katswiri wogonetsa anthu yemwe anali nawo m’gululo, anati: “N’zotheka kugonetsa munthu m’njira yabwino kwambiri pamenenso mukugwiritsa ntchito njira zonse zoletsa magazi kutayika. Choncho tingalemekeze maganizo achipembedzo a Mboni za Yehova ndiponso tikhoza kuwathandiza pamene adwala.”

Nyuzipepala ya Reforma mu October 2006 inati pali njira zina zoposa 30 zimene zingagwiritsidwe ntchito m’malo mwa magazi. Zina mwa njira zimenezi ndi kutseka mitsempha ya magazi, kukuta ziwalo ndi tinsalu tapadera tokhala ndi mankhwala oletsa kutaya magazi, ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala ochulukitsa magazi. *

Dr. Moisés Calderón, yemwe ndi mkulu wa madokotala ochita opaleshoni ya mtima pachipatala chachikulu cha La Raza ku Mexico City, amachita maopaleshoni popanda kuika magazi. Iye ananena mu nyuzipepala ya Reforma kuti: “Kuika munthu magazi kuli ndi mavuto ake. N’zotheka kupatsira munthuyo tizilombo toyambitsa matenda. Ndiponso, nthawi zina thupi la munthu silingagwirizane ndi magaziwo moti impso ndi mapapu zingasiye kugwira bwino ntchito.” Chifukwa cha mavutowa, Dr. Calderón anati: “Odwala onse timawachita opaleshoni ngati kuti ndi a Mboni za Yehova. Timayesetsa kuti munthuyo asataye magazi ambiri, timabwezeretsanso m’thupi lake magazi amene akutayika, ndiponso timagwiritsa ntchito mankhwala amene amathandiza kuti magazi asatuluke ambiri.”

Nyuzipepalayo inagwira mawu lemba la Machitidwe 15:28, 29, lomwe ndi lemba limene a Mboni za Yehova amaligwiritsa ntchito kwambiri pankhaniyi. Palembali, atumwi anagamula kuti: “Mzimu woyera pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakuwonjezereni mtolo wina, kupatulapo zinthu zofunika zokhazi, kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano, magazi, zopotola, ndi dama.”

Dipatimenti Yopereka Chidziwitso cha Zachipatala ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico inanena kuti, m’dzikolo muli Makomiti Olankhulana ndi Achipatala okwana 75 omwe ali ndi anthu 950, amene amadzipereka kukaonana ndi madokotala kuti awadziwitse njira zina zochiritsira popanda magazi. Madokotala pafupifupi 2,000 ku Mexico amavomereza kuthandiza Mboni za Yehova popanda kugwiritsa ntchito magazi. Mboni zimayamikira zedi thandizo la madokotala amenewa, omwe tsopano ali okonzeka kwambiri kuthandizanso anthu amene si a Mboni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Magazini ya Galamukani! silimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito njira inayake monga yabwino kuposa njira zina, munthu aliyense amafunika kudzisankhira yekha.

[Chithunzi patsamba 30]

Dr. Ángel Herrera

[Chithunzi patsamba 30]

Dr. Isidro Martínez

[Chithunzi patsamba 30]

Dr. Moisés Calderón