Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?

Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?

Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?

BAIBULO limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Komanso, iye ndi wachilungamo ndiponso wachifundo. “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”—Deuteronomo 32:4.

Popeza kuti Yehova Mulungu ndi Mlengi, iye angathe kuoneratu chinthu chilichonse chimene chingachititse mavuto, ndipo ali ndi mphamvu yoti angathe kuchitapo kanthu. Poganizira mfundo zimenezi ndiponso makhalidwe a Mulungu ofotokozedwa m’Baibulo, m’pake anthu amafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti pazichitika masoka achilengedwe?” * Anthu ambiri ofunadi kupeza yankho la funso limeneli aphunzira kuti Mulungu mwiniwakeyo anapereka yankho logwira mtima kwambiri m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Taonani zotsatirazi.

Anakana Chikondi cha Mulungu

Baibulo limatiuza kuti Mulungu anapatsa makolo athu oyambirira zinthu zonse zofunikira kuti akhale ndi moyo wosangalala ndiponso wotetezeka. Komanso, anthu onse, amene chiwerengero chawo chikanawonjezeka pomvera lamulo la Mulungu lakuti “mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi,” akanakhala ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu apitiriza kuwathandiza.—Genesis 1:28.

Koma, n’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anakana Mlengi wawo mwadala ndipo anasankha kudziimira pawokha, popanda kutsogozedwa ndi iye. (Genesis 1:28; 3:1-6) Ndiponso ana awo ambiri achita chimodzimodzi. (Genesis 6:5, 6, 11, 12) Mwachidule, tinganene kuti pafupifupi anthu onse asankha kudzilamulira ndiponso kuyang’anira dzikoli popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu. Popeza kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi ndipo amapereka ufulu wosankha zochita, iye sakakamiza anthu kumvera ulamuliro wake. Amatero ngakhale kuti anthuwo angathe kukumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zawozo. *

Komabe sikuti Yehova wangosiyiratu anthu. Mpaka pano, iye “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mateyo 5:45) Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anapatsa anthu luso lophunzira bwino za dzikoli, ndipo maphunziro amenewa amatha kuthandiza anthu kudziwiratu kuti kudzakhala nyengo yoipa ndiponso masoka ena, monga kuphulika kwa mapiri.

Anthu akudziwanso madera amene zivomezi ndi masoka ena achilengedwe amachitika kawirikawiri. M’mayiko ena, zimenezi zathandiza kuti anthu apulumuke chifukwa chophunzitsidwa bwino za masokawo ndiponso kumanga nyumba zotetezeka komanso kukhala ndi zinthu zowachenjeza tsoka likayandikira. Komabe, malipoti amasonyeza kuti masoka achilengedwe akuwonjezeka chaka ndi chaka. Zimenezi zikuchitika pa zifukwa zambiri ndiponso zovuta kumvetsa.

Kukhala M’madera Oopsa Kwambiri

Nthawi zina mphamvu ya tsoka lachilengedwe si imene imachititsa kuti tsokalo likhale losakaza kwambiri. Tsoka limakhala losakaza kwambiri malinga ndi kuchuluka kwa anthu okhala m’deralo. Malinga ndi zimene a banki lalikulu la padziko lonse anapeza, m’mayiko oposa 160, anthu oposa 25 pa 100 alionse amakhala ku madera amene anthu ambiri angathe kufa chifukwa cha masoka achilengedwe. Katswiri wina wa sayansi ku yunivesite ya Columbia, m’dziko la United States, dzina lake Klaus Jacob, anati: “Zinthu zina zimene zimachitika mwachilengedwe zimakhala masoka ngati anthu ambiri akukhala m’madera amene zinthuzo zimachitika kawirikawiri.”

Zinthu zikuipiraipira chifukwa chakuti mizinda ina ikukula mopanda dongosolo labwino, anthu akudula mitengo mwachisawawa, ndipo m’malo ambiri muli konkire yokhayokha moti madzi a mvula salowa m’nthaka. Makamaka, zifukwa ziwiri zomalizirazi zikuchititsa kuti kuzikhala masoka a matope okokolola zinthu ndiponso madzi osefukira.

Zochita za anthu nazonso zimachititsa kuti zivomezi zikhale zoopsa kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti kawirikawiri kugwa kwa nyumba n’kumene kumapha ndi kuvulaza anthu osati mphamvu imene ikugwedeza dziko. Choncho akatswiri oona za zivomezi amanena kuti: “Zivomezi sizipha anthu koma nyumba ndi zimene zimapha anthu.”

Kulephera kwa maboma kungachititsenso kuti anthu ambiri afe. M’dziko lina ku South America zivomezi zakhala zikusakaza likulu la dzikolo katatu konse m’zaka 400 zapitazi. Ndipo chichitikireni chivomezi chomaliza mu 1967, chiwerengero cha anthu chawonjezeka kufika pa miliyoni asanu. Magazini ya New Scientist inati: “M’dzikoli mulibe malamulo a kamangidwe kabwino ka nyumba ndipo ngati alipo amanyalanyazidwa.”

Mfundo yomalizirayi ikufotokoza bwino kwambiri za mzinda wa New Orleans, ku Louisiana m’dziko la United States. Mzindawu uli m’dera lotsika kwambiri limene madzi angasefukire mosavuta. Ngakhale kuti kuli mizere yotchinga madzi kuti asasefukire ndiponso makina ochotsa madzi m’deralo, tsoka limene anthu ambiri ankaliopa linachitika. Mu 2005, mzindawu unawonongedwa ndi mphepo yamkuntho yotchedwa Katrina. Ponena za tsokali nyuzipepala ya USA Today inanena kuti, anthu sanasamale n’komwe “zizindikiro zake zimene zinakhalapo kwanthawi yaitali” kapena “anangochita zinthu mosaikirapo mtima.”

N’chimodzimodzinso ndi nkhani ya kutentha kwa dzikoli, kumene akatswiri a sayansi akunena kuti kungachititse kusefukira kwa nyanja zikuluzikulu ndiponso masoka ena achilengedwe. Anthu akuchitanso zinthu mosaikirapo mtima kwenikweni. Choncho ndi bwino kuganizira zinthu zokhudza maboma, chuma, ndi zochita za anthu, zomwe si Mulungu amene amachititsa. Zochitika zonsezi zikutikumbutsa choonadi cha m’Baibulo chakuti munthu sangathe “kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Vuto linanso lagona pa zimene anthu amachita akaona zizindikiro zachilengedwe kapena akachenjezedwa ndi akuluakulu a boma za tsoka linalake.

Phunzirani Kumvera Machenjezo

N’zoona kuti masoka achilengedwe amachitika mwadzidzidzi. Lemba la Mlaliki 9:11 limati: “Yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” Ngakhale zili choncho, kawirikawiri tsoka lisanachitike pamakhala zizindikiro zachilengedwe kapena machenjezo a akuluakulu a boma. Motero, anthu akadziwa zizindikiro angathe kupulumuka tsokalo.

Pamene mafunde osakaza otchedwa tsunami anawononga zinthu pa chilumba cha Simeulue, ku Indonesia, m’chaka cha 2004, anthu 7 anafa pamene anthu zikwizikwi anapulumuka. Iwo anadziwa kuti mafunde akasiya mosayembekezeka, pamabwera mafunde osakaza, choncho anthu ambiri anathawa ataona zimenezi. Anthu enanso apulumuka mkuntho ndi kuphulika kwa mapiri chifukwa chomvera machenjezo. Popeza kuti nthawi zina zizindikiro zachilengedwe zimayamba machenjezo ochokera ku boma asanabwere, ndi bwino kudziwa zonsezi, makamaka ngati tikukhala m’madera oopsa.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti “anthu ali ndi chizolowezi chokana kuvomereza kuti kuchitika tsoka ngakhale pamene zikuonekeratu kuti tsokalo lichitika,” anatero katswiri wina woona za kuphulika kwa mapiri. Kawirikawiri zimenezi zimachitika m’madera amene kwakhala machenjezo a zinthu zimene pambuyo pake sizinachitike kapena kumene tsoka lachilengedwe latenga nthawi yaitali lisanachitike. Ndipo nthawi zina anthu safuna kusiya katundu wawo ngakhale zizindikiro za tsoka linalake zikuchita kuonekeratu.

M’madera ambiri anthu ndi osauka kwambiri moti sangathe kusamukira ku madera otetezeka. Komatu sitingaimbe mlandu Mlengi wathu chifukwa cha umphawi ayi, popeza kuti limenelo ndi vuto lochititsidwa ndi anthu. Mwachitsanzo, nthawi zambiri maboma amagwiritsira ntchito ndalama zambiri kugulira zida zankhondo koma amachita zinthu zochepa kwambiri pothandiza anthu osauka.

Ngakhale zili choncho, anthu ambiri akupeza chithandizo china, mosaganizira mmene zinthu zilili pamoyo wawo. Motani? Mulungu, kudzera m’Mawu ake Baibulo Lopatulika, watipatsa mfundo zabwino zambiri zimene zingapulumutse anthu ngati atazigwiritsira ntchito.

Mfundo Zimene Zingapulumutse Moyo

Osayesa Mulungu. Lemba la Deuteronomo 6:16 limati: “Musamayesa Yehova Mulungu wanu.” Akhristu oona saika dala moyo wawo pachiswe, n’kumaganiza kuti Mulungu aziwateteza nthawi zonse. Choncho, ngati zikuoneka kuti tsoka lichitika, iwo amamvera chenjezo louziridwa lakuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3.

Tiziona kuti moyo n’ngofunika kuposa katundu. “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) N’zoona kuti chuma chimathandiza, koma sichingam’thandize munthu atafa. Choncho, amene amakonda moyo ndipo amayamikira mwayi wawo wotumikira Mulungu, saika dala moyo pachiswe n’cholinga choti apulumutse katundu.—Salmo 115:17.

Mu 2004, Tadashi amene amakhala ku Japan, anathawa m’nyumba yake kutangochitika chivomezi. Iye anachita izi akuluakulu a boma asanapereke n’komwe malangizo. Kwa iye, moyo wake unali wofunika kwambiri kuposa nyumba ndi katundu. Akira, amene amakhalanso m’dera lomwelo, analemba kuti, “vuto lenileni silikhala pa kuwonongeka kwa katundu, koma mmene munthu akuonera zinthu. Ndinaona kuti tsoka limeneli landipatsa mwayi wokhala ndi moyo wosalira zambiri.”

Tizimvera machenjezo ochokera ku boma. ‘Mverani olamulira aakulu.’ (Aroma 13:1) Ndi bwino kumvera akuluakulu a boma akalamula kuti tisamuke m’dera linalake kapena kuti tichite zinthu zinazake kuti tidziteteze. Tadashi anathawa m’dera lomwe munachitika tsoka lija pomvera lamulo lakuti asamuke ndipo atatero anapewa kuvulala kapena kufa chifukwa cha kugunda komwe kunachitika pambuyo pa chivomezi chija.

Ngati akuluakulu a boma sakupereka chenjezo lililonse lokhudza tsoka limene lichitike, anthu amafunika kuona okha zochita, malinga ndi zimene akudziwa. M’madera ena, akuluakulu a boma m’deralo amatha kupereka malangizo othandiza kupulumuka tsoka. Ngati m’dera lanu malangizo oterowo alipo, kodi inu mukuwadziwa bwino? Ndipo kodi mwakambirana malangizowo ndi banja lanu? (Onani bokosi limene lili m’nkhani ino.) M’madera ambiri padziko lonse, mipingo ya Mboni ili ndi dongosolo limene abale ndi alongo angatsatire ngati kutachitika tsoka. Dongosolo limeneli limatsogoleredwa ndi ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dzikolo, ndipo kulitsatira kwakhala kothandiza kwambiri.

Sonyezani chikondi chachikhristu. Yesu anati: ‘Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake, mmene ine ndakukonderani.’ (Yohane 13:34) Anthu amene amasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena, monga mmene Khristu anachitira, amachita chilichonse chimene angathe pothandiza kukonzekera kapena kupulumuka tsoka lachilengedwe. M’mipingo ya Mboni za Yehova, akulu amachita khama kufufuza abale ndi alongo onse a mumpingo wawo pofuna kutsimikizira kuti ali bwino kapena kuona ngati angakwanitse kupita ku malo otetezeka. Komanso, akulu amaonetsetsa kuti aliyense ali ndi zinthu zofunikira pamoyo, monga madzi akumwa abwino, chakudya, zovala, ndiponso mankhwala. Panthawi ya tsoka, Mboni za m’madera otetezeka zimasunga abale awo ochokera m’madera omwe kwachitika tsokalo. Zoonadi, chikondi choterechi “ndicho chomangira umodzi changwiro.”—Akolose 3:14.

Kodi masoka achilengedwe adzafika poipa kwambiri ngati mmene anthu ena akunenera? Mwina zingatero, komatu osati kwanthawi yaitali. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti nthawi yoti anthu azichita zinthu popanda kudalira Mulungu yatsala pang’ono kutha. Nthawiyi ikadzatha, dziko lonse lapansi ndiponso anthu adzakhala mu ulamuliro wabwino kwambiri wa Yehova, ndipo zotsatirapo zake zidzakhala zosangalatsa kwambiri, monga momwe tionere m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zivomezi, nyengo yoipa kwambiri, kuphulika kwa mapiri ndiponso zochitika zina, sizikhala tsoka mwa izo zokha. Zimakhala tsoka pokhapokha zikasokoneza kapena kupha anthu ndiponso kuwononga katundu.

^ ndime 6 Zifukwa zimene Mulungu walolera mavuto kuchitika kwakanthawi chabe, zafotokozedwa mwatsatanetsatane mu Galamukani! ya November 2006 pa mutu wakuti, “Kuyankha Funso Lovuta Kwambiri Loti ‘Chifukwa Chiyani?’” komanso mutu 11 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

KODI NDINU WOKONZEKA KUTHAWA?

Ofesi yoona za zinthu zogwa mwadzidzidzi mu mzinda wa New York City, ku United States imati ndi bwino kuti mabanja azikhala okonzeka kusamuka pakachitika zamwadzidzidzi. Ofesiyi imati angatero mwa kukhala ndi chikwama chaching’ono, cholimba, chosavuta kunyamula, pamalo osavuta kuchipeza. M’chikwamachi ayenera kulongedzamo zinthu zofunikira kwambiri panthawi ya ngozi, monga: *

▪ Mafotokope a zikalata zofunika kwambiri oikidwa m’pulasitiki

▪ Makiyi ena a galimoto ndiponso a nyumba

▪ Khadi logulira zinthu pangongole kapena khadi la kubanki, ndiponso ndalama

▪ Botolo la madzi akumwa ndi zakudya zosawonongeka msanga

▪ Tochi, kawailesi, foni ya m’manja (ngati muli nayo), mabatire

▪ Mankhwala omwe mungagwiritsire ntchito kwa mlungu umodzi, malangizo a kamwedwe kake, mabuku a kuchipatala, mayina ndi manambala a foni za madokotala. (Muzionetsetsa kuti mukusintha mankhwalawo tsiku lake lotha mphamvu lisanakwane)

▪ Zinthu zothandizira munthu akavulala kapena kudwala mwadzidzidzi

▪ Nsapato zolimba zimene munthu angayende nazo mtunda wautali, ndiponso zovala zoteteza ku mvula

▪ Pepala la manambala a foni a anthu a m’banja mwanu, malo amene mungakumane nawo, ndiponso mapu adera lanu

▪ Zinthu zogwiritsira ntchito posamalira mwana

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 35 Pa zinthu zimene ofesiyi inatchula tasinthako pang’ono zina ndi zina. Malinga ndi dera limene mukukhala, mwina simungafunike kutenga zinthu zonse zimene zalembedwazi, ndipo mwinanso mungawonjezerepo zina. Mwachitsanzo, anthu achikulire ndi olumala ali ndi zinthu zawo zimene amafunikira.

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

USGS, David A. Johnston, Cascades Volcano Observatory