Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?

Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?

“Makolo anga ndi a ku Italy, ndipo sachita manyazi kusonyeza chikondi pagulu. Koma tsopano timakhala ku Britain. Anthu a kuno amaoneka kuti n’ngaulemu kwambiri. Sindikhala womasuka pakati pa anthu a zikhalidwe ziwiri zonsezi. Ndimaona kuti sindine Mngelezi weniweni komanso sindine Mtaliyana weniweni.”—Anatero Giosuè, ku England.

“Kusukulu aphunzitsi anandiuza kuti ndikamalankhula nawo ndiziwayang’ana kumaso. Koma bambo anga ankandiuza kuti ndi mwano kumawayang’ana kumaso polankhula nawo. Motero sindinadziwe kuti nditsatire chikhalidwe chiti.”—Anatero Patrick, yemwe akukhala ku France koma kwawo ndi ku Algeria.

Kodi mayi anu kapena bambo anu ndi ochokera kunja?

□ Inde □ Ayi

Kodi chilankhulo kapena chikhalidwe cha anthu a kusukulu kwanu n’chosiyana ndi cha kunyumba kwanu?

□ Inde □ Ayi

CHAKA chilichonse pali anthu ochuluka kwambiri amene amasamukira kunja ndipo ambiri amakakumana ndi mavuto aakulu. Amangozindikira kuti ali pakati pa anthu a chilankhulo china, chikhalidwe china ndiponso ovala zovala zosiyana. Motero, nthawi zambiri anthu ochokera kunja amasekedwa. Zimenezi n’zimene mtsikana wina dzina lake Noor anakumana nazo. Banja lawo lonse linasamukira ku North America kuchokera ku Jordan. Iye anati: “Anthu ankatiseka chifukwa cha zovala zathu. Koma zinthu zambiri zimene anthu a kuno ku America amaona kuti n’zoseketsa, ifeyo sitinkamvetsa kuti n’zoseketsa chifukwa chiyani.”

Mtsikana wina dzina lake Nadia anakumana ndi vuto linanso. Iye anati: “Ine ndinabadwira ku Germany. Koma popeza kuti makolo anga ndi a ku Italy, ndinkalankhula Chijeremani cha Chitaliyana, motero kusukulu anzanga ankandinena kuti ndine kape wakunja. Koma ndikapita ku Italy, anthu amati ndimalankhula Chitaliyana cha Chijeremani. Choncho ndimaona kuti ndilibe kwathu kwenikweni, chifukwa kulikonse kumene ndingapite ndimaonedwa ngati wakunja.”

Kodi ana amene makolo awo ali ochokera kunja amakumana ndi mavuto enanso otani? Ndipo kodi angatani kuti zinthu ziwayendere bwino?

Kusamvetsetsana Chifukwa cha Chikhalidwe Ndiponso Chilankhulo

Ana amene makolo awo ali ochokera kunja angayambe kukumana ndi vuto losiyana chikhalidwe ngakhale kunyumba. Kodi zimenezi zingachitike motani? Nthawi zambiri ana amazolowera msanga chikhalidwe china kusiyana ndi makolo awo. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Ana, anasamukira ku England pamodzi ndi makolo ake ndi azibale ake. Panthawiyi n’kuti iyeyu ali ndi zaka 8. Iye anati: “Ineyo ndi mchimwene wanga sitinavutike n’komwe kutengera chikhalidwe ndi chilankhulo cha ku London. Koma makolo anga zinkawavuta kwambiri, chifukwa anakhala zaka zambiri pa kachilumba ka Apwitikizi kotchedwa Madeira.” Mtsikana wina dzina lake Voeun anali ndi zaka zitatu pamene makolo ake anasamuka ku Cambodia n’kupita ku Australia. Iye anati: “Makolo anga zikuwavuta kwambiri kuzolowera chikhalidwe cha kuno. Moti nthawi zambiri bambo ankandilusira kwambiri chifukwa choti sindinkamvetsa kaganizidwe kawo.”

Kusiyana chikhalidwe kumeneku kuli ngati mtsinje waukulu wolekanitsa ana ndi makolo awo. Ndipo kusiyana kwa chilankhulo kumawonjezera kwambiri vuto limeneli. Vutoli limayamba ana akaphunzira mwachangu chilankhulo china kuposa makolo awo. Ndiyeno limakulirakulira anawo akayamba kuiwala chilankhulo cha makolo awo n’kumalephera kumvana nawo bwinobwino.

Ian, amene tsopano ali ndi zaka 14, anakumana ndi vuto limeneli pamene banja lawo linasamuka ku Ecuador n’kupita ku New York. Iye anati: “Panopo ndimalankhula bwino Chingelezi kuposa Chisipanishi. Aphunzitsi athu kusukulu amalankhula Chingelezi, anzanga amalankhula Chingelezi ndipo inenso ndimalankhula Chingelezi ndi mng’ono wanga. Motero, Chingelezi n’chimene chikutenga malo kwambiri m’mutu mwanga kuposa Chisipanishi.”

Kodi zimene anafotokoza Ian n’zimenenso zikukuchitikirani? Ngati banja lanu linasamukira kwina inuyo mudakali aang’ono, n’kutheka kuti simunkadziwa kuti chilankhulo cha makolo anu chingakupindulitseni patsogolo. Motero mwina munachiiwala chifukwa chosaikirapo mtima. Noor, amene tam’tchula kale uja, anati: “Bambo anga anayesetsa kulimbikira kwambiri zoti tizilankhula chinenero chawo cha Chiarabu kunyumba, koma ifeyo sitinkafuna. Tinkaona kuti kuphunzira Chiarabu n’kungodzivutitsa chabe. Anzathu onse ankalankhula Chingelezi, komanso mapulogalamu onse amene tinkaonera pa TV anali m’Chingelezi. Choncho sitinkaona chifukwa chophunzirira Chiarabu.”

Koma mukamakula mungaone kuti kulankhula bwino chilankhulo cha makolo anu kuli ndi ubwino wake. Komabe, n’kutheka kuti mungamachite kuganizira mawu ena amene kale simunkavutika nawo n’komwe. Michael ali ndi zaka 13, ndipo iye ndi makolo ake anasamuka ku China n’kupita ku England. Iye anati: “Nthawi zina ndimasakaniza zilankhulo ziwirizi.” Mtsikana wina wa zaka 15, dzina lake Ornelle, anasamuka ku Congo (Kinshasa) n’kupita ku London, ndipo anati: “Nthawi zina ndimafuna kuuza mayi anga zinazake m’Chilingala, koma ndimalephera chifukwa choti Chingelezi chinandilowerera kwambiri.” Mtsikana wina dzina lake Lee, yemwe anabadwira ku Australia koma makolo ake n’ngochokera ku Cambodia, amadandaula kuti sadziwa bwino kulankhula chinenero cha makolo ake. Iye anati: “Ndimangodzikolakola ndikafuna kufotokoza bwinobwino zinazake kwa makolo anga, kapena ndikafuna kuwalongosolera maganizo anga pankhani inayake m’chilankhulo chawo.”

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuthetsa Vutoli?

Ngati mwayamba kuiwala chilankhulo cha makolo anu, musadandaule kwambiri. N’zotheka kuyambiranso kuchilankhula bwinobwino. Koma choyamba muyenera kumvetsetsa ubwino wodziwa chilankhulo cha makolo anu. Kodi kudziwa bwino chilankhulocho kungakuthandizeni m’njira zotani? Giosuè, yemwe tam’tchula kale uja anati: “Ndinaphunzira chilankhulo cha makolo anga pofuna kuti tizimvana bwinobwino ndiponso kuti tizilambira Mulungu mogwirizana kwambiri. Zimenezi zandithandiza kuti ndiziwamvetsa ndipo nawonso zawathandiza kuti azindimvetsa.”

Achinyamata ambiri achikhristu akuphunzira chilankhulo cha makolo awo chifukwa chofuna kuuza anthu achilankhulocho uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Salomão, yemwe wakhala ku London kuyambira ali ndi zaka zisanu, anati: “N’zosangalatsa kwambiri kutha kufotokoza Malemba m’zilankhulo ziwiri. Ndinatsala pang’ono kuiwaliratu Chipwitikizi, chomwe n’chilankhulo cha makolo anga. Koma chifukwa choti panopo ndinayamba kupita ku mpingo wa Chipwitikizi, ndimatha kulankhula bwinobwino Chingelezi ndi Chipwitikizi chomwe.” Oleg, yemwe ali ndi zaka 15, ndipo akukhala ku France, anati: “Ndimasangalala kwambiri kuthandiza ena. Ndimatha kulalikira kwa anthu olankhula Chirasha, Chifalansa, kapenanso Chimodova.” Noor anaona kuti gawo la Chiarabu likufunikira alaliki ambiri a uthenga wabwino. Iye anati: “Panopa ndinayamba kuphunziranso chilankhulochi ndipo ndikuyesetsa kukumbukira zina ndi zina zimene ndinaziiwala. Poyamba sindinkafuna kulankhula chinenerochi. Koma panopo ndimachita kuwauza anthu kuti azindiuza zimene ndikulakwitsa chifukwa ndikufuna kuchidziwa bwinobwino chilankhulochi.”

Kodi mungatani kuti muyambenso kulankhula bwino chilankhulo cha makolo anu? Mabanja ena aona kuti kunyumba, akamalankhula chilankhulo chawo chokhacho basi, ana awo amaphunzira bwinobwino zilankhulo ziwiri zonsezo. * Ndi bwinonso kupempha makolo anu kuti akuphunzitseni kulemba chilankhulocho. Stelios, yemwe anakulira ku Germany koma chilankhulo cha makolo ake ndi Chigiriki, anati: “Makolo anga ankakambirana nane lemba la m’Baibulo tsiku lililonse. Ankawerenga lembalo mokweza ndipo ine ndinkalilemba. Moti panopo ndimatha kuwerenga ndi kulemba Chigiriki ndi Chijeremani chomwe.”

Inde, kudziwa bwino zikhalidwe ndiponso zilankhulo ziwiri kapena zingapo kungakuthandizeni kwambiri. Mumatha kumvetsa bwino anthu ndi kuyankha mafunso awo okhudza Mulungu. Baibulo limati: “Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m’kamwa mwake; ndi mawu a pa nthawi yake kodi sali abwino?” (Miyambo 15:23) Mtsikana wina dzina lake Preeti, yemwe anabadwira ku England koma makolo ake ndi a ku India, anati: “Sindivutika mu utumiki chifukwa ndimadziwa bwino zikhalidwe ziwiri ndipo ndimamvetsa bwino anthu a zikhalidwe ziwiri zonsezi. Ndimamvetsa zimene amakhulupirira ndiponso maganizo awo.”

“Mulungu Alibe Tsankho”

Ngati zikukuvutani kudziwa kuti mutsatire chikhalidwe chiti musataye mtima. Anthu angapo m’Baibulo anakumananso ndi vuto ngati limeneli. Mwachitsanzo, Yosefe anatengedwa kwawo n’kupita naye kudziko la chikhalidwe china ku Iguputo, komwe anakhalako moyo wake wonse. Koma zikuoneka kuti sanaiwale chilankhulo cha makolo ake. (Genesis 45:1-4) Chifukwa cha zimenezi, patsogolo pake anatha kuthandiza abale ake.—Genesis 39:1; 45:5.

Timoteyo, amene anayenda kwambiri ndi mtumwi Paulo, bambo ake anali Mgiriki ndipo mayi ake anali Myuda. (Machitidwe 16:1-3) Ngakhale kuti anali ndi makolo osiyana zikhalidwe, iye sanalole kuti zimenezi zimulepheretse kuchita zinthu zina. Pantchito yake ya umishonale, iye anathandiza anthu ena mosavuta chifukwa cha zimenezi.—Afilipi 2:19-22.

Ngati inunso mukukumana ndi zoterezi, kodi mungazione ngati mwayi wanu m’malo modandaula nazo? Kumbukirani kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Yehova amakukondani kwambiri chifukwa cha umunthu wanu, osati chifukwa cha kumene mumachokera. Kodi nanunso mungachite zimene achinyamata amene atchulidwa m’nkhani ino anachita? Kodi mungagwiritse ntchito chikhalidwe ndiponso chilankhulo cha makolo anu pothandiza anthu a mtundu wanu kuphunzira za Mulungu wathu Yehova? Mutatero, mungathe kukhaladi wosangalala kwambiri, chifukwa Yehova ndi Mulungu wopanda tsankho ndiponso wachikondi.—Machitidwe 20:35.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Malangizo ena othandiza mungawapeze mu nkhani yakuti “Kulera Ana M’dziko Lachilendo—Mavuto ndi Mphoto Zake,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2002.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mukukumana ndi mavuto otani okhudza chikhalidwe kapena chilankhulo?

▪ Kodi ena mwa mavuto amenewa mungathane nawo bwanji?

[Chithunzi patsamba 20]

Kulankhula chinenero cha makolo anu kungathandize kuti muzigwirizana kwambiri m’banja mwanu