Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Matenda Onse Adzatha! (January 2007) Pamene munanena kuti anthu ena “amawononga ndalama ndiponso nthawi pofunafuna thandizo la mankhwala osathandiza, kapena oopsa kumene,” zikuoneka kuti munali kunena za mankhwala ena omwe si a kuchipatala. Ndikutero chifukwa chakuti nkhani yanu inakayikira ubwino wa njira zina zamankhwala zochiritsira. Kodi ndiye kuti Galamukani! ikunena kuti mankhwala a kuchipatala ndi amene ali abwino ndi othandiza kwambiri? Bungwe la ku America loyang’anira chuma cha boma likuti, pali umboni wambiri wosonyeza kuti mankhwala a kuchipatala si othandiza kwenikweni.
G. C., United States
Yankho la “Galamukani!”: Njira zambiri za mankhwala zimene zinali zabwino panthawi ina m’mbuyomu, m’kupita kwa nthawi zapezeka kuti n’zosathandiza. Zimenezi zachitikira mitundu yonse iwiri ya mankhwala, a kuchipatala ndi omwe si a kuchipatala. Choncho, musanasankhe mankhwala, ndi bwino kufufuza kaye ubwino ndi kuipa kwake, ndipo onetsetsani kuti mankhwalawo sakutsutsana ndi mfundo za m’Baibulo. Zimenezi n’zofunika kusankha nokha. Ndipo monga mmene takhala tikunenera m’mbuyo monsemu, “Galamukani!” sisankhira munthu mankhwala oti agwiritse ntchito. Ndipotu Akhristu amapewa kuweruza ena kapena kutsutsa mankhwala amene anthu ena akugwiritsa ntchito. Monga mmene nkhani zathu zinasonyezera, mfundo ndi yoti palibe mankhwala, kaya akhale a ku chipatala kapena ayi, amene angathetseretu matenda. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetseratu matenda.—Chivumbulutso 21:3, 4.
‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’ (August 2006) Kupirira ndi kudzichepetsa kwa Francesco Abbatemarco, kunandichititsa kuganiza mozama. Kuti atumikire Yehova, analimbana ndi vuto lake la kulumala ndiponso maganizo odziona ngati munthu wolephera. Nkhani yake yandithandiza kumvetsa kuti tingathe kutumikira Yehova ndi mphamvu zathu zonse ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu chotani. Ndinalimbikitsidwanso kuona kuti kutsatira Mawu a Mulungu, kunamuthandiza kusintha kwambiri moyo wake.
N. G., Cambodia
Francesco anali ndi mavuto ambiri oti alimbane nawo. Koma kuphunzira choonadi kunamupatsa mphamvu zolimbana ndi mavuto akewo. Anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri cha kulimba mtima. Ndikukhulupirira kuti nkhani yake ilimbikitsa anthu ambiri monga mmene yandilimbikitsira ineyo.
M. D., South Africa
Nkhaniyi inandisangalatsa kwambiri. Ndikulakalaka nditakumana naye Francesco Abbatemarco kuti ndimuuze mmene nkhani yake yandilimbikitsira kuchita nkhama kwambiri potumikira Yehova.
J. B., United States
Zikomo kwambiri Francesco chifukwa cha chitsanzo chanu chabwino kwambiri chopirira mavuto ndi kutumikira Yehova mwakhama. Ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti m’dziko latsopano, mudzadumpha ngati nswala. Dziwani kuti muli ndi abale ndi alongo amene amakukondani ndi kukupemphererani kwambiri.
S. G., Russia