Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Masoka Atha Posachedwapa

Masoka Atha Posachedwapa

Masoka Atha Posachedwapa

YESU ananeneratu kuti zivomezi, nkhondo, njala, ndiponso matenda ndi zina mwa zinthu zosonyeza “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 24:3, 7, 8; Luka 21:7, 10, 11) N’zodziwikiratu kuti si Yesu kapenanso Atate wake, Yehova Mulungu, amene akuchititsa zinthu zimenezi.

Koma Mulungu ndiye adzabweretse Ufumu umene zinthu zimene zikuchitikazi zikusonyeza kuti wayandikira. Ufumu umenewu ndi boma lakumwamba lolamulidwa ndi Yesu Khristu ndipo udzawononga anthu onse amene amatsutsa ulamuliro wa Yehova. (Danieli 2:44; 7:13, 14) Kenako, dziko lapansi lidzakhala malo amtendere, omwe sikudzakhalanso kuopa masoka achilengedwe. Malonjezo a Mulungu akuti, “anthu anga adzakhala m’malo amtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe,” adzakwaniritsidwadi.—Yesaya 32:18.

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha

Monga mmene nkhani yapitayi yafotokozera, kumvera machenjezo kungapulumutse moyo. Machenjezo a Mulungu opezeka m’Baibulo ndiye ofunika kuwamvera kwambiri. Mulungu akulonjeza kuti: “Wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Miyambo 1:33.

Mboni za Yehova zimayesetsa kumvera Mulungu mwa kuwerenga Mawu ake ouziridwa nthawi zonse ndi kugwiritsira ntchito zimene mawuwo amanena. Ndipo inu mukupemphedwa kuti muzichitanso chimodzimodzi. N’zoonadi, anthu amene amamvera Yehova sayenera kuopa za m’tsogolo ndiponso tsoka limene lidzagwere anthu oipa. M’malo mwake, iwo n’ngosangalala kuyembekezera moyo wosatha m’dziko lapansi la Paradaiso, mmene ‘adzakondwere nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:10, 11.

[Bokosi patsamba 8]

KULIMBIKITSA ANTHU AMENE AKULIRA

Kodi pali munthu wina amene munali kum’konda yemwe anamwalira, mwinamwake chifukwa cha tsoka lachilengedwe kapena pangozi inayake? Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Lazaro, amene anali mnzake wapamtima wa Yesu, anamwalira. Yesu atamva za imfayo, anapita ku mudzi wa Lazaro, ku Betaniya, n’kukamuukitsa ku ‘tulo’ ta imfa.—Yohane 11:1-44.

Pochita chozizwitsachi, Yesu anasonyeza kuti ankakonda Lazaro ndiponso banja lake. Komanso, anatsimikizira lonjezo lake lakuti adzaukitsa “onse ali m’manda a chikumbutso” pamene akulamulira mu Ufumu wake. (Yohane 5:28, 29) Zoonadi, m’Paradaiso m’tsogolo muno, Yesu adzathetsa mavuto onse amene anayamba chifukwa cha kupanduka komwe kunachitika mu Edeni. *1 Yohane 3:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mungapeze malangizo a m’Malemba okuthandizani kupirira ndi kuthana ndi mavuto amene amadza chifukwa cha imfa ya munthu amene munali kum’konda, komanso nkhani zatsatanetsatane zokhudza lonjezo la kuuka kwa akufa m’kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

CHIVOMEZI CHINANDISINTHITSA ZOLINGA ZANGA

Mu 1971, ndinali mayi wachitsikana ndiponso ndinali ndi chidwi chodzakhala woimba. Mu 1957, ndinasamuka mu mzinda womwe ndinabadwira wa Winnipeg, ku Manitoba, m’dziko la Canada, n’kukakhala kufupi ndi Hollywood, ku California, m’dziko la United States. Ndinachita izi n’cholinga choti ndikakwaniritse chikhumbo changa chodzakhala woimba.

Kwa zaka 9, amayi anga, omwe anali a Mboni za Yehova, ankabwera m’nyengo ya chilimwe kuchokera ku Canada kudzandichezera. Pamaulendo oterowo ankakonda kundifotokozera za m’Baibulo, ndipo ankakhulupirira kuti linali ndi malangizo abwino kwambiri onena za mmene tingakhalire achimwemwe ndiponso onena za moyo wa banja. Ndinkawakonda kwambiri amayi ndipo ndinkawamvetsera mwaulemu. Koma akangochoka, ndinkataya mabuku amene anandipatsa, pokhulupirira kuti tsogolo langa lili bwino.

M’mawa wina, tsiku Lachiwiri mu February 1971, kunachitika chivomezi champhamvu chimene chinandidzutsa kutulo. Kunali phokoso logonthetsa m’makutu ndipo dziko linagwedezeka kwambiri. Mwamantha, ndinathamanga kuti ndikaone mwana wanga ndipo mtima wanga unakhala m’malo nditamuona kuti ali bwinobwino m’bedi lake. Chivomezicho chitasiya, zidutswa za matambula ndi zinthu zina zimene zinali m’kabati zinangoti mbwee pansi ndipo kuseli kwa nyumba yathu kunali madzi okhaokha ochokera padziwe losambiramo. Sindinagonenso ngakhale kuti tonse m’banja mwathu sitinavulale.

Amayi anali atandiuzapo za “masiku otsiriza” omwe mbali ya chizindikiro chake ndi “zivomezi zamphamvu.” (2 Timoteyo 3:1; Luka 21:7-11) M’chilimwe cha chaka chimenechi amayi anabweranso koma sanatenge mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Iwo anali atataya nane mtima chifukwa anali atandilalikira kwa zaka 9 koma popanda chilichonse chochitikapo. Komatu zinthu zinali zitasintha. Atangofika, ndinawapanikiza ndi mafunso. Mwadzidzidzi, ndinayamba kuona kuti kuimba ndi kutchuka n’zopanda ntchito.

Mlungu womwewo ndinatsagana ndi amayi kupita ku misonkhano yachikhristu, ku Nyumba ya Ufumu. Ndipo kuyambira pamenepo sindiphonya misonkhano. Iwo anakonza zoti ndiziphunzira Baibulo. Ndinabatizidwa mu 1973 ndipo panopa ndimalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu maola pafupifupi 70 mwezi uliwonse. (Mateyo 24:14) M’malo mosokoneza chikhulupiriro changa mwa Mulungu, chivomezi chinandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro.—Yofotokozedwa ndi Colleen Esparza.